Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zotheka Kulera Nokha Ana

N’zotheka Kulera Nokha Ana

N’zotheka Kulera Nokha Ana

MABANJA okhala ndi makolo onse awiri akucheperachepera padziko lonse. Mwachitsanzo, ku United States kokha kuli makolo oposa 13 miliyoni amene akulera okha ana ndipo ambiri mwa makolo amenewa ndi akazi. Kafukufuku akusonyeza kuti pafupifupi theka la ana onse ku United States panthawi ina adzaleredwa ndi mayi kapena bambo wokha.

Ngati ndinu mayi kapena bambo amene mukulera nokha ana, musataye mtima, zinthu zikhoza kukuyenderani bwino. Yesani kugwiritsa ntchito mfundo zotsatirazi:

Muzipewa maganizo olakwika. Baibulo limati: “Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.” (Miyambo 15:15) Mwina panopa inuyo zinthu sizikukuyenderani bwino, koma monga mmene lembali lasonyezera, kuti munthu akhale wosangalala zimadalira mmene munthuyo amaonera zinthu, osati mmene zinthu zilili pamoyo wake. (Miyambo 17:22) Palibe chimene mungapindule ngati mumangokhalira kuganiza kuti ana anu alibe tsogolo kapena banja lanu silingayendenso bwino. Maganizo amenewa ndi osathandiza ndipo angachititse kuti muzilephera kulera ana anu.—Miyambo 24:10.

Yesani izi: Lembani mawu olakwika amene mumanena okhudza mmene zinthu zilili pabanja lanu, ndipo pa mawu aliwonse olakwikawo lembani mawu ena abwino. Mwachitsanzo, m’malo monena kuti “Zanditopetsa” muzinena kuti “Ndikukwanitsa kulera ndekha ana ndipo ndimapeza zinthu zofunikira.”—Afilipi 4:13.

Muzigwiritsa ntchito ndalama mwanzeru. Vuto lalikulu limene makolo ambiri amene akulera okha ana, makamaka amayi, amakumana nalo ndi lokhudza ndalama. Komabe, nthawi zina vutoli lingachepe ngati mutamagwiritsa ntchito ndalama mwanzeru. Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.” (Miyambo 22:3) Choncho kuti mupewe vuto losowa ndalama, muyenera kupanga bajeti ndiponso kuganizira mozama zinthu zoyenera kugula.

Yesani izi: Lembani bajeti. Mwezi uliwonse muzilemba zinthu zimene mwagula kuti mudziwe kumene ndalama zanu zikupita. Onani kuti ndi zinthu ziti zimene zikukuwonongerani ndalama. Kodi mumadalira kwambiri ngongole? Kodi mumagulira ana anu zinthu kuti asamadandaule za bambo kapena mayi awo amene munalekana nawo? Ngati ana anu ndi okulirapo, kambiranani za mmene mungachepetsere kuwononga ndalama. Zimenezi zingathandize ana anu kuti azisamala ndalama, ndipo mwina iwo angakuuzeninso zinthu zina zothandiza kuti musamawononge ndalama.

Musamakangane ndi mwamuna kapena mkazi wanu wakale. Ngati banja lanu linatha, yesetsani kuti musamauze ana anu zinthu zoipa zokhudza mkazi kapena mwamuna wanu wakale. Komanso si bwino kutuma ana anu kuti azifufuza zinthu zimene mkazi kapena mwamuna wanu wakale akuchita. * Ndi bwinonso kuti muzikambirana ndi mkazi kapena mwamuna wanu wakale mmene mungamalangizire ana anu komanso zinthu zina zokhudza moyo wawo. Muziyesetsa kuchita zinthu mwamtendere ndi mwamuna kapena mkazi wanu wakale. Baibulo limati: “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”—Aroma 12:18.

Yesani izi: Nthawi ina mukadzasemphana maganizo ndi mkazi kapena mwamuna wanu wakale, mudzakambirane naye ngati mmene mungachitire ndi mnzanu wa kuntchito. Mukakhala kuntchito mumayesetsa kuti muzigwirizana ndi munthu aliyense ngakhale amene mumaona kuti sachita zinthu zabwino. Muzichita chimodzimodzi ndi mkazi kapena mwamuna wanu wakale. N’zoona kuti nthawi zina mungasemphane maganizo ndi mnzanuyo koma zimenezi zisakuchititseni kuti muyambane.—Luka 12:58.

Khalani chitsanzo chabwino. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikufuna kuti ana anga akhale ndi makhalidwe otani? Kodi ineyo ndili ndi makhalidwe amenewa?’ Mwachitsanzo, kodi inuyo mumakhala mosangalala ngakhale kuti mukulera nokha ana? Kapena kodi mavuto amene mukukumana nawo amakuchititsani kusasangalala pamoyo wanu? Kodi nthawi zonse mumakhala wokhumudwa chifukwa cha zimene mkazi kapena mwamuna wanu wakale anakuchitirani? Kapena kodi mumalimba mtima ngakhale akuchitireni zinthu zopanda chilungamo? (Miyambo 15:18) Kunena zoona, nkhani zimenezi n’zovuta ndipo nthawi zina mungalephere kuzipirira. Komabe dziwani kuti mukamangodandaula ana anunso adzatengera zomwezo.

Yesani izi: Lembani makhalidwe atatu amene mukufuna kuti ana anu azidzasonyeza akadzakula. * Lembaninso zimene mungachite panopa kuti ana anuwo adzakhale ndi makhalidwe amenewo.

Muzidzisamalira. Makolo ambiri amene amalera okha ana amatanganidwa kwambiri, ndipo n’zosavuta kumangoda nkhawa kapena kusiya kudzisamalira. Yesetsani kuti zimenezi zisakuchitikireni. Kuzindikira ‘zosowa zanu zauzimu’ n’kofunika kwambiri. (Mateyo 5:3) Kumbukirani kuti ngati galimoto ilibe mafuta, siyenda mtunda wautali. Inunso zinthu sizingakuyendereni bwino ngati simukhala ndi nthawi yochita zinthu zauzimu.

Baibulo limanena kuti tiyenera kukhalanso ndi “mphindi yakuseka” ndi “mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:4) Dziwani kuti kupeza nthawi yosangalala n’kofunika chifukwa kumathandiza kuti mukhalenso ndi mphamvu.

Yesani izi: Kambiranani ndi anthu ena amene amalera okha ana kuti akuuzeni mmene amadzisamalirira. Pamene ‘mukutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti,” mungachite bwinonso kumakhala ndi nthawi yosangalala. (Afilipi 1:10) Lembani zinthu zosangalatsa zimene mungakonde kuchita ndi nthawi imene mungazichite.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Kodi Kutha kwa Banja Kumakhudza Bwanji Ana?” patsamba 18 mpaka 21 m’magazini ino.

^ ndime 11 Mungalembe makhalidwe monga “ulemu,” “kulolera,” ndi “kukhululuka,” amene afotokozedwa m’magazini ino patsamba 6 mpaka 8.