Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUNGATANI KUTI MUZIKHALA WOSANGALALA?

Zimene Mungachite

Zimene Mungachite

KODI INUYO MUMAKHALA WOSANGALALA? Ngati ndi choncho, n’chiyani chimakuchititsani kuti muzisangalala? Kodi ndi banja lanu, ntchito kapena chipembedzo chanu? Kapena panopa mukuyembekezera chinachake chomwe chidzakuchititseni kukhala wosangalala. Mwina mukuyembekezera kumaliza sukulu, kupeza ntchito yabwino kapena kugula galimoto yatsopano.

Anthu ambiri amaona kuti amakhala osangalala akakwanitsa cholinga chomwe anali nacho kapena akapeza chinthu chimene ankafuna. Koma kodi amasangalala kwa nthawi yaitali bwanji? N’zomvetsa chisoni kuti kawirikawiri amangosangalala kwa kanthawi kochepa basi.

Akatswiri amanena kuti munthu wosangalala ndi amene kwa nthawi yaitali amakhala wopanda nkhawa ndipo amakhala ndi moyo wokhutira moti amafunitsitsa kukhalabe ndi moyo ngati umenewo nthawi zonse.

Amanenanso kuti munthu amafunika kukhala wosangalala nthawi zonse. Amati kukhala wosangalala kuli ngati ulendo wopitirira osati ngati cholinga chomwe munthu amafuna atangochikwaniritsa. Anthu amene amanena kuti adzakhala osangalala akadzapeza kapena kuchita zinazake nthawi ina, sakhala ndi moyo wosangalala.

Mwachitsanzo, kukhala wosangalala tingakuyerekeze ndi kukhala ndi moyo wathanzi. Kuti tikhale athanzi, timafunika kudya zakudya zoyenera, kuchita masewera olimbitsa thupi komanso kuchita zinthu zina zofunika. N’chimodzimodzinso ndi kukhala wosangalala. Timafunika kutsatira mfundo zoyenera pa moyo wathu.

Kodi timafunika kutsatira makhalidwe komanso mfundo ziti kuti tikhaledi munthu wosangalala? Ngakhale kuti mfundo zina zingakhale zofunika kwambiri kuposa zina, mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni:

  • KUKHALA WOKHUTIRA KOMANSO WOPATSA

  • KUKHALA WATHANZI KOMANSO WOPIRIRA

  • CHIKONDI

  • KUKHULULUKA

  • KUDZIWA CHIFUKWA CHAKE TILI NDI MOYO

  • KUKHALA NDI CHIYEMBEKEZO

Buku la Masalimo lomwe anthu ambiri amati ndi buku la malangizo anzeru limati: “Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu m’njira zawo.” (Sal. 119:1) Tiyeni tsopano tikambirane njira zotchulidwa palembali.