MUNGATANI KUTI MUZIKHALA WOSANGALALA?
Dziwani Zambiri Zokhudza Zimene Mungachite Kuti Muzikhala Osangalala
KODI MUNADZIFUNSAPO KUTI:
-
Ndingatani kuti banja langa lizisangalala?
-
Ndingatani kuti ndipeze anzanga abwino komanso kuti ena azindiona kuti ndine munthu wabwino?
-
Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?
-
Kodi mavuto amene timakumana nawowa adzathadi?
-
Kodi anthu sadzaliwonongeratu dziko lapansili?
-
Kodi zipembedzo zonse zimathandiza anthu kudziwa Mulungu woona?
KUTI MUPEZE MAYANKHO A MAFUNSOWA KOMANSO ENA
Pitani pawebusaiti yathu ya jw.org yomwe ikupezeka m’zinenero zoposa 900. Pamalowa mukhoza kupeza mfundo zothandiza kwambiri pa nkhani zosiyanasiyana.
Mungapezeponso mavidiyo a anthu osiyanasiyana omwe anayamba kusangalala ataphunzira Baibulo ndipo sakunong’oneza bondo. Ena mwa anthuwa ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo ena anali akaidi. Enanso ndi ophunzira kwambiri kuphatikizaponso akatswiri a zasayansi.
Pa jw.org/ny mukhoza kuwerenga kapena kupanga dawunilodi Mabaibulo komanso mabuku ndi magazini osiyanasiyana, kwaulere. Nkhani zina zomwe mungazipeze pawebusaiti ndi izi: