Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUNGATANI KUTI MUZIKHALA WOSANGALALA?

Kudziwa Chifukwa Chake Tili Ndi Moyo

Kudziwa Chifukwa Chake Tili Ndi Moyo

ANTHUFE TINALENGEDWA MODABWITSA CHIFUKWA TIMATHA KULEMBA, KUJAMBULA, KOMANSO KUKONZA ZINTHU. TIMATHANSO KUDZIFUNSA MAFUNSO OFUNIKA KWAMBIRI NGATI AKUTI: N’chifukwa chiyani kuli zinthu zachilengedwe zonsezi? Kodi anthufe tinachokera kuti? N’chifukwa chiyani tili ndi moyo? Kodi n’chiyani chidzachitike m’tsogolo?

Anthu ena amaona kuti mafunsowa ndi ovuta ndipo salimbana ndi kufufuza mayankho ake. Pomwe ena amati mafunsowa ndi opanda nzeru chifukwa zamoyo zinangokhalako zokha. Pulofesa wina woona za mbiri yakale komanso woona za zinthu zamoyo dzina lake William Provine, ananena kuti: “Kunjaku kulibe mulungu choncho sitinganene kuti moyo wathu uli ndi cholinga chilichonse. Nditha kunenanso kuti, ‘sindiona zifukwa zomwe timakhazikitsira mfundo zimene timayendera, ndipo sindiona cholinga chenicheni cha moyo wathuwu.’”

Komabe anthu ena amaona kuti maganizo amenewa ndi osathandiza. Anthuwa amaona kuti zinthu zam’chilengedwe zimatsatira mfundo komanso malamulo enaake. Amadabwa ndi mmene zinthu zam’chilengedwe zinapangidwira moti mpaka amafika popanga zinthu zina potengera mmene zinthuzi zilili. Zinthu zochititsa chidwi zomwe amapeza akafufuza, zimasonyeza kuti pali winawake wanzeru kwambiri amene anazipanga.

Zimenezi zachititsa anthu ena omwe ankakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, kusintha maganizo awo. Mwachitsanzo, tiyeni tione zomwe anthu ena awiri ananena:

DR. ALEXEI MARNOV NDI DOKOTALA WOPANGA MAOPALESHONI A UBONGO. A Marnov ananena kuti: “Kumasukulu omwe ndinkapita ankatiphunzitsa kuti kulibe Mulungu ndipo ankati zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Aliyense wokhulupirira kuti kuli Mulungu ankamuona ngati wotsalira.” Koma pofika mu 1990, a Marnov anasintha zomwe ankakhulupirira.

Dokotalayu ananenanso kuti: “Ndakhala ndikufufuza kuti ndidziwe mmene zachilengedwe komanso ubongo wa munthu zimagwirira ntchito. Ubongo umadziwika kuti ndi chiwalo chomwe chinapangidwa mogometsa kwambiri. Nthawi zina ndinkadzifunsa kuti, koma kodi ubongowu unapangidwa kuti uzithandiza munthu kuphunzira zinthu n’kukhala katswiri koma kenako basi n’kufa. Ndinkaona kuti zinali zosamveka. Ndinkadzifunsabe kuti, kodi anthufe tinakhalako bwanji? Nanga n’chifukwa chiyani tili ndi moyo? Koma nditafufuza mozama, ndinaona kuti pali winawake amene analenga zinthu zonsezi.”

A Marnov anayamba kuphunzira Baibulo kuti adziwe zambiri zokhudza moyo. Mkazi wawo ndi dokotala ndipo nayenso ankakhulupirira kuti kulibe Mulungu. Kenako anayambanso kuphunzira Baibulo pofuna kusonyeza mwamuna wake kuti zomwe ankaphunzirazo zinali zolakwika. Panopa a Marnov ndi mkazi awo amakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo amamvetsa chifukwa chimene analengera anthu.

DR. HUABI YIN NDI KATSWIRI WOONA ZA MPHAMVU ZA DZUWA. Kwa zaka zambiri a Yin anaphunzira mmene zinthu zinapangidwira ndipo anachitanso kafukufuku wokhudza mphamvu za dzuwa. Pa zinthu zonse zomwe ziliko m’chilengedwechi, dzuwa ndi lamphamvu kwambiri.

A Yin ananena kuti: “Tikamafufuza zinthu zachilengedwe pa kafukufuku wathu wa sayansi, timaona kuti zinthu zam’chilengedwe zimachita zinthu mwadongosolo komanso kutsatira malamulo enaake. Komano ndinkadzifunsa kuti, ‘kodi malamulowa anapangidwa ndi ndani? Ngati moto umene timaphikirawu umafunika kuuyang’anira kuti usawononge zinthu, nanga dzuwa lamphamvu zambiri chonchi, amaliyang’anira ndi ndani?’ Patapita nthawi ndinaona kuti mawu a pa Genesis 1:1 ndi omveka. Mawuwo amati: ‘Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.’”

N’zoona kuti sayansi yatithandiza kudziwa mmene ubongo umagwirira ntchito komanso zimene zimachitika kuti dzuwa lizitulutsa mphamvu yotentha. Koma monga ananenera a Marnov ndi a Yin, Baibulo latithandiza kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri okhudza moyo. Mwachitsanzo, timadziwa chifukwa chake kuli zinthu zachilengedwezi, chifukwa chake zinthu zam’chilengedwe zimatsatira malamulo komanso chifukwa chimene anthufe tinakhalira ndi moyo.

Ponena za dzikoli, Baibulo limanena kuti: ‘[Mulungu] sanalilenge popanda cholinga, koma analiumba kuti anthu akhalemo.’ (Yesaya 45:18) Lembali likusonyeza kuti Mulungu analenga dzikoli ndi cholinga. Nkhani yotsatira isonyeza kuti cholinga chimenechi ndi chogwirizana kwambiri ndi zimene tikuyembekezera m’tsogolo.