Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

ANANENA IZI NDANI?

Lembani mzere wolumikiza mawu ndi munthu amene anawalankhula.

Davide

Yesu

Solomo

Paulo

1. “Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.”

2. “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zimenezo.”

3. “Chikondi sichitha konse.”

4. “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.”

▪ Kambiranani: Kodi ndi mfundo ina imodzi iti imene mukudziwa yokhudza aliyense wa anthu a m’Baibulowa?

ZINACHITIKA LITI?

Tchulani anthu amene analemba mabuku a m’Baibulo amene ali m’munsiwa, ndipo lembani mzere wolumikiza buku ndi nthawi imene anamaliza kulilemba.

1450 B.C.E. 1090 B.C.E. 1078 B.C.E. 36 C.E. 56 C.E.

5. Yoswa

6. Rute

7. Aroma

NDINE NDANI?

8. Ndinalosera kuti Sisera adzaphedwa ndi mkazi.

NDINE NDANI?

9. Ine ndi mwamuna wanga tinaika moyo wathu pachiswe kuti tipulumutse Paulo.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo amene akusowapo.

Tsamba 6 Kodi munthu ayenera kuchitanji kuti akhale wotsatira wa Khristu? (Luka 9:․․․)

Tsamba 7-8 Kodi mtumwi Paulo anati n’chiyani chidzachitikire mpingo wachikhristu iye akachoka? (Machitidwe 20:․․․)

Tsamba 13 Kodi Satana wachita chiyani ndi maganizo a anthu ambiri? (2 Akorinto 4:․․․)

Tsamba 28 Kodi Baibulo limanenanji pankhani yogonana amuna kapena akazi okhaokha? (Aroma 1:․․․)

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani nokha zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

(Mayankho ali pa tsamba 20)

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Solomo.—Miyambo 9:10.

2. Yesu.—Luka 6:31.

3. Paulo.—1 Akorinto 13:8.

4. Davide.—Salmo 23:1.

5. Yoswa, 1450 B.C.E.

6. Samueli, 1090 B.C.E.

7. Paulo, 56 C.E.

8. Debora.—Oweruza 4:4, 9.

9. Purisika, kapena Purisikila.—Aroma 16:3, 4.