Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mchira wa Gulo

Mchira wa Gulo

GULO amatha kudumpha mosavuta kuchoka pansi kupita pakhoma. Koma ngati pansipo ndi poterera, gulo amavutika kuti adumphe moti kuti akafike pa khoma bwinobwino osagwa, amadalira mchira wake.

Taganizirani izi: Gulo akafuna kudumpha amagwira kwambiri pansi zomwe zimathandiza kuti thupi lake likonzekere kudumpha n’kukafika pakhoma kapena pamtengo osagwa. Koma pansi pakakhala poterera, gulo amadumpha thupi lake lisanakonzeke bwinobwino. Ali m’malere, gulo amalozetsa mchira wake m’mwamba zomwe zimamuthandiza kuti thupi lake liloze pamene akufuna kukaima. Koma polozetsa mchirawo m’mwamba, samangouyendetsa mwachisawawa, amauyendetsa mwaluso kwambiri kuti asagwe. Lipoti lina limene yunivesite ya California, Berkeley inatulutsa linati: “Gulo amafunika kuyendetsa mchira wake mwaluso kwambiri ali m’malere kuti thupi lake likhale lowongoka.” Ngati pamene wanyamukira pali poterera kwambiri, guloyo amafunika kupinda kwambiri mchira wake kuti asagwe.

Mchira wa guloyo ukhoza kuthandiza akatswiri opanga maloboti, omwe angathandize kufufuza anthu opulumuka pakachitika chivomezi kapena ngozi zina za chilengedwe. Maloboti amenewa akhoza kumayenda mofulumira m’malo oterera kwambiri koma osagudubuka. Wasayansi wina, dzina lake Thomas Libby ananena kuti: “Maloboti sachedwa kugwa poyerekeza ndi zinyama, choncho ngati akatswiri atakwanitsa kupanga maloboti oti asamagwe ndiye kuti apita patsogolo kwambiri.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti mchira wa gulo ukhale woterewu kapena pali wina amene anachita kukonza kuti uzichita zimenezi?