Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Mapulogalamu a pa JW Broadcasting ‘Ndi Othandiza Komanso Olimbikitsa Kwambiri’

Mapulogalamu a pa JW Broadcasting ‘Ndi Othandiza Komanso Olimbikitsa Kwambiri’

M’CHAKA cha 2014, panakhazikitsidwa TV ya pa intaneti yotchedwa JW Broadcasting. Pa TV imeneyi pamakhala mapulogalamu omwe akuthandiza komanso kulimbikitsa anthu ambiri padziko lonse. Panopa TV imeneyi ikupezeka m’zinenero zoposa 90. Mwachitsanzo, ikupezeka m’Chiewe, Chiga ndi Chitwi (monga tikuonera pachithunzipa) ndipo ikuthandiza ofalitsa oposa 130,000 a ku Benin, Côte d’Ivoire, Ghana ndi Togo. *

Mlongo wina wa ku Ghana dzina lake Agatha, yemwenso ndi mkazi wa woyang’anira dera anati: “Ndikamaonera mapulogalamuwa n’kumamva abale a m’Bungwe Lolamulira komanso owathandiza akulankhula, ndimangoona ngati Yehova akulankhula  nane ndili m’nyumba mwanga. Ndimadzifunsa kuti, ‘Kupanda mapulogalamu amenewa, kodi munthu wamba ngati ine ndikanadziwa bwanji zimene zimanenedwa m’mapulogalamuwa?’ Mapulogalamuwa akutithandiza kuti tizidziwa zambiri zokhudza abale ndi alongo athu padziko lonse.”

Abale a ku Zambia anatumiza lipoti lonena kuti ngakhale kuti abale a m’mipingo yambiri ku Zambia ndi osauka, amayesetsa kuti azionera mapulogalamu a pa JW Broadcasting. Mwachitsanzo, mpingo wa Misako uli pa mtunda wa makilomita 32 kuchokera m’tauni. Kuderali kuli minda komanso mitsinje yambiri yomwe imadzaza m’nyengo yamvula. M’bale wina dzina lake Simon, yemwenso ndi mtumiki wothandiza ndipo anasamukira kumpingowu, anati: “Mwezi uliwonse munthu wina amayenda pafupifupi maola awiri kuti akafike mumsewu waukulu. Akafika kumeneko, amakwera galimoto n’kupita m’tauni momwe abale amatha kupanga dawunilodi pulogalamuyi. Bambo ena azaka 70 ndi ana awo awiri aamuna anali asanapezekepo pamisonkhano ya Mboni za Yehova. Koma bambowo atamva kuti kumisonkhanoko kukaonetsedwa vidiyo, ngakhale kuti ndi kumudzi, anaganiza zopita. Ataonera pulogalamu ya JW Broadcasting anati: ‘Imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yophunzirira za Mulungu.’”

Abale a ku Russia anatumiza kalata yoyamikira yakuti: “Takhala tikuonera mapulogalamu a JW Broadcasting kwa chaka tsopano ndipo tikusangalala nawo kwambiri. Titangoonera pulogalamu yoyamba, tinaona kuti ndife ogwirizana ndi abale athu padziko lonse ndipo tinasangalala kwabasi. Timaona kuti tili ngati anthu a m’banja limodzi lapadziko lonse. Timasangalalanso kuona abale athu a m’Bungwe Lolamulira. Abalewa akuyesetsa kutipatsa chakudya pa nthawi yake ndipo tonsefe tingathe kuchipeza. Mwezi uliwonse timayembekezera mwachidwi pulogalamu yatsopano. Mapulogalamuwa akutichititsa kuona kuti ndi mwayi waukulu kukhala wa Mboni za Yehova. Tikukuthokozani kwambiri abale athu okondedwa. Tikuthokozanso Yehova ndi Khristu chifukwa cha zimene akutichitira.  Mapulogalamuwa amatithandiza komanso kutilimbikitsa kwambiri.”

A Horst ndi akazi awo a Helga amakhala ku Germany ndipo onse ndi achikulire komanso amadwaladwala. Banjali linalemba kuti: “Mapulogalamu a JW Broadcasting ndi abwino kwambiri. Chimene chimatilimbikitsa kwambiri ndi nkhani za abale ndi alongo olumala. Zitsanzo zawo zimatithandiza kuti tizichita zimene tingathe ngakhale kuti timadwaladwala. Titaonera vidiyo ya m’bale wina yemwe ndi mkulu ngakhale kuti miyendo yake yonse inaferatu, tinaona kuti aliyense angathe kupereka kwa Mulungu zinthu zamtengo wapatali. Tikaona zitsanzo ngati zimenezi, timathokoza Yehova komanso timamupempha kuti apitirize kuwadalitsa.”

Kamnyamata kena ka ku England dzina lake Kodi kanati: “Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cha khama ndiponso nthawi imene mumathera kuti mutulutse mapulogalamu a JW Broadcasting komanso mavidiyo a Kalebe ndi Sofiya. Zinthu zimenezi zikundithandiza kuti ndizimvetsa bwino Baibulo. Ndinabatizidwa ndili ndi zaka 8. Ndikufuna kuti ndikadzakula, ndidzadzipereke kukagwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Ndimafunanso kuti ndikatumikire ku Beteli. Panopa ndili ndi zaka 9, choncho si kale kwambiri pamene ndikwanitse zaka zofunika kuti ndikatumikire ku Beteli.”

Kamtsikana kena kazaka 8 dzina lake Arabella, komwe kamakhala ku England kanalemba kuti: “Ndikuthokoza chifukwa cha mavidiyo ndi zinthu zina zomwe zimakhala pa jw. org. Zonsezi zikundithandiza kuti ndimudziwe bwino Yehova. Mbali yakuti, ‘Zoti Muchite Pophunzira Baibulo’ ndi yabwinonso kwambiri. Ndikamachita mbali imeneyi ndimasangalala koma ndimakhalanso ndikuphunzira za Yehova. Ndinu akatswiri opanga nyimbo zosavuta kuzikumbukira. Mavidiyo a Kalebe ndi Sofiya amandithandizanso kwambiri. Ndikuthokoza nonse chifukwa chogwira ntchito mwakhama.”

^ ndime 3 Mapulogalamu a JW Broadcasting mungawapeze pa tv.jw.org.