Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Osamukira Kudziko Lina Amakapezadi Zimene Akufuna?

Kodi Osamukira Kudziko Lina Amakapezadi Zimene Akufuna?

Kufunafuna Moyo Wabwino

GEORGE ankakhala m’dziko losauka kwambiri ndipo ankadziwa kuti atangosamukira kudziko lina akhoza kukapeza ntchito yabwino. M’dziko lawo, iye ankalephera kupezera banja lake chakudya chokwanira. Anthu ambiri am’dera lake ankadwala komanso kusowa chakudya, pomwe dziko lina loyandikana ndi dziko lawo linali lolemera. Choncho George anaganiza zosamukira kudziko limenelo kuti akapeze ntchito. Iye ankaganiza kuti akakapeza ntchitoyo adzatenga banja lake kuti lizikakhala naye.

Patricia ankafuna atasamukira kudziko lina. Zinali zovuta kupeza ntchito komanso maphunziro abwino m’dziko la kwawo. Choncho iye ndi chibwenzi chake anachoka ku Nigeria kudutsira ku Algeria pa ulendo wawo wopita ku Spain. Iwo sankadziwa kuti ulendo wodutsa m’chipululu cha Sahara unali wovuta kwambiri. Patricia ananena kuti: “Ndinasamuka chifukwa chakuti ndinali wodwala ndipo ndinkafuna kuti mwana wangayo asadzavutike ndi umphawi.”

Rachel wa ku Philippines ankafuna kusamukira ku Ulaya chifukwa chakuti anali atachotsedwa ntchito. Azibale ake anamuuza kuti atapita kunja akhoza kukapeza ntchito yam’nyumba mosavuta. Choncho iye anakongola ndalama zoti alipirire ndege ndipo anatsimikizira mwamuna wake ndi mwana wake kuti sipapita nthawi yaitali asanaonane.

Zikuoneka kuti anthu 200 miliyoni anasamukira kudziko lina ngati mmene anachitira George, Patricia, ndi Rachel. Ngakhale kuti ena amasamuka kudziko lawo chifukwa chothawa kuzunzidwa, nkhondo komanso masoka achilengedwe, ambiri amasamuka chifukwa cha mavuto a zachuma. Kodi anthu amene amasamukira kudziko lina amakumana ndi mavuto otani? Kodi amakakhaladi mosangalala ngati mmene amaganizira? Kodi ana amakumana ndi zotani kholo likasamukira kudziko lina? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso amenewa.

 Vuto la Kayendedwe Komanso Kuzolowera Dziko Lachilendo

Vuto loyamba limene anthu osamukira kudziko lina amakumana nalo ndi kayendedwe. George, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, anayenda ulendo wautali ali ndi chakudya chochepa. Iye anati: “Sindinavutikepo ngati mmene ndinavutikira paulendo umenewu.” Ndipo anthu ambiri amene amasamuka samakafika n’komwe kumene amapitako.

Cholinga cha Patricia, yemwe tamutchula kale uja, chinali choti akafike ku Spain. Choncho iye anayenda ulendo wapalole kudutsa m’chipululu cha Sahara. Iye anafotokoza kuti: “Ulendo wochoka ku Nigeria kukafika ku Algeria unatitengera mlungu umodzi. M’galimotoyo tinali anthu 25 ndipo tinakhala mopanikizana kwambiri. Paulendowu tinaona mitembo yambirimbiri komanso anthu akungoyendayenda m’chipululu kusowa mtengo wogwira. Zikuoneka kuti anthu amenewa anali atasiyidwa ndi madalaivala a magalimoto omwe anakwera.”

Koma Rachel sanavutike ndi mayendedwe ngati mmene anachitira George komanso Patricia, chifukwa popita ku Ulaya anakwera ndege ndipo anapezadi ntchito yam’nyumba. Koma vuto linali lakuti ankamusowa kwambiri mwana wake wamkazi wazaka ziwiri. Iye anafotokoza kuti: “Ndinkati ndikaona mayi akusamalira mwana wake, mtima unkandipweteka kwambiri.”

George nayenso anavutika kuti azolowere moyo wa m’dziko lomwe anasamukira. Panapita miyezi yambiri asanayambe kutumiza ndalama kumudzi kwawo. Iye anafotokoza kuti: “Nthawi zambiri usiku ndinkalira chifukwa chosowa wocheza naye komanso nkhawa.”

Patatha miyezi yambiri, Patricia anafika kumalire a dziko la Algeria ndi Morocco. Iye anafotokoza kuti: “Mwana wanga wamkazi anabadwira kumeneko. Ndinkakhala mobisa poopa anthu omwe amagwira azimayi kuti azikawagwiritsa ntchito ya uhule. Kenako ndinapeza ndalama zolipirira ulendo wapanyanja wopita ku Spain. Ulendowu unali woopsa kwambiri chifukwa botilo linali lophwasukaphwasuka ndipo linali losayenera kunyamula anthu ambiri. Nthawi zambiri m’botimo munkalowa madzi moti tinkachita kuwakapa ndi nsapato. Ndinafika ku Spain nditatopa kwambiri moti ndinkachita kulephera kuyenda.”

N’zoona kuti anthu amene akuganiza zosamukira ku dziko lina ayenera kuganizira mavuto amene angakumane nawo pa ulendowo. Koma ayenera kuganiziranso vuto lachinenero komanso kusiyana zikhalidwe. Amavutikanso kuti apeze chilolezo choti akhale nzika kapena chowalola kugwira ntchito m’dzikolo. Anthu omwe alibe chilolezo chokhala m’dzikolo sangapeze ntchito, nyumba, maphunziro komanso chithandizo chamankhwala chabwino. Iwo sangathe kupezanso laisensi ya galimoto kapena kutsegula akaunti ya ku banki. Kawirikawiri anthu ochoka kudziko lina omwe alibe makalata owaloleza kukhala m’dzikolo amangogwiritsidwa ntchito za ndalama zochepa.

Chinanso chimene ayenera kuganizira ndi mmene amaonera ndalama. Kodi tiyenera kudalira kwambiri ndalama? Baibulo limatichenjeza kuti: “Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma. . . . Kodi maso ako amayang’anitsitsa chuma, pomwe icho sichichedwa kuchoka? Chifukwa ndithu chimadzipangira mapiko ngati a chiwombankhanga n’kuulukira kumwamba.” (Miyambo 23:4, 5) Tizikumbukira kuti zimene timafunikira kwambiri pa moyo ndi  zinthu monga chikondi, mtendere wam’maganizo komanso mtendere wam’banja zomwe sizifuna ndalama. Koma zimakhala zomvetsa chisoni kuti makolo ena amasiya ana awo alibe aliyense amene angawasonyeze chikondi n’cholinga chokafunafuna ndalama.—2 Timoteyo 3:1-3.

Komanso anthufe timafunikira kupeza zosowa zathu zauzimu. (Mateyu 5:3) Choncho makolo anzeru amayesetsa kukwaniritsa udindo umene Mulungu anawapatsa wophunzitsa ana awo za Mulungu, cholinga chake komanso zimene iye amafuna.—Aefeso 6:4.

 Chofunika Kwambiri Kuposa Ndalama

Pali nkhani zosiyanasiyana zokhudza anthu amene anasamukira kudziko lina koma pali vuto limodzi lofanana mu nkhanizi monga taonera pa zimene zinachitikira George, Rachel, ndi Patricia. Vutolo ndi loti banja lonse limavutika mmodzi m’banja akasamukira kudziko lina ndipo pamatenga zaka zambiri kuti banjalo lidzakumanenso. N’zimene zinam’chitikira George, chifukwa panatenga zaka zinayi kuti akumanenso ndi banja lake.

Rachel anabwerera ku Philippines kukatenga mwana wake patatha pafupifupi zaka zisanu. Ndipo Patricia anafika ku Spain ali ndi mwana wakhanda m’manja. Iye ananena kuti: “Ndimamukonda kwambiri mwana wangayu chifukwa ndimaona kuti kunoko wachibale wanga ndi yekhayu basi.”

Ena amayesetsabe kuzolowera moyo wa dziko limene asamukira ngakhale kuti amasowa ocheza nawo, amasowa ndalama komanso amasowa banja lawo. Anthu amenewa amakhala kuti awononga ndalama zambiri kuti akafike kudziko lina, choncho zinthu zikavuta, safuna kubwerera ali chimanjamanja chifukwa amaopa kuchita manyazi.

Allan ndi m’modzi wa anthu amene analimba mtima kubwerera kwawo ku Philippines. Iye anapeza ntchito yabwino ku Spain koma anangogwira kwa chaka ndi miyezi 6 basi. Allan ananena kuti: “Ndinkafunitsitsa nditaonananso ndi mkazi wanga komanso mwana wanga wamkazi. Ndinawasowa kwabasi. Ndinaganiza kuti ngati ndikufuna kukagwira ntchito kudziko lina, ndidzapite ndi banja langa ndipo zimenezi n’zimene pamapeto pake ndinachita. Ndimaona kuti banja langa ndi lofunika kwambiri kuposa ndalama.”

Patricia anapezanso kuti pali chinthu china chomwe ndi chofunika kwambiri kuposa ndalama. Popita ku Spain, anatenga Baibulo lake la “Chipangano Chatsopano,” kapena kuti la Malemba Achigiriki. Iye anafotokoza kuti: “Ndinkaona Baibuloli ngati chithumwa chondipatsa mwayi. Kenako tsiku lina mayi wina wa Mboni za Yehova anafika kumene ndinkakhala. Poyamba a Mboni akafika pakhomo panga sindinkawalandira. Koma patsikulo ndinafunsa mayiyo mafunso ambiri n’cholinga choti ndimusonyeze kuti zimene amakhulupirira n’zabodza. Koma mayiyo anayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo ndipo anasonyeza kuti zimene amakhulupirira n’zoona.”

Zimene Patricia anaphunzira zinamuthandiza kudziwa kuti ndalama kapena kusamukira kudziko lina sikungathandize munthu kuti akhale wosangalala. Koma munthu amakhala wosangalala komanso kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha akamaphunzira za Mulungu ndi cholinga chake. (Yohane 17:3) Patricia anaphunziranso kuti dzina la Mulungu woona ndi Yehova. (Salimo 83:18) Iye anawerenganso m’Baibulo kuti posachedwapa Mulungu abweretsa Ufumu wake, womwe mfumu yake ndi Yesu Khristu ndipo udzathetsa umphawi. (Danieli 7:13, 14) Ndipotu lemba la Salimo 72:12, 14 limanena kuti: “[Yesu] adzalanditsa wosauka wofuulira thandizo, komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza.”

Mungachite bwino kupeza nthawi yophunzira Baibulo. Buku limeneli lili ndi nzeru zochokera kwa Mulungu ndipo lingakuthandizeni kudziwa zinthu zomwe zili zofunika kwambiri pa moyo wanu. Lingakuthandizeninso kuti muzisankha bwino zinthu ndiponso kupirira mavuto amene mumakumana nawo.—Miyambo 2:6-9, 20, 21.