Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ana anu amatengera zotani kwa inu?

 MAKOLO

8: Kupereka Chitsanzo

8: Kupereka Chitsanzo

ZIMENE ZIMACHITIKA

Makolo omwe amatsatira zomwe amaphunzitsa amapereka chitsanzo chabwino kwa ana awo. Zingakhale zovuta kuti mwana wanu azinena zoona ngati inuyo simulankhula zoona. Mwachitsanzo, mwina kunyumba kukabwera anthu enaake mumanena kuti, “Mungowauza kuti ndachokapo.”

A David ananena kuti: “Makolo ambiri amakonda kunena kuti, ‘Musamayang’ane zomwe ndimachita, muzingochita zomwe ndakuuzani.’ Zimenezi sizipereka chitsanzo chabwino kwa ana. Ana amatengera chilichonse chomwe mumanena ndi kuchita. Ngati zomwe tikuwauza sizikugwirizana ndi zomwe timachita, anawo amaonanso zimenezo.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Iwe amene umalalikira kuti ‘Usabe,’ umabanso kodi?”​—Aroma 2:21.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Ana aang’ono komanso achinyamata amatengera kwambiri zimene makolo awo amachita kuposanso zomwe amaona kwa anthu ena komanso anzawo. Zimenezi zikusonyeza kuti makolo ayenera kupereka chitsanzo chabwino pophunzitsa ana awo. Choncho zimene mumanena zizigwirizana ndi zimene mumachita.

A Nicole ananena kuti: “Nthawi zina mukhoza kunena zinthu zina mobwerezabwereza chifukwa choganiza kuti mwana wanu sakumva. Koma tsiku lina mukadzachita zosemphana ndi zomwe munkanenazo, mwana wanu adzadziwa zimenezo. Ana amaonetsetsa zimene timachita ndipo tisamaganize kuti palibe chomwe akudziwa.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Nzeru yochokera kumwamba, . . . ndi yopanda chinyengo.”​—Yakobo 3:17.

ZIMENE MUNGACHITE

Muziganizira zomwe mumachita. Kodi mumaonera mafilimu otani? Kodi mumasonyeza khalidwe lotani kwa mwamuna kapena mkazi wanu komanso kwa ana anu? Kodi mumacheza ndi anthu otani? Kodi mumachita zinthu moganizira ena? Mwachidule tingafunse kuti, kodi zimene mumachita ndi zimene mumafuna mwana wanu atatengera?

A Christine ananena kuti: “Ine ndi mwamuna wanga sitikakamiza ana athu kuchita zinthu zomwe ife sitichita.”

Muzipepesa mukalakwitsa. Ana anu amadziwa kuti nanunso mumalakwitsa nthawi zina. Choncho mukamapepesa mwamuna kapena mkazi wanu komanso ana anu, mumawaphunzitsa kukhala okhulupirika komanso kukhala odzichepetsa.

A Robin ananena kuti: “Makolofe timafunika kuvomereza tikalakwitsa zinazake ndipo tizipepesa. Koma ngati sitingachite zimenezo, ana athu adzatengeranso zomwezo. Nawonso sangamavomere akalakwitsa.”

A Wendell ananena kuti: “Ana amatengera kwambiri zomwe makolofe timachita. Zinthu zomwe amationa tikuchita nthawi zonse n’zimene nawonso amachita. Zimakhala ngati ali kusukulu ndipo akuphunzira phunziro limodzimodzilo nthawi zonse.”