Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Sierra Leone: Munthu wina akulozera Mlongo Crystal njira

NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Africa

Africa
  • MAYIKO 58

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 1,109,511,431

  • OFALITSA 1,538,897

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 4,089,110

Anapemphera Kuti Akumane ndi Munthu Amene Ali ndi Vuto Losamva

Mlongo Crystal akuchita umishonale ku Sierra Leone ndipo ali mumpingo wa Chinenero Chamanja. M’mawa wa tsiku lina anapemphera kuti apeze munthu amene ali ndi vuto losamva woti amulalikire. Ndiyeno pamene ankapita ku ulendo wobwereza anadutsa njira ina, osati yomwe ankadutsa masiku onse. Kenako anafunsa anthu ngati akudziwa munthu aliyense amene ali ndi vutoli ndipo anthuwo anamuperekeza kunyumba ina. Kumeneko anapeza mtsikana wansangala yemwe anamvetsera uthenga wa m’Baibulo. Ataitanira mtsikanayu kumisonkhano ya Chinenero Chamanja anavomera. Anthu ena anafunsa mlongoyu ngati angakonde kukumana ndi munthu winanso yemwe ali ndi vutoli. Atavomera anamuperekezanso kwa munthu amene ankafuna kuphunzira choonadi. Ngakhale kuti mlongoyu anali atayenda m’derali kangapo konse, anali asanakumanepo ndi anthu awiriwa. Iye akuona kuti Yehova ndi amene anamuthandiza kuti apeze anthuwa.

“Nkhani Ija Amakambira Ineyo”

Tsiku lina M’bale Emmanuel, yemwe amakhala ku Liberia anali pagalimoto yake ndipo ankapita ku Nyumba ya Ufumu kukasonkhana. Kenako anaona mnyamata wina wovala bwino ataima m’mbali mwa msewu koma ankaoneka wankhawa kwambiri. M’baleyu anaima kuti aone ngati angamuthandize. Mnyamatayo ananena kuti dzina lake ndi Moses ndipo ndalama zake zonse zinali zitabedwa chadzulo lake usiku. Pa nthawiyi n’kuti akuganiza zodzipha. M’bale Emmanuel anamvetsera pamene mnyamatayu ankalankhula ndipo kenako anamuuza kuti: “Bwanji tipitire limodzi ku Nyumba ya Ufumu?” Moses anavomera ndipo zimene anamva kumeneko zinamukhudza kwambiri mpaka analira. Iye anati: “Nkhani ija amakambira ineyo. Ndaona kuti a Mboni ndi osiyana ndi anthu ena.” Misonkhano itatha Moses anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndipo panopa amasonkhana nthawi zonse.

“Ine Si Wachikunja”

Mtsikana wina dzina lake Aminata ali ndi zaka 15 ndipo amakhala ku Guinea-Bissau. Ali ndi zaka 13, aphunzitsi ake anauza ana onse kuti ajambule zigoba zimene anthu amavala pochita chikondwerero chinachake. Koma Aminata anajambula chithunzi chokhala ndi anthu komanso maluwa ndipo analembapo kuti “Paradaiso.” Aphunzitsi ake atatolera mapepala a ana onse, anauza Aminata kuti zimene wajambula sizikugwirizana ndi zimene anauzidwa. Choncho anamuuza kuti walephera. Ataweruka, Aminata anapita kwa aphunzitsi ake n’kuwafunsa kuti: “Kodi ndi ndani amene amachita chikondwerero chimenechi?”

Aphunzitsiwo anayankha kuti: “Anthu achikunja.”

Guinea-Bissau: Aminata akujambula chithunzi cha “Paradaiso”

Ndiyeno Aminata anati: “Ine si wachikunja, choncho sindipanga nawo chikondwerero chimenechi. Ndimakhulupirira kuti Mulungu adzakonza dzikoli n’kukhala Paradaiso n’chifukwa chake ndinajambula chithunzi chimene chija.” Aphunzitsiwo atamva zimenezi anamuuza kuti amupatsa mwayi woti ayankhe mafunso pochita kulemba. Aminata atayankha mafunsowo, anakhoza 18 pa 20.

Anthu Ambiri Anabwera ku Chikumbutso

M’mudzi wina wa ku Malawi muli kagulu kakutali ka ofalitsa 7. Ofalitsawa amachita misonkhano yawo pamalo omangidwa ndi udzu komanso mphasa. Atalimbikitsidwa ndi woyang’anira dera wawo, ofalitsawo anachita khama kwambiri kuitanira anthu ku Chikumbutso. Pochita mwambowu anagwiritsa ntchito nyali zagalasi. M’bale amene anakamba nkhani ankachita kulephera kusuntha chifukwa pamalowo panadzaza anthu. Ofalitsa anasangalala kwambiri atamva kuti pamwambowo panasonkhana anthu okwana 120.

Malawi: Pa Chikumbutso panasonkhana anthu okwana 120

Kabuku Kanathandiza Kuti Banja Liyambe Kuyenda Bwino

Nthawi zambiri zotsatira za ulaliki wa timashelefu tamatayala sizioneka nthawi yomweyo. Mwachitsanzo, pamene ofalitsa ena ankachita ulalikiwu mumzinda wa Lomé, womwe ndi likulu la dziko la Togo, mayi wina anabwera n’kutenga kabuku kakuti, Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala. Ofalitsawo anakambirana mwachidule ndi mayiyo lemba la Aefeso 5:3 ndipo kenako anapatsana manambala a foni. Patatha milungu iwiri, mayiyo anaimbira foni ofalitsawo n’kunena kuti: “Poyamba sindinkagwirizana kwenikweni ndi a Mboni za Yehova. Komabe kabuku kaja ndinakawerenga ndipo ndi kabwino kwambiri. Kandithandiza kale kuthetsa mavuto ena a m’banja langa komanso ndathandiza mabanja awiri. Ndikuona kuti ndinali ndi maganizo olakwika okhudza Mboni za Yehova. Ndikupempha kuti muzibwera kudzandiphunzitsa Baibulo.” Panopa mayiyo komanso banja limodzi pa mabanja amene anawathandiza aja, akuphunzira Baibulo.

Munthu Wina Anamasulira Kabuku

Ku Ghana kuli katauni kena kotchedwa Ankasie. M’tauniyi anthu amakonda kuyala malonda awo m’mbali mwa msewu. Lolemba lililonse ofalitsa amaika kashelefu kamatayala mumsewuwu. Tsiku lina M’bale Samuel, yemwe ankachita ulalikiwu, analalikira bambo ena dzina lawo a Enoch. Kenako anawagawira kabuku kakuti, Mverani Mulungu. Bamboyu anafunsa m’baleyu ngati anali ndi mabuku a m’Chikusaala.

Ghana: A Enoch anamasulira kabuku m’Chikusaala

M’bale Samuel anayankha kuti: “Pepani, tilibe. Koma tili ndi timabuku tachifulafula.” Chinenero chimenechi ndi chofananako ndi Chikusaala. Kenako a Enoch akupita kumudzi kwawo, anapempha mabuku ena kuti akagawire achibale awo.

A Enoch atabwereranso ku Ankasie, anapatsa M’bale Samuel mapepala. A Enoch anali atamasulira kabuku ka Mverani Mulungu m’Chikusaala. Panopa amasonkhana komanso akuphunzira Baibulo.