Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Masoka Onse Adzatha Posachedwapa

Masoka Onse Adzatha Posachedwapa

Masoka Onse Adzatha Posachedwapa

“Ana inu ndi zidzukulu inu, tamverani! . . . Posachedwapa phiri ili liyaka. Koma zimenezi zisanachitike pamveka kugunda mkokomo ndi mabingu ndi zivomezi. Patuluka utsi ndi malawi a moto, pachita ziphaliwali, ndiponso pawomba chimphepo chamkokomo. Thawirani kutali kwambiri . . . Ngati phirili mumaliderera, ndiponso ngati katundu ali wofunika kwambiri kwa inu kuposa moyo, likulangani chifukwa cha kusasamala kwanuko ndi dyera lanu. Musadere nkhawa za katundu wanu ndi nyumba yanu, koma thawani osazengereza.”

CHENJEZO limenelo, lochokera m’buku lotchedwa Earth Shock, lolembedwa ndi Andrew Robinson, linalembedwa pa chipilala cha chikumbutso m’tawuni ya Portici, yomwe ili m’munsi mwa phiri la Vesuvius ku Italy, phirilo litangophulika kumene mu 1631. Kuphulika kwa phirilo kunapha anthu opitirira 4,000. Robinson anati: “N’zochititsa chidwi kuti kuphulika kwa mu 1631 kumeneku . . . n’kumene kunatchukitsa phiri la Vesuvius.” Chifukwa chiyani? Chifukwa choti pamene ankamanganso tawuni ya Portici m’pamene anatulukira mizinda ya Herculaneum ndi Pompeii. Mizinda iwiriyi inafafanizika pamene phiri la Vesuvius linaphulika mu 79 C.E.

Pliny Wamng’ono, Mroma amene anapulumuka tsoka limenelo ndipo kenaka anadzakhala kazembe, analemba za kunjenjemera kwachilendo kwa phirilo komwe kunawachenjeza. Iye, mayi ake, ndi ena anamvera chenjezolo ndipo anapulumuka.

Chizindikiro Chotichenjeza Masiku Ano

Masiku ano tikuyandikira kwambiri mapeto a dongosolo la zachuma, zachikhalidwe, ndi zandale a dzikoli. Tikudziwa bwanji zimenezo? Chifukwa choti Yesu Kristu ananeneratu zinthu zosiyanasiyana zomwe zidzachitike padzikoli zosonyeza kuti tsiku la Mulungu lachiweruzo lili pafupi. Mofanana ndi phiri lomwe limabangula, limatuluka utsi, ndiponso limatulutsa phulusa, chizindikiro chokhala ndi mbali zosiyanasiyana chimenecho chimaphatikizapo nkhondo zikuluzikulu, zivomezi, njala, ndi matenda. Ndipo zinthu zonsezi zavutitsa dzikoli kwambiri kuposa kale lonse kuchokera m’chaka cha 1914.—Mateyu 24:3-8; Luka 21:10, 11; Chivumbulutso 6:1-8.

Koma chizindikiro chochenjeza cha Yesu chimaphatikizaponso uthenga wa chiyembekezo. Iye anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Taonani kuti Yesu anati uthenga wa Ufumuwo ndi ‘uthenga wabwino.’ Ndi uthenga wabwinodi chifukwa Ufumu wa Mulungu, boma lakumwamba lolamulidwa ndi Kristu Yesu, udzakonzanso zinthu zonse zomwe anthu awononga. Kuwonjezera apo, udzathetsa masoka achilengedwe.—Luka 4:43; Chivumbulutso 21:3, 4.

Indedi, pamene Yesu anali munthu padziko lapansi, anasonyeza mphamvu imene ali nayo pachilengedwe potontholetsa namondwe yemwe akanatha kupha anthu. Podabwa, ophunzira ake anafunsa mwamantha kuti: “Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye?” (Luka 8:22-25) Masiku ano, Yesu si munthu chabe, koma ndi mzimu wamphamvu. Choncho sadzavutika n’komwe kulamulira zinthu zachilengedwe kuti zisavulaze anthu ake.—Salmo 2:6-9; Chivumbulutso 11:15.

Ena angaone ngati zonsezi n’kungolakalaka chabe. Koma kumbukirani kuti ulosi wa m’Baibulo, mosiyana ndi malonjezo kapena maulosi a anthu, wonse umakwaniritsidwa. Ulosiwu ukuphatikizapo maulosi amene taona akukwaniritsidwa kuyambira mu 1914. (Yesaya 46:10; 55:10, 11) Indedi, n’zotsimikizika kuti m’tsogolo mwa dziko lapansi mudzakhala mwamtendere. Nafenso m’tsogolo mwathu mungakhale motsimikizika ngati tikhulupirira Mawu a Mulungu n’kumvera chenjezo lake lachikondi la zinthu zazikulu zomwe zatsala pang’ono kuchitika padziko pano.—Mateyu 24:42, 44; Yohane 17:3.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

KODI PALI CHIYEMBEKEZO CHOTANI CHA OKONDEDWA ATHU AMENE ANAMWALIRA?

MUNTHU amene tinali kumukonda akamwalira, tikhoza kudzazidwa ndi chisoni. Baibulo limatiuza kuti Yesu analira, Lazaro, yemwe anali mnzake wapamtima, atamwalira. Koma patangodutsa kanthawi kochepa, Yesu anachita chozizwitsa chochititsa chidwi kwambiri. Anaukitsa Lazaro kuti akhalenso ndi moyo. (Yohane 11:32-44) Pochita zimenezo, iye anapatsa anthu onse maziko okhulupirira lonjezo lochititsa chidwi limene ananena m’mbuyomo mu utumiki wake. Iye analonjeza kuti: “Ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Yesu], nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Tikufuna kuti chiyembekezo chabwino kwambiri choti anthu adzauka n’kukhala ndi moyo padziko lapansi chitonthoze anthu onse amene okondedwa awo anamwalira.—Machitidwe 24:15.

[Zithunzi patsamba 26]

Kodi mukumvera chenjezo loti dzikoli lili m’masiku ake otsiriza?

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

USGS, David A. Johnston, Cascades Volcano Observatory