Mika 4:1-13

4  M’masiku otsiriza,+ phiri+ la nyumba+ ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa mapiri ang’onoang’ono.+ Mitundu ya anthu idzakhamukira kumeneko.+  Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana adzabwera n’kunena kuti: “Bwerani+ anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova. Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+ Iye akatiphunzitsa njira zake,+ ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.”+ Pakuti mu Ziyoni mudzatuluka malamulo ndipo mawu a Yehova adzatuluka mu Yerusalemu.+  Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu+ ndipo adzakonza zinthu+ zokhudza anthu ochokera m’mitundu yamphamvu yakutali.+ Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+  Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu+ ndipo sipadzakhala wowaopsa,+ pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu panena zimenezi.+  Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake.+ Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu+ mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.+  Yehova wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzasonkhanitsa anthu amene anali kuyenda motsimphina.+ Anthu amene anamwazikana ndidzawasonkhanitsa pamodzi.+ Ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu amene ndawasautsa.  Anthu amene anali kuyenda motsimphina ndidzawasonkhanitsanso pamodzi monga anthu otsala.+ Anthu amene anawachotsa m’dziko lawo ndi kuwapititsa kutali ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.+ Yehova adzawalamulira monga mfumu m’phiri la Ziyoni kuyambira nthawi imeneyo mpaka kalekale.+  “Koma iwe nsanja ya gulu la nkhosa, malo okwera a mwana wamkazi wa Ziyoni,+ ulamuliro udzabwerera kwa iwe. Ulamuliro woyamba, ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu,+ udzabwerera kwa iwe.+  “Tsopano n’chifukwa chiyani ukufuula kwambiri?+ Kodi mwa iwe mulibe mfumu, kapena kodi alangizi ako awonongedwa? Kodi n’chifukwa chake zowawa ngati za mkazi amene akubereka zakugwira?+ 10  Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni udzamva ululu waukulu ngati mkazi amene akumva kupweteka kwambiri pobereka.+ Tsopano uchoka m’tauni ndipo ukakhala kumudzi.+ Ukafika mpaka ku Babulo+ koma kumeneko udzapulumutsidwa.+ Kumeneko Yehova adzakuwombola m’manja mwa adani ako.+ 11  “Tsopano mitundu yambiri ya anthu idzasonkhana kuti ikuukire. Mitunduyo ikunena kuti, ‘Tiyeni timuwononge ndipo maso athu aone kuwonongeka kwa Ziyoni.’+ 12  Koma iwo sakudziwa maganizo a Yehova. Iwo sakumvetsa cholinga chake+ pakuti adzawasonkhanitsa ndithu ndi kuwaika pamalo opunthira ngati mmene munthu amasonkhanitsira tirigu amene angomumweta kumene.+ 13  “Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,+ nyamuka upunthe tirigu pakuti nyanga* yako ndidzaisandutsa chitsulo. Ziboda zako ndidzazisandutsa mkuwa ndipo udzanyenyanyenya mitundu yambiri ya anthu.+ Phindu lawo limene apeza mwachinyengo udzalipereka kwa Yehova monga chinthu chopatulika.+ Zinthu zawo udzazipereka kwa Ambuye woona wa dziko lonse lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.