Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mpukutu wa m’zaka za m’ma 1300 C.E., wa mabuku a Uthenga Wabwino m’Chijojiya

 GEORGIA | 1924-1990

Baibulo la M’Chijojiya

Baibulo la M’Chijojiya

CHIJOJIYA ndi chimodzi mwa zinenero zoyambirira zomwe Baibulo linamasuliridwa. Zina mwa zinenerozi zinali Chiameniya, Chikoputiki, Chilatini ndi Chisiriya. Zinthu za m’Chijojiya monga mipukutu yakale kwambiri ya mabuku a Uthenga Wabwino, makalata a Paulo komanso buku la Masalimo zinamasuliridwa cha m’ma 450 C.E. kapena nthawi imeneyi isanafike. Zaka zimenezi zitadutsa, anthu anapitirizabe kumasulira komanso kukopera Baibulo lachijojiya ndipo zimenezi zinathandiza kuti pakhale Mabaibulo angapo a m’Chijojiya. *

Zimene olemba mabuku a ku Georgia ankalemba komanso mfundo zina zimene anthu amayendera zimapezeka m’Baibulo. Mwachitsanzo, nkhani yomvetsa chisoni ya Mfumukazi Shushanik, yomwe inalembedwa m’zaka za m’ma 400 C.E., ili ndi mawu ena omwe amapezeka m’Baibulo. Wolemba ndakatulo wina dzina lake Shota Rustaveli analemba ndakatulo yake m’chaka cha 1220 (ya mutu wakuti Vepkhvistqaosani) ndipo m’ndakatuloyi anatchula mfundo zina za makhalidwe abwino zomwe Akhristu amatsatira. Analemba nkhani zokhudza kukhala bwino ndi anthu ena, kukhala woolowa manja komanso kukonda anthu amene sukuwadziwa. Makhalidwe amenewa ndi amene anthu ambiri a ku Georgia amatsatira mpaka pano.

^ ndime 3 Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Chuma Chomwe Chinabisika kwa Zaka Zambiri,” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 2013.