Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

‘Paulo Anayamika Mulungu, Ndipo Analimba Mtima’

‘Paulo Anayamika Mulungu, Ndipo Analimba Mtima’

Akhristu a mpingo wa ku Roma atamva kuti Paulo akubwera, gulu la abale linayenda ulendo wa makilomita 64 kukamuchingamira. Kodi chikondi chimene abalewa anasonyeza chinamukhudza bwanji Paulo? Iye “atawaona, anayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.” (Mac. 28:15) Ngakhale kuti Paulo ankalimbikitsa mipingo imene ankaichezera, pa nthawi imeneyi pamene anali mkaidi, iyeyo ndi amene analimbikitsidwa.​—2 Akor. 13:10.

Masiku ano oyang’anira dera amayendera mipingo kuti alimbikitse abale ndi alongo. Mofanana ndi atumiki enanso a Mulungu, nawonso nthawi zina amatopa, amakhala ndi nkhawa komanso amafooka. Ulendo wina woyang’anira dera ndi mkazi wake akamadzachezera mpingo wanu, kodi mungadzachite chiyani kuti mumulimbikitse pamene nayenso akukulimbikitsani?​—Aroma 1:11, 12.

  • Muzipezeka pamsonkhano wokonzekera utumiki. Woyang’anira dera amalimbikitsidwa akamaona ofalitsa akusiya zinthu zina n’cholinga choti achirikize mokwanira mlungu wapadera. (1 Ates. 1:2, 3; 2:20) Mungachite bwino kudzachita upainiya wothandiza pa nthawi imeneyi. Kodi mungakonde kudzalowa mu utumiki ndi woyang’anira dera kapena mkazi wake, mwinanso kupita naye ku phunziro lanu la Baibulo? Woyang’anira dera ndi mkazi wake amasangalala kwambiri kulalikira ndi ofalitsa osiyanasiyana kuphatikizapo amene angoyamba kumene kulalikira kapenanso amene alibe luso lolalikira.

  • Muzikhala ochereza. Kodi n’zotheka kumuitana kuti adzadye kunyumba kwanu kapena kumupatsa malo ogona? Zimenezi zingachititse woyang’anira dera ndi mkazi wake kuona kuti mumawakonda. Si kuti amayembekezera kuti muwapangire zinthu zimene simungakwanitse.​—Luka 10:38-42.

  • Muzimvera komanso kugwiritsa ntchito malangizo amene mwapatsidwa. Woyang’anira dera amatithandiza kuona zimene tingachite kuti tizichita zambiri potumikira Yehova. Nthawi zina angafunike kutipatsa malangizo amphamvu. (1 Akor. 5:1-5) Woyang’anira dera amasangalala kwambiri akaona kuti tikutsatira zimene watiuza.​—Aheb. 13:17.

  • Muziwayamikira. Muziuza woyang’anira dera ndi mkazi wake mmene mwapindulira ndi khama lawo. Mukhoza kuwauza pamasom’pamaso, kuwalembera kalata kapena khadi.​—Akol. 3:15.