Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Satana Ndani? Kodi Alikodi?

Kodi Satana Ndani? Kodi Alikodi?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Satana Ndani? Kodi Alikodi?

AKATSWI ena amakono a zamaphunziro amanena kuti Satana si munthu woti alikodi ayi. Iwo amati ndi munthu amene anthu anangomulenga m’maganizo mwawo. Nkhani imeneyitu siinayambe lero. Wolemba ndakatulo wina wa m’zaka za m’ma 1800, dzina lake Charles-Pierre Baudelaire, anati: “Chinyengo chachikulu kwambiri cha Mdyerekezi ndicho choyesa kuchititsa anthufe kukhulupirira kuti iyeyo kulibe.”

Kodi Satana alikodi? Ngati alikodi, kodi anachokera kuti? Kodi iyeyo ndiye akuchititsa mavutowa padziko pano? Kodi mungatani kuti asakusocheretseni?

Zimene Baibulo Limanena

Baibulo limanena kuti Satana alikodi ndipo ndi munthu wauzimu wosaoneka. (Yobu 1:6) Limatiuza za nkhanza zake zoopsa, kuuma mtima kwake komanso za zochita zake zina zoipa. (Yobu 1:13-19; 2:7, 8; 2 Timoteyo 2:26) Limatchulanso makambitsirano a pakati pa iyeyu ndi Mulungu komanso ndi Yesu.—Yobu 1:7-12; Mateyo 4:1-11.

Kodi zinatani kuti iyeyu afike pokhala woipa chonchi? Kalekale munthu asanalengedwe, Mulungu analenga Mwana wake “woyamba kubadwa,” amene patsogolo pake anadzadziwika ndi dzina loti Yesu. (Akolose 1:15) Patapita nthawi, ‘ana a Mulungu’ ena, otchedwa angelo, analengedwa. (Yobu 38:4-7) Onse anali angwiro ndi olungama. Komano mmodzi wa angelo amenewa anadzakhala Satana.

Satana si dzina limene anapatsidwa polengedwa ayi. Ili ndi dzina lomufotokoza, lomwe limatanthauza kuti “Mdani, kapenanso Wotsutsa.” Anadzatchedwa dzina loti Satana chifukwa choti anasankha moyo wotsutsana ndi Mulungu.

Mtima wodzikuza komanso wolimbana ndi Mulungu unam’kulira mngelo ameneyu. Iye ankafuna kuti ena azimulambira. Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu, Yesu, ali pa dziko lapansi, Satana anayesa kum’chititsa ‘kum’lambirako’ iyeyo.—Mateyo 4:9.

Satana “sanakhazikike m’choonadi.” (Yohane 8:44) Anasonyeza ngati kuti Mulungu ndi wabodza pamene kwenikweni wabodza anali iyeyo. Anauza Hava kuti angathe kukhala ngati Mulungu, pamene kwenikweni iyeyo ndiye ankafuna kukhala ngati Mulungu. Ndipo kudzera m’njira zake zachinyengo, iye anakwaniritsa chilakolako cha mtima wake wadyerachi. Kwa Hava, anadzichititsa kuoneka ngati wamkulu kuposa Mulungu. Pomvera Satana, Hava anavomereza kuti Satanayo ndiye mulungu wake.—Genesis 3:1-7.

Polimbikitsa ena kuukira Mulungu, mngelo amene poyamba anali wokhulupirikayu anadzipanga kukhala Satana, mdani wa Mulungu ndi anthu. Mawu akuti “Mdyerekezi,” omwe amatanthauza kuti “Wamiseche,” anakhalanso mbali ya dzina la woipayu. Woyambitsa machimo ameneyu anafika pochititsa kuti angelo ena am’tsatire posiya kumvera Mulungu. (Genesis 6:1, 2; 1 Petulo 3:19, 20) Zimene anachita angelo amenewa sizinathandize anthu. Chifukwa choti iwowa anatsanzira kudzikonda kwa Satana, ‘dziko lapansi linadzala ndi chiwawa.’—Genesis 6:11; Mateyo 12:24.

Kodi Satana Amasocheretsa Anthu Kumlingo Wotani?

Chigawenga chingathe kuyeretsa malo onse amene chachitirapo zauchigawenga pofuna kuti pasapezeke umboni uliwonse wochigwiritsa. Koma apolisi akafika pa malopo, amadziwa ndithu kuti ngati pachitika zauchigawenga ndiye kuti pali chigawenga basi. Satana, yemwe ndi woyamba kukhala “wopha anthu” amayesa kudzibisa kuti asadziwike. (Yohane 8:44; Aheberi 2:14) Polankhula ndi Hava, Satana anadzibisa kuseli kwa njoka. Masiku anonso iyeyu akuyesabe kubisala. “Wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira” kuti asadziwe kuti iyeyu akusocheretsa kwambiri anthu.—2 Akorinto 4:4.

Komano Yesu anasonyeza kuti Satana ndiye chigawenga chimene chinachititsa dzikoli kuipa chonchi. Yesu anatcha Satana kuti “wolamulira wa dzikoli.” (Yohane 12:31; 16:11) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Satana “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” pogwiritsira ntchito mwaluso “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pamoyo wake.” (1 Yohane 2:16; Chivumbulutso 12:9) Iyeyu ndi amene anthu ambiri amam’mvera.

Monga anachitiranso Hava, anthu amene amamvera Satana, kwenikweni amasankha iyeyo kukhala mulungu wawo. Motero, Satana ndiye “mulungu wa dongosolo lino la zinthu.” (2 Akorinto 4:4) Ulamuliro wake wabweretsa zinthu monga chinyengo, mabodza, nkhondo, kuzunza anthu, kuwononga zinthu, kuswa malamulo, umbombo ndi ziphuphu.

Mmene Mungapewere Kusocheretsedwa ndi Satana

Baibulo limachenjeza kuti: “Sungani maganizo anu, khalani maso.” Chifukwa chiyani? Chifukwa choti “mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.” (1 Petulo 5:8) Ngakhale kuti mfundo ya m’lembali n’njofunika kuiganizira mosamala, n’zolimbitsa mtima kudziwa kuti anthu amene ‘Satana amawachenjerera’ ndi okhawo amene sasunga maganizo awo, amene sakhala maso.—2 Akorinto 2:11.

M’pofunika kwambiri kuti tizindikire kuti Satana alikodi ndipo kuti tilole Mulungu ‘kutilimbitsa’ ndi ‘kutipatsa mphamvu.’ Potero tingathe ‘kulimbana naye’ n’kukhala ku mbali ya Mulungu.—1 Petulo 5:9, 10.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi Satana anachokera kuti?—Yobu 38:4-7; Yohane 8:44.

▪ Kodi Satana amasocheretsa dzikoli kumlingo wotani?—Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9.

▪ Kodi tingatani kuti tidziteteze ku njira zoipa zimene Satana amasocheretsera anthu?—1 Petulo 5:8-10.

[Zithunzi patsamba 12]

Kodi Satana ndiye akuchititsa mavutowa padziko pano?