Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Kulankhulana pakati pa makolo ndi ana kukusokonezeka chifukwa cha zinthu monga ‘kuyatsa TV tsiku lonse, kusadyera pamodzi chakudya, ndiponso chifukwa choti zikuku zoyendetsera ana anazipanga m’njira yakuti anawo asamayang’anane ndi makolo.’ Zimenezi zikuchititsa kuti ana akayamba sukulu “azikhala amtima wapachala” chifukwa satha kufotokoza bwinobwino mmene akumvera mumtima mwawo.—Zachokera m’nyuzipepala ya THE INDEPENDENT, KU BRITAIN.

Ana 23 pa ana 100 alionse a ku Spain amakhala apathengo. Ku France, pa ana 100 aliwonse ana apathengo ndi 43, ku Denmark, ndi 45, ndipo ku Sweden, ndi ana 55.—Zachokera ku bungwe la INSTITUTO DE POLÍTICA FAMILIAR, KU SPAIN.

Munthu mmodzi pa anthu atatu alionse a ku Britain amagona nthawi yosakwana maola asanu usiku ulionse. Zimenezi zimachititsa kuti anthuwa “asamakhazikike maganizo, aziiwalaiwala, [ndiponso] azisinthasintha n’kumati pena kukhala osangalala pena kukhala okwiya.” Komanso, kusagona mokwanira kungachititse mosavuta zinthu monga “vuto lonenepa kwambiri, matenda a shuga, matenda ovutika maganizo, kutha kwa mabanja ndiponso ngozi zoopsa kwambiri za galimoto.”—Zachokera m’nyuzipepala ya THE INDEPENDENT, KU BRITAIN.

Kuchita Zachiwawa “Chifukwa Chongosowa Chochita”

“Achinyamata akumenya ndi kuchititsa manyazi anthu ambiri, ndipo achinyamatawo amajambula zithunzi za vidiyo pamene akuchita zimenezi pogwiritsa ntchito telefoni zam’manja,” inatero nyuzipepala ya ku Spain ya El País. Ena mwa anthuwo amafa chifukwa chomenyedwa modetsa nkhawa. Kodi n’chifukwa chiyani achinyamata akuchita zinthu zachiwawazi? “Sachita zachiwawazi pofuna kubera anthuwo, kapena podana nawo chifukwa cha fuko lawo, kapenanso chifukwa choti achinyamatawo ndi zigawenga ayi. Koma, n’zodabwitsa kuti iwo amachita zimenezi chifukwa chongosowa chochita,” inatero magazini ya XL. Ndipo Vicente Garrido, yemwe ndi katswiri wa zamaganizo okhudzana ndi zachiwawa anati: “Achinyamatawa nthawi zina amakhala ataledzera ndipo nthawi zina amakhala ali bwinobwino. Komabe, mfundo yaikulu n’njoti onsewo chikumbumtima chawo sichimawapweteka.”

Alibe Chidwi ndi Matenda a M’mayiko Otentha

Anthu ofufuza za mankhwala akunyalanyaza matenda ambiri amene n’ngofala m’mayiko otentha omwenso n’ngosauka. Chifukwa chiyani? “Chomvetsa chisoni n’chakuti . . . makampani opanga mankhwala sakufufuzanso mankhwala [atsopano],” anatero Michael Ferguson yemwe ndi katswiri wa sayansi pa yunivesite ya Dundee ku Scotland. Makampani opanga mankhwala sakuikirapo mtima pa ntchito yofufuzayi mwa kupereka ndalama zogwirira ntchitoyi ndipo ichi n’chifukwa choti akudziwa kuti sangapeze phindu. M’malo mwake, makampaniwa amapanga mankhwala omwe angagulitse pa mtengo wokwera kwambiri a matenda monga matenda aubongo a Alzheimer’s, vuto la kunenepa kwambiri, ndi kusabereka. Padakali pano, monga mmene magazini ya New Scientist inanenera, pafupifupi “anthu 1 miliyoni padziko lonse amamwalira chaka chilichonse chifukwa cha malungo, ndipo mankhwala abwino ndiponso othandizadi a matendawa sanapezekebe.”

“Timakasitomala” Tating’ono

Malinga ndi zomwe yunivesite ya La Sapienza ku Rome m’dziko la Italy inanena, ana ang’onoang’ono ngakhale azaka zitatu, angathe kusiyanitsa katundu wopangidwa ndi makampani osiyanasiyana, ndipo akafika zaka 8, amakhala “makasitomala.” Anawa amatengeka kwambiri ndi malonda amene amawaona akutsatsidwa pa TV, ndipo zimenezi zimawachititsa kuti ayambe “kulamula” makolo awo kuti aziwagulira zinthu zinazake, inatero nyuzipepala ya La Repubblica. Ndipo nyuzipepalayo inapitiriza kuti, ‘kuopsa kwake n’kwakuti anawo amayamba kukhulupirira zabodza, zakuti chilichonse chomwe chikugulitsidwa n’chofunika kwambiri.’

Chidole “Chokhala ndi Pakati”

Kwa zaka zambiri, madokotala ndi anthu ena osamalira azimayi a pakati akhala akuphunzirira ntchito yawo pa odwala enieni. Koma tsopano, malinga ndi lipoti la bungwe la Associated Press, iwo “akuphunzirira ntchito yawo pa chidole chokhala ndi pakati” chomwe akuchitcha Noelle. Chidole “chapakatichi” amatha kuchichuna kuti mtima wake uzigunda zenizeni, njira yake yoberekera izikula, chizikhala ndi mavuto angapo obereka, ndiponso kuti chizitha kubereka mwana mofulumirirapo kapena mochedwerapo. “Mwana” amene Noelle amaberekayo akhoza kukhala wathanzi, wooneka bwinobwino, kapena wooneka ngati akudwala chifukwa chosowa mpweya wabwino m’thupi. Koma kodi n’chifukwa chiyani akugwiritsa ntchito chidolechi pophunzitsa? Lipotilo linati: “Ndibwino kulakwitsira pa chidole, ngakhale kuti n’cha ndalama zokwana madola 20,000, kusiyana ndi kulakwitsira pa munthu weniweni.”