Mika 2:1-13

2  “Tsoka kwa anthu amene amati akagona pabedi, amakonza chiwembu ndiponso kuganiza mmene angachitire zoipa.+ M’mawa kukangocha, iwo amazichitadi+ chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.+  Iwo alakalaka minda ya anthu ena ndipo ailanda.+ Alakalakanso nyumba za anthu ena n’kuzitenga kukhala zawo.+ Atenga mwachinyengo cholowa cha munthu ndi cha banja lake.+  “Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndikuganiza zobweretsa tsoka pa banja ili.+ Tsoka+ limenelo simudzatha kulipewa,+ moti anthu inu simudzayendanso modzikuza+ chifukwa idzakhala nthawi ya tsoka.+  Pa tsikulo munthu adzanena mwambi+ wokhudza anthu inu ndipo ndithu adzakuimbirani nyimbo ya maliro.+ Anthu adzanena kuti: “Ife talandidwa zinthu zathu!+ Cholowa cha anthu amtundu wathu chaperekedwa kwa anthu ena.+ Talandidwa cholowa chathu. Iye wapereka minda yathu kwa anthu osakhulupirika.”  Choncho mumpingo wa Yehova simudzapezeka aliyense amene azidzayeza ndi chingwe malo ogawidwa mwa kuchita maere.+  Anthu inu musalosere.+ Aneneri amalosera koma sadzalosera zokhudza tsoka limeneli. Ndithu zochititsa manyazi zidzawagwera.+  “‘Inu a nyumba ya Yakobo,+ kodi mukunena kuti: “Kodi mzimu wa Yehova sukukhutira, kapena kodi izi ndiye zochita zake?”+ Kodi mawu anga sapindulitsa+ munthu woyenda mowongoka mtima?+  “‘Dzulo anthu anga enieni andiukira ngati mdani weniweni.+ Anthu amene akuyenda molimba mtima, ngati anthu obwera kuchokera kunkhondo, muwavule mkanjo wawo wokongola kwambiri umene avala pamwamba pa zovala zawo.  Inu mwathamangitsa akazi pakati pa anthu anga, m’nyumba imene mkazi aliyense anali kusangalala kukhalamo. Mwalanda ana awo zinthu zonse zaulemerero+ zimene ndinawadalitsa nazo ndipo simudzazibwezanso mpaka kalekale.*+ 10  Nyamukani,+ chokani chifukwa ano si malo opumulirako.+ Dzikoli liwonongedwa chifukwa chakuti ladetsedwa+ ndipo kuwonongedwako kukhala kopweteka.+ 11  Munthu wolondola zinthu zopanda pake ndi zachinyengo akanena bodza lakuti:+ “Ndidzakulosererani zokhudza vinyo ndi chakumwa choledzeretsa,” ndiye adzakhale mneneri wa anthu awa.+ 12  “‘Ndithu ndidzasonkhanitsa mbadwa zonse za Yakobo.+ Ndidzasonkhanitsa otsala a Isiraeli.+ Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola, komanso ngati gulu la ziweto limene lili pamalo amsipu.+ Kumeneko kudzakhala phokoso la anthu.’+ 13  “Ndithu wogumula mpanda adzawatsogolera.+ Iwo adzadutsa pogumukapo. Adzatuluka kudutsa pachipata.+ Mfumu yawo idzakhala patsogolo pawo ndipo Yehova adzawatsogolera.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.