Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Anthu Ovutika

Anthu Ovutika

Kodi Mulungu amathandiza anthu ovutika?

“Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama. . . . Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’”Aheberi 13:5.

MMENE MULUNGU AMATHANDIZIRA

Mtumiki wa Yehova akakumana ndi mavuto, Mulungu amamuthandiza m’njira zosiyanasiyana. Njira imodzi imene amatithandizira ndi kudzera mwa Akhristu anzathu. * Lemba la Yakobo 1:27 limati: “Kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo.”

Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankathandizana akavutika. Mwachitsanzo, mneneri wina atalosera kuti kudzagwa chilala chimene chidzakhudze kwambiri dera la Yudeya, Akhristu a mumzinda wa ku Antiokeya, ku Siriya, “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo lililonse limene akanatha kwa abale okhala ku Yudeya.” (Machitidwe 11:28-30) Zimenezi zinathandiza kwambiri Akhristu omwe ankavutikawo ndipo zinasonyeza kuti ankakondanadi kuchokera pansi pa mtima.—1 Yohane 3:18.

 Zimene ovutikawo angachite pawokha

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.”—Yesaya 48:17, 18.

MULUNGU AMATIPATSA MALANGIZO

Anthu ambiri azindikira kuti nzeru za m’Baibulo n’zothandiza ndipo sitingaziyerekezere ndi nzeru za anthu. Lemba la Miyambo 2:6, 7 limati: “Yehova amapereka nzeru. Kudziwa zinthu ndi kuzindikira kumatuluka m’kamwa mwake. Anthu owongoka mtima, iye amawasungira nzeru zopindulitsa.” Anthu akamagwiritsa ntchito nzeru zimenezi amapindula.

Mwachitsanzo, amapewa zinthu zimene zimangowonongetsa ndalama monga mankhwala osokoneza bongo ndi kumwa mwauchidakwa. (2 Akorinto 7:1) Amachitanso zinthu moona mtima, amakhala olimbikira ntchito komanso odalirika. Zimenezi zimathandiza kuti asamavutike kupeza ntchito komanso kuti mabwana awo aziwadalira. Lemba la Aefeso 4:28 limati: “Wakubayo asabenso, koma agwire ntchito molimbikira. . . . kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.”

Kodi pali umboni wosonyeza kuti Baibulo lili ndi malangizo othandiza?

Nzeru [ya Mulungu] imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.”—Mateyu 11:19.

UMBONI WOSONYEZA KUTI YEHOVA AMATHANDIZA.

Wilson, yemwe amakhala ku Ghana, ankagwira ntchito yaganyu pa kampani inayake. Pa tsiku lake lomaliza kugwira pakampaniyo, anapeza ndalama m’galimoto ya bwana wamkulu pamene ankaitsuka. Bwana wina amene ankamuyang’anira anamuuza kuti atenge ndalamazo. Koma Wilson, yemwe ndi wa Mboni za Yehova, anakana kutenga ndalamazo chifukwa kunali ngati kuba. Iye anakabweza ndalamazo kwa bwana wamkuluyo. M’malo moti ntchito yake ithe, bwanayo anamulemba ntchito ndipo kenako anadzamukweza kukhala woyang’anira antchito ena pakampanipo.

Géraldine, yemwe amakhala ku Ulaya, anachotsedwa ntchito chifukwa chakuti abwana ake ankadana ndi Mboni za Yehova. Koma amayi ake a bwanayo anamuuza kuti sanachite bwino kumuchotsa ntchito Géraldine. Mayiyo anati: “Ngati pali anthu olimbikira ntchito komanso okhulupirika ndi a Mboni za Yehova.” Bwanayo anayamba kufufuza kuti adziwe zambiri za Mboni za Yehova kenako anamuitana Géraldine kuti adzayambirenso ntchito.

Sarah, yemwe amakhala ku South Africa ndipo akulera yekha ana, anaona mmene Baibulo limathandizira anthu kuti azikondana. Atavutika kwambiri, Akhristu a mumpingo mwake ankamubweretsera chakudya komanso thiransipoti. Nthawi ina ana ake ananena kuti: “Timaona kuti tili ndi makolo ambiri mumpingo mwathu.”

Izi ndi zina mwa zitsanzo zosonyeza kuti Mulungu amathandiza anthu ovutika. Zimenezi zimatikumbutsa lemba la Miyambo 1:33, lomwe limati: “Munthu wondimvera [ine Yehova] adzakhala mwabata.” Mawu amenewa ndi oona.

^ ndime 5 M’mayiko ena, boma limapereka ndalama kwa anthu ovutika. Koma m’mayiko amene zimenezi kulibe, achibale a munthuyo ndi amene ali ndi udindo womuthandiza.—1 Timoteyo 5:3, 4, 16.