Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Choonadi Chonena za Zimene Zidzachitike M’tsogolo

Choonadi Chonena za Zimene Zidzachitike M’tsogolo

Kodi munaganizapo kuti kutsogoloku kuchitika zotani? Baibulo limasonyeza kuti posachedwapa kuchitika zinthu zapadera zomwe zidzakhudze anthu onse padzikoli.

Yesu anafotokoza mmene ‘tidzadziwire kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.’ (Luka 21:31) Iye analosera kuti padzikoli padzakhala zinthu monga nkhondo zoopsa, zivomerezi zikuluzikulu, njala komanso miliri ndipo zinthu zimenezi tikuziona masiku ano.​—Luka 21:10-17.

Baibulo limasonyezanso kuti ‘m’masiku otsiriza’ a ulamuliro wa anthu, anthu adzakhala ndi makhalidwe oipa ndipo mukhoza kuwerenga zimenezi pa 2 Timoteyo 3:1-5. Mukaona anthu akuchita makhalidwe amenewa masiku ano, kodi simuvomereza kuti ulosi wa m’Baibulowu ukukwaniritsidwa panopa?

Ndiye kodi zimenezi zikutiuza chiyani? Zikutiuza kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kusintha kwambiri zinthu padzikoli kuti ziyambe kuyenda bwino. (Luka 21:36) Kudzera m’Baibulo, Mulungu walonjeza zinthu zabwino zokhudza dziko lapansi komanso anthu amene adzakhale padzikoli. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

ULAMULIRO WABWINO

“Kenako anamupatsa [Yesu] ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira. Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.”—DANIELI 7:14.

Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Mukhoza kudzakhala ndi moyo wosangalala mu ulamuliro wabwino kwambiri wa padziko lonse umene Mulungu wakhazikitsa komanso wasankha Yesu kuti akhale Mfumu.

MOYO WATHANZI

“Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”​YESAYA 33:24.

Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Simudzadwala kapena kulumala ndipo mudzakhala ndi moyo mpaka kalekale osafa.

MTENDERE WENIWENI

“Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​SALIMO 46:9.

Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Palibe amene azidzaopa kuti kukhala nkhondo komanso sipadzakhala mavuto amene amabwera chifukwa cha nkhondo.

DZIKO LIDZADZAZA NDI ANTHU ABWINO OKHAOKHA

“Woipa sadzakhalakonso . . . Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi.”​SALIMO 37:10, 11.

Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Padzikoli sipadzakhalanso anthu oipa, koma padzakhala anthu okhawo amene amafunitsitsa kumvera Mulungu.

DZIKO LONSE LAPANSI LIDZAKHALA PARADAISO

“Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.”​YESAYA 65:21, 22.

Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Dziko lonse lapansi lidzakhala lokongola kwambiri. Mulungu adzayankha pemphero lathu lakuti chifuniro chake chichitike “pansi pano.”​—Mateyu 6:10.