Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GEORGIA

Anakumbukira Mlengi Wawo Wamkulu

Anakumbukira Mlengi Wawo Wamkulu

Anthu ambiri amene tawatchula masamba apitawa ndi achinyamata omwe ‘anakumbukira mlengi wawo wamkulu adakali achinyamata.’ (Mlal. 12:1) Ku Georgia kuli apainiya 3,197 ndipo mpainiya mmodzi pa apainiya atatu alionse ali ndi zaka zosapitirira 25. N’chifukwa chiyani m’dzikoli muli apainiya achinyamata ochuluka chonchi?

Pali zifukwa zingapo zimene zikuchititsa zimenezi. Chimodzi mwa zimenezi ndi zimene mabanja ambiri a m’dzikoli la Georgia amachita. Mabanja ambiri amakonda kuchitira zinthu limodzi ndipo amagwirizana kwambiri. M’bale Konstantine, yemwe anathandiza ana ake 5 kuti azikonda Yehova, anati: “Mfundo imene inandithandiza kuti ndiphunzire choonadi inali yoti Yehova ndi Atate wathu wachikondi. Ndiye nditakwatira n’kukhala ndi ana, cholinga changa chinali choti ndizitsanzira Yehova kuti ana anga azimasuka nane.”

 M’bale Malkhazi ndi mkazi wake, omwe ali ndi ana atatu, amayesetsa kuti azigwirizana kwambiri ndi ana awo. M’bale Malkhazi anati: “Nthawi zina timauza ana athu kuti aganizire makhalidwe abwino amene makolo awofe komanso abale awo ena ali nawo. Kenako timawauza kuti adzafotokoze pa kulambira kwa pabanja. Zimenezi zawathandiza kuti aziona zabwino zimene anthu ena amachita, n’kumawayamikira.”

“Panopa M’pamene Ndikusangalala Kwambiri”

Akulu athandizanso kwambiri kuti ana a m’dzikoli azikonda Yehova. Mwachitsanzo, amapereka ntchito zina komanso nkhani kwa achinyamata kuyambira ali aang’ono. Nestori, yemwe anabatizidwa ali ndi zaka 11 zokha, anati: “Akulu ankandipatsa nkhani kuyambira ndili wamng’ono. Zimenezi zinachititsa kuti ndiziona kuti amandiganizira.”

Abale ndi alongo a chitsanzo chabwino athandizanso kwambiri kuti achinyamata azichita bwino. Koba, yemwe ndi mkulu wake wa Nestori, anati: “Abale anga ena ankachita bwino kwambiri, koma ineyo ndinali wosokonekera. Ndimakumbukira kuti mkulu wina wachinyamata, yemwe anali wachitsanzo chabwino, anandithandiza zedi. Ankayesetsa  kundimvetsera ndikamayankhula ndipo sankaona kuti ndine wokanika. Ndimaona kuti anandithandiza kuti ndibwerere kwa Yehova.”

Panopa Nestori, Koba komanso mchemwali wawo Mari, amatumikira kudera lina lakutali. Koba anati, “Panopa m’pamene ndikusangalala kwambiri.”

“Ana Anga Akuyendabe M’choonadi”

Nayonso ofesi ya nthambi ya m’dzikoli imathandiza kuti achinyamata azilimbikira powapatsa ntchito zosiyanasiyana. M’bale wina yemwe ali m’Komiti ya Nthambi anati: “Timadyadira kwambiri achinyamata athu ndipo timayesetsa kuwathandiza kuti akwaniritse zolinga zawo zauzimu.”

Abale ndi alongo ku Tbilisi akugwira ntchito yomanga Nyumba ya Msonkhano limodzi ndi abale ndi alongo ochokera m’mayiko ena

Achinyamatawa akamagwira ntchito komanso kucheza ndi abale ndi alongo achikulire, zimawathandiza kuti azikonda kwambiri Yehova. M’bale Mamuka anagwirapo ntchito ndi abale ochokera m’mayiko ena pamene ankamanga Nyumba ya Msonkhano ku Tbilisi. Iye anati: “Ndinaphunzira zambiri pamene ndinkagwira ntchito limodzi ndi abale ndi alongo ochokera m’mayiko ena. Abalewa anandithandiza kuti ndizigwira ntchito mwaluso komanso kuti ndizikonda kwambiri Yehova.”

Mwachidule, taona kuti achinyamata ambiri a m’dziko la Georgia amakonda kwambiri Yehova chifukwa mabanja awo amakhala ogwirizana, akulu amawalimbikitsa komanso pali abale ndi alongo ambiri amene amawapatsa chitsanzo chabwino. N’zosakayikitsa kuti makolo a achinyamata amene akuchita bwino m’dziko la Georgia, amanena mawu ofanana ndi amene mtumwi Yohane ananena. Mtumwiyu anati, “Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.”3 Yoh. 4.

Ntchito Yomasulira Mabuku Inayamba Kuyenda Bwino Kwambiri

M’chaka cha 2013, Bungwe Lolamulira linapempha abale onse a m’Makomiti a Nthambi kuti afufuze ngati pangafunike kuti mabuku athu azimasuliridwanso m’zinenero zina  za m’dziko lawo. Cholinga chawo chinali choti anthu ambiri amve uthenga wabwino.

Zimenezi zitangochitika, abale a ku ofesi ya nthambi m’dziko la Georgia anaganiza zoyamba kumasulira mabuku athu m’Chisivani ndi Chimingirelia, zinenero zomwe ena amaona kuti ndi zofanana kwambiri ndi Chijojiya.

Apainiya odzipereka omwe amalalikira m’dera lomwe anthu ake amayankhula Chisivani, anati: “Anthu ambiri amene amayankhula chinenerochi amakonda kulambira Mulungu komanso amalemekeza Baibulo. Mabuku athu atayamba kumasuliridwa m’chinenerochi, anthu ambiri ankawakonda kwambiri chifukwa anali a chinenero chawo.”

Abale ndi alongo omwe amayankhula Chimingirelia anasangalala kwambiri pamene anayamba kuchita misonkhano m’chinenero chawo. M’bale Giga, yemwe ndi mpainiya wachinyamata, anati: “Panopa sindivutikanso kupereka  ndemanga pamisonkhano. Sindifunika kuchita kumasulira m’chinenero china ndikamafuna kuyankha pamisonkhano.”

M’bale Zuri ndi mkulu mumpingo wachimingirelia mumzinda wa Tkaia, ndipo anati: “Pa moyo wanga ndakumana ndi zinthu zambiri zosangalatsa komanso zomvetsa chisoni, koma sindinayambe ndalirapo. Koma tsiku lina tikuimba nyimbo koyamba m’Chimingirelia, abale ndi alongo ambiri anagwetsa misozi. Ndipo nanenso, ngakhale kuti ndine wouma m’maso, ndinalephera kupirira moti ndinalira.”

Zinthu Zapadera Zimene Zachitika Posachedwapa

Loweruka pa 6 April, 2013, m’dziko la Georgia munachitika chinthu chosaiwalika. Pa tsikuli, M’bale David Splane yemwe ali m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani  yopatulira Nyumba ya Msonkhano, nyumba zina zomwe kuzichitikira sukulu zophunzitsa Baibulo komanso mbali ya ofesi ya nthambi yomwe inawonjezeredwa. Pa nthawiyi, abale ndi alongo a m’dzikoli analandira alendo okwana 338 m’nyumba zawo. Alendowa anali ochokera m’mayiko 24.

Tsiku lotsatira, M’bale Splane anakamba nkhani yapadera ndipo mipingo ina ya m’dzikoli inamvetsera nkhaniyi kudzera pa intaneti. Anthu okwana 15,200, anamvetsera nkhaniyi ndipo umenewu unali msonkhano waukulu kwambiri kuchitika m’dzikoli. Abale analimbikitsana kwambiri ndipo anasangalala kucheza ndi abale ndi alongo awo. M’bale wina wachinyamata anati: “Zimene zachitika pamsonkhanowu zandithandiza kudziwa mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano.”

Mwambo wopatulira ofesi ya nthambi ku Tbilisi, mu 2013

Nayonso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja, yomwe panopa timati Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, yathandiza kwambiri abale ndi alongo a ku Georgia. Kungochokera mu 2013, abale ndi alongo oposa 200 anamaliza maphunziro awo. Abale ndi alongowa akuyamikira kwambiri ndipo akutumikira modzipereka m’madera amene kukufunika ofalitsa ambiri.

“Ndikuyesetsa Kuti Ndikapeze Zakutsogolo”

Abale ndi alongo a ku Georgia omwe anagwira ntchito mwakhama m’mbuyomu, anathandiza kwambiri kuti uthenga wabwino ufalikire m’dzikoli. Yehova anadalitsa kwambiri khama, chikondi chawo komanso mtima wawo wodzipereka pothandiza ena.

Panopa m’dziko la Georgia muli ofalitsa oposa 18,000. Abale ndi alongo amenewa akuyesetsa kuthandiza ena ngati mmene abale ndi alongo awo m’mbuyomo ankachitira. Akuthandizanso anthu a mitima yabwino kuti adziwe kuti Mawu a Mulungu ndi amphamvu ndipo amasintha moyo wa munthu.Afil. 3:13; 4:13.

Abale a m’Komiti ya Nthambi ya m’dziko la Georgia: Wayne Tomchuk, Levani Kopaliani, Joni Shalamberidze ndi Michael E. Jones