Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

“Ndinu Aneba Abwino”

“Ndinu Aneba Abwino”

PA 7 ndi pa 8 May 2016, abale ndi alongo ena otumikira pa Beteli ya kulikulu lathu ku 25 Columbia Heights mumzinda wa Brooklyn ku New York, anali pamalo olandirira alendo n’kumayembekezera anthu odzaona malo. Ngakhale kuti anthu sankaloledwa kukaona malo Loweruka ndi Lamlungu, pa masikuwa anaitana anthu onse apafupi kuti abwere ku Beteli kudzaona malo amene amasungirako Mabaibulo osiyanasiyana.

Ntchito yoitana anthuwa inathandiza kuti anthu adziwe za Mboni za Yehova. Komanso abale ndi alongo amene anagwira nawo ntchitoyi anasangalala kwambiri. Zinalinso zolimbikitsa kumva mawu osangalatsa amene anthu ena omwe anabwera ananena.

 Mwachitsanzo, bambo wina anati: “Ndakhala kudera lino kuyambira m’ma 1960 ndipo ndaona kuti ndinu anthu abwino kuyandikana nanu. Zikanakhala bwino mukanapanda kusamuka chifukwa tikusowani kwambiri.”

Mayi wina anati: “Mwathandiza kuti dera lino likhale lotukuka. Tikuthokoza kuti takhala nanu kwa zaka zonsezi.”

Apainiya ambiri amene anagwira nawo ntchito yoitana anthuwa, anasangalala ataona kuti anthu ake ankawalandira bwino komanso ankamvetsera. Munthu wina anayamikira kwambiri gulu lathu ndipo anadandaula chifukwa choti sakanatha kubwera kudzaona malo.

Zotsatira za ntchitoyi zinali zabwino kwambiri. Pa masiku awiriwa, anthu 48 omwe si a Mboni anabwera kudzaona malo.

Mtsikana wina wazaka za m’ma 20, dzina lake Sally anatha pafupifupi maminitsi 30 akuona malo amene anaikapo Mabaibulo osiyanasiyana. Kenako atafika pamalo olandirira alendo anakumana ndi apainiya amene anamuitana kuti abwere. Sally anawauza kuti sankadziwa zoti kuli malo amene anaikapo Mabaibulo osiyanasiyana. Apainiyawo anamuuza kuti anasangalala kwambiri kuona munthu wophunzira ngati iyeyo akuchita chidwi ndi Baibulo. Sally anayankha kuti: “Baibulo ndi lofunika kwambiri chifukwa ndi limene lingatithandize kumva uthenga wothandiza wochokera kwa Mulungu.”

Sally ananena kuti chifukwa choti amakonda Baibulo, anaphunzira Chilatini ndi Chigiriki ndipo amasangalala akaona Baibulo lomasuliridwa bwino. Amaona kuti Baibulo likamasuliridwa bwino limakhaladi ndi uthenga wolondola osati maganizo a munthu. Apainiyawo atamuuza Sally kuti pawebusaiti yathu ya jw.org pamapezeka mabuku othandiza kuphunzira Baibulo m’zilankhulo  zoposa 800, Sally anadabwa kwambiri. Atamuuzanso kuti omasulira Baibulo ena anachotsa dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo, iye anadabwanso kwambiri ndipo anati: “Koma amachitiranji zimenezi? Zimenezo si zabwino.” Pamene Sally ankapita, ananena kuti: “Ine ndakulira komwe kuno ndipo inu ndinu aneba abwino kwambiri.”

Lolemba, m’bale wina dzina lake John, yemwenso akutumikira pa Betelipo ankalalikira pogwiritsa ntchito kashelefu. Ndiyeno m’busa wina anafika pamalopo ndipo anauza John kuti anali m’gulu la anthu amene anabwera kudzaona malo ndipo anasangalala kwambiri kuona kuti timalemekeza Baibulo. Atacheza kwakanthawi, m’busayo anati: “Koma a Mboninu mwandikwiyitsa kwambiri.” John anadabwa kuti chavuta ndi chiyani, choncho anamufunsa kuti afotokoze. M’busayo anati: “Chifukwa choti mukusamuka. MUSACHOKE CHONDE. Mukhoza kugula nyumba zina zazikulu kapena kumanga zina ngati mukufuna. Anthu inu mwathandiza kwambiri dera lino. Ndadandaula kwambiri kumva kuti mukusamuka.”

Mwachidule, tinganene kuti ntchito yoitana anthuwa inathandiza kuti anthu ambiri a m’derali amve uthenga wathu komanso kuti adziwe dzina la Mulungu.