Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Kuphunzira Baibulo Kuzikusangalatsani Komanso Kuzikuthandizani?

Kodi Mungatani Kuti Kuphunzira Baibulo Kuzikusangalatsani Komanso Kuzikuthandizani?

YOSWA anapatsidwa ntchito yovuta kwambiri. Iye ankayenera kutsogolera mtundu wa Aisiraeli pa ulendo wokalowa m’Dziko Lolonjezedwa ndipo ankayembekezera kukumana ndi mavuto ambiri. Yehova anamutsimikizira kuti akwanitsa ntchitoyi ndipo anamuuza kuti: ‘Khala wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo anga. Uziwawerenga usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatira zonse zolembedwamo. Pakuti ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.’​—Yos. 1:7, 8.

Popeza tili ‘m’masiku otsiriza komanso ovuta,’ nafenso timakumana ndi mavuto ambiri. (2 Tim. 3:1) Kuti zinthu zitiyendere bwino, tiyenera kutsatira chitsanzo cha Yoswa yemwe ankatsatira malangizo amene Yehova anamupatsa. Zimenezi zingatheke tikamawerenga Baibulo nthawi zonse komanso kugwiritsa ntchito mfundo zake tikakumana ndi mayesero.

Ambirife tingavomereze kuti sitikonda kuwerenga ndipo timafunika kuchita khama kwambiri kuti tiziwerenga. Koma popeza kuwerenga Baibulo ndi kofunika kwambiri, tikukupemphani kuti muwerenge bokosi lakuti “ Yesani Izi.” M’bokosili mupezamo mfundo zimene zingachititse kuti kuwerenga Baibulo kuzikusangalatsani komanso kuzikuthandizani.

Munthu wina wolemba masalimo anati: “Ndiyendetseni m’njira ya malamulo anu, pakuti ndikukondwera ndi njira imeneyi.” (Sal. 119:35) Nanunso mukhoza kumasangalala kwambiri powerenga Mawu a Mulungu. Ndipo mukamawerenga Baibulo mwakhama mudzazindikira mfundo zothandiza kwambiri.

N’zoona kuti inuyo simunapatsidwe udindo wotsogolera mtundu wa anthu ngati mmene zinalili ndi Yoswa. Koma tingavomereze kuti aliyense amakumana ndi mavuto. Ndiye muziwerenga komanso kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti zikuthandizeni ngati mmene zinathandizira Yoswa. Mukamachita zimenezi, zidzakuyenderani bwino ndipo mudzachita zinthu mwanzeru.