Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mphatso Zachifundo Zingathetse Mavuto Athu Onse?

Kodi Mphatso Zachifundo Zingathetse Mavuto Athu Onse?

Kodi Mphatso Zachifundo Zingathetse Mavuto Athu Onse?

MASIKU ano pali anthu ambiri a mtima wabwino amene akupereka mphatso zachifundo. Ngakhale kuti nkhani zambiri zimene zimafalitsidwa zimanena za masoka achilengedwe, umphawi, njala, matenda ndiponso kuwonongedwa kwa chilengedwe, timamvanso za anthu ambiri amene amapereka ndalama zokwana mamiliyoni kapena mabiliyoni kuti zithandize anthu. Nthawi zambiri anthu otchuka ndi amene amakonda kudziwitsa anthu za mavuto akuluakulu amene tili nawo. Palinso anthu ambiri omwe si olemera amene amapereka mphatso zachifundo. Komabe, kodi zimenezi zingathandize mpaka pati m’tsogolomu?

Anthu Opereka Mphatso Zachifundo Akuchuluka

M’mayiko ambiri anthu akupereka mphatso zachifundo. Buku lina linati: “Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 2000, m’mayiko ambiri anthu anapereka mphatso zachifundo zambiri kuposa kale lonse.” Poti anthu ambiri ayamba kulemera kwambiri, zikuoneka kuti anthu ambiri ayambanso kupereka mphatso zachifundo komanso mabungwe othandiza anthu osauka azilandira chuma chambiri chamasiye. Mpake kuti magazini ina inati, “n’kutheka kuti anthu opereka mphatso zachifundo ayamba kuchuluka kwambiri” panopo kuposa kale lonse.—The Economist.

Kulephera kwa maboma kuthetsa mavuto akuluakulu apadziko lonse n’kumene kukuchititsa zimenezi. Nthumwi ya UN yoona za matenda a Edzi mu Africa muno inati, anthu otchuka ambiri ayamba kuthandizapo pamavuto amatenda apadziko lonse chifukwa “atsogoleri andale alephereratu.” M’buku lake lina, Joel Fleishman anati, pankhani yothetsa mavuto okhudza zinthu monga umphawi, matenda, chilengedwe, maphunziro, ndiponso chilungamo, anthu olemera ndiwo makamaka “amaona kwambiri kulephera kwa maboma padziko lonse.” Pofunitsitsa kukonza zinthu, anthu olemera ena amagwiritsa ntchito njira zimene zinawathandiza kuti alemere.—The Foundation: A Great American Secret—How Private Wealth Is Changing the World.

Amathandiza Kwambiri

Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, anthu opereka mphatso zachifundo analinso ambiri ndithu. Zikhwaya monga Andrew Carnegie ndi John D. Rockefeller, anagwiritsa ntchito ndalama zawo pothandiza anthu ovutika. Zikhwayazi zinaona kuti ngakhale kuti mabungwe ambiri othandiza ovutika ankapereka chakudya kwa anthu ndiponso ankathandiza ana odwala, kwenikweni sankathetsa zimene zimayambitsa mavutowo. Atazindikira kuti pakufunika njira zabwino zothetsera mavutowa, iwo anakhazikitsa mabungwe othandiza kutukula miyoyo ya anthu ndiponso anapereka ndalama kumagulu amene cholinga chawo ndi kuthetsa zimene zimayambitsa mavutowo. Kuyambira nthawi imeneyo, mabungwe ambirimbiri akhazikitsidwa padziko lonse ndipo mabungwe oposa 50 oterewa ali ndi ndalama zoposa madola 1 biliyoni.

Palibe amene angatsutse zoti mabungwe amenewa athandiza kwambiri. Umboni wa zimenezi ndi kumangidwa kwa masukulu, malaibulale, zipatala, malo osungiramo nyama zam’tchire ndi nyumba zosungiramo zinthu zochititsa chidwi. Komanso ntchito zolimbikitsira ulimi kuti chakudya chisamasowe zathandiza kuti mayiko osauka akhale ndi chakudya chambiri. Ndalama zimene mabungwewa amapereka ku magulu ofufuza zamankhwala zathandiza kuti pakhale chithandizo chabwino cha mankhwala. Ndalamazi zathandizanso kuti matenda monga ntchofu atheretu m’madera ena.

Masiku ano, ambiri akuona kuti zinthu zisintha chifukwa mabungwewa akuyesetsa kwambiri kuthetsa mavuto apadziko lonse ndipo pali thandizo lambiri limene akupatsidwa. Mu 2006, Pulezidenti wina wakale wa dziko la United States anauza gulu lina lopereka mphatso zachifundo kuti: “Anthu ndiponso mabungwe opereka mphatso zachifundo adzathandiza kwambiri kuti moyo wa anthu ambiri usinthe.”

Komabe anthu ambiri akukayikira zimenezi. Katswiri wina pankhani zamankhwala padziko lonse, dzina lake Laurie Garrett, analemba kuti: “Chifukwa cha kuchuluka kwa ndalama, anthu ambiri akuganiza kuti matenda adzatheratu. Koma zimenezi sizoona.” Chifukwa chiyani akutero? Iye anati pali ndondomeko zina za boma komanso mabungwe zimene zimachedwetsa zinthu. Palinso katangale ndi vuto lolephera kuchita zinthu mogwirizana. Chifukwa chinanso n’chakuti anthu amaneneratu kuti ndalama zawo zithandize pa vuto limodzi lokha monga Edzi.

Garrett akuona kuti chifukwa chakuti anthu sakuchita zinthu mogwirizana, komanso ndalama “zimangothandiza pa matenda odziwika okha, osati pamoyo wa anthu onse, mphatso zachifundozi sizikonza kwenikweni zinthu, koma zimangowonjezera mavuto.”

Ndalama Zokha Sizokwanira

Kaya zolinga zikhale zotani, mphatso zachifundo sizingathetse mavuto onse. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chimodzi n’chakuti kuchuluka kwa ndalama ndiponso maphunziro sizingathetse mavuto monga dyera, udani, tsankho, kukondetsa dziko lanu, kusankhana mitundu komanso zikhulupiriro za zipembedzo zonyenga. Ngakhale kuti zinthu zimenezi zimawonjezera mavuto, si zimene zimayambitsa mavutowo. Baibulo limatchula chimene chinayambitsa mavutowa.

Ilo limati chinthu chimodzi ndicho kupanda ungwiro kumene tili nako chifukwa cha uchimo. (Aroma 3:23; 5:12) Chifukwa cha kupanda ungwiro, timakonda kuganiza ndiponso kuchita zinthu zoipa. Lemba la Genesis 8:21, limati: “Ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.” Chifukwa chotsatira mtima woipawu, anthu ambiri amachita zachiwerewere ndiponso amagwiritsira ntchito mankhwala osokoneza ubongo. Makhalidwe amenewa amachititsa kuti matenda osiyanasiyana monga Edzi, afale.—Aroma 1:26, 27.

Chinthu chinanso chimene chimachititsa kuti tizivutika n’chakuti anthufe sitingathe kudzilamulira bwinobwino. Lemba la Yeremiya 10:23, limati: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Mabungwe ambiri opereka mphatso zachifundo amachita ntchito yawo mosadalira boma chifukwa cha vuto limene tatchula kale lija, lakuti “atsogoleri andale alephereratu.” Baibulo limati anthu analengedwa kuti azilamuliridwa ndi Mlengi, osati kulamulirana okhaokha.—Yesaya 33:22.

Komanso Baibulo limalonjeza kuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu adzathetsa mavuto athu onse. Inde, Yehova wachitapo kale mbali zofunika kwambiri pankhaniyi.

Wopatsa Wamkulu

Palibe amene amakonda kwambiri anthu mofanana ndi Mlengi wathu. Lemba la Yohane 3:16 limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” Yehova anapereka mphatso yofunika kwambiri kuposa ndalama kuti anthufe timasuke ku uchimo ndi imfa. Iye anapereka Mwana wake wokondedwa monga “dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) Ponena za Yesu, mtumwi Petulo analemba kuti: “Iye ananyamula machimo athu m’thupi lake pa mtengo, kuti tilekane ndi machimo ndi kukhala amoyo m’chilungamo. Ndipo ‘mwa mabala ake munachiritsidwa.’”—1 Petulo 2:24.

Chinanso, Yehova wakonza njira yothetsera vuto la kusowa ulamuliro wabwino limene lilipo. Watero pokhazikitsa boma limene lidzalamulire dziko lonse. Boma limeneli ndilo Ufumu wa Mulungu womwe uli kumwamba ndipo udzathetsa kuipa konse padziko lapansi n’kubweretsa mtendere.—Salmo 37:10, 11; Danieli 2:44; 7:13, 14.

Popeza Mulungu adzathetsa zimene zimayambitsa mavuto athu onse, iye adzachita zimene munthu kapena magulu a anthu sangathe kuchita. N’chifukwa chake Mboni za Yehova sizikhazikitsa magulu opereka mphatso zachifundo. Koma motsatira Yesu Khristu, zimathera nthawi yawo ndi chuma chawo polalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.’—Mateyo 24:14; Luka 4:43.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 21]

“Mulungu Amakonda Wopereka Mokondwera”

Mboni za Yehova zimatsatira mfundo imeneyi, yomwe imapezeka pa 2 Akorinto 9:7. Iwo amagwiritsa ntchito nthawi yawo, mphamvu zawo ndiponso chuma chawo kuti athandize ena, potsatira langizo lakuti: “Tisakondane ndi mawu okha kapena ndi lilime lokha, koma mwa zochita ndi choonadi.”—1 Yohane 3:18.

Pakachitika zinthu monga masoka achilengedwe, Mboni zimapezerapo mwayi wothandiza anthu ovutika. Mwachitsanzo, kum’mwera kwa dziko la United States kutachitika mvula zamkuntho, (zotchedwa Katrina, Rita ndi Wilma) Mboni za Yehova zambiri zinadzipereka kupita kumadera okhudzidwawo kukathandiza anthu komanso kukakonza nyumba zowonongeka. Moyang’aniridwa ndi makomiti opereka chithandizo, anthu odziperekawo anakonza ndi kumanganso nyumba zopitirira 5,600 za Mboni za Yehova komanso Nyumba za Ufumu 90.

Mboni za Yehova sizipereka chachikhumi komanso sizipemphetsa ndalama m’njira ina iliyonse. Ndalama zonse zoyendetsera ntchito zawo zimakhala zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.—Mateyo 6:3, 4; 2 Akorinto 8:12.

[Chithunzi patsamba 19]

Ndalama sizingathetse zimene zinayambitsa kuti anthu azidwala komanso azivutika

[Mawu a Chithunzi]

© Chris de Bode/Panos Pictures