Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhulupirika kuli ngati nangula woteteza banja lanu mukakumana ndi mavuto okhala ngati chimphepo

MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

1: Kukhulupirika

1: Kukhulupirika

ZIMENE ZIMACHITIKA

Munthu akakhala wokhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wake, amaona kuti banja ndi mgwirizano wa moyo wonse ndipo sakayikirana. M’banja lotere, palibe amene amakhala ndi nkhawa kuti mnzake akhoza kumuthawa ngati zinthu zitavuta.

Mabanja ena amakakamizika kukhalabe limodzi chifukwa choopa zimene anzawo kapena achibale awo anganene ngati atasiyana. Komabe ngati mwamuna ndi mkazi wake sakondana komanso salemekezana, zimakhala zovuta kuti azikhulupirirana.

MFUNDO YA M’BAIBULO: ‘Mwamuna asasiye mkazi wake.’​—1 Akorinto 7:11.

A Micah ananena kuti: “Ngati umaona mwamuna kapena mkazi wako kukhala wofunika, sukhumudwa kwambiri akakulakwira. Ndipo simuvutika kukhululukirana kapena kupepesana mukalakwirana. Mumangoona mavutowo ngati nkhani yaing’ono osati ngati chifukwa chothetsera banja.”

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

M’banja limene mwamuna kapena mkazi ndi wosakhulupirika, akakumana ndi mavuto amangoti, ‘tinakumana okulakula.’ Ndipo zikatero amafunafuna njira zothetsera banjalo.

A Jean ananena kuti: “Anthu ambiri amalowa m’banja ali ndi maganizo akuti adzathetsa banjalo zinthu zikadzavuta. Munthu akalowa m’banja ali ndi maganizo amenewa zimakhala zovuta kuti akhale wokhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wake.”

ZIMENE MUNGACHITE

DZIFUNSENI KUTI

Tikasemphana maganizo . . .

  • Kodi ndimaona kuti ndinalakwitsa kukwatirana ndi mwamuna kapena mkazi wangayu?

  • Kodi ndimaganiza kuti nthawi ina ndikhoza kudzakwatirana ndi mwamuna kapena mkazi wina?

  • Kodi nthawi zina ndimalankhula mawu monga akuti: “Nditha kukusiya” kapena “nditha kupeza wina wondikonda?”

Ngati mwavomera kuti inde pa funso limodzi kapena angapo, dziwani kuti mukufunika kulimbitsa banja lanu panopa.

ZOTI MUKAMBIRANE

  • Kodi panopa chikondi chathu chachepa? Ngati ndi choncho, n’chiyani chikuchititsa zimenezi?

  • Kodi tingatani kuti tizikondana kwambiri?

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI

  • Nthawi zambiri muzilembera mawu achikondi mwamuna kapena mkazi wanu

  • Muzisonyeza kuti mumakonda kwambiri mwamuna kapena mkazi wanu poika zithunzi zake pamalo oonekera mukakhala kuntchito

  • Tsiku lililonse muziimbira foni mwamuna kapena mkazi wanu mukakhala kuntchito kapena mukapita kwinakwake

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”​—Mateyu 19:6.