Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 1 2018 | Mungatani Kuti Muzikhala Wosangalala?

KODI MALANGIZO OTHANDIZA KUTI TIZIKHALA OSANGALALA TINGAWAPEZE KUTI?

Baibulo limanena kuti: “Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu m’njira zawo.”​—Salimo 119:1.

Nkhani zokwana 7 zomwe zili m’magaziniyi zikufotokoza zimene tingachite kuti tizikhala osangalala.

 

Zimene Mungachite

Kodi inuyo mumakhala wosangalala? Kodi ndi chiyani chomwe chimachititsa munthu kuti azisangalala?

Kukhala Wokhutira Komanso Wopatsa

Ambiri amaona kuti munthu amene ali ndi chuma kaya katundu wambiri ndi amene amakhala wosangalala. Koma kodi munthu akakhala ndi ndalama komanso katundu amakhala wosangalala nthawi zonse? Kodi ochita kafukufuku anapeza zotani pa nkhaniyi?

Kukhala Wathanzi Komanso Wopirira

Kodi kuvutika ndi matenda kungachititse munthu kuti asamasangalale?

Chikondi

Kusonyezana chikondi kumathandiza kuti anthu azikhala mosangalala.

Kukhululuka

Munthu amene amakhalira kukwiya komanso kusunga zifukwa, sakhala wosangalala komanso sakhala wathanzi.

Kudziwa Chifukwa Chake Tili Ndi Moyo

Kupeza mayankho ogwira mtima a mafunso ofunika kwambiri pa moyo kungatithandize kuti tizikhala osangalala.

Kukhala ndi Chiyembekezo

Anthu ambiri zimawavuta kukhala osangalala akaona kuti tsogolo lawo kapena la anthu amene amawakonda silikuoneka bwinobwino.

Dziwani Zambiri Zokhudza Zimene Mungachite Kuti Muzikhala Osangalala

Pali zinthu zambiri zomwe zingachititse kuti munthu azikhala osangalala kapena ayi. Werengani Galamukaniyi kuti mupeze mfundo zomwe zingakuthandizeni kuti muzikhala osangalala.