Mika 5:1-15

5  “Iwe mzinda wogonjetsedwa, tsopano udzichekecheke.+ Adani atizungulira kuti atiukire.+ Iwo adzamenya woweruza wa Isiraeli patsaya ndi ndodo.+  “Iwe Betelehemu Efurata,+ ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda.+ Komabe mwa iwe+ mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli,+ amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.+  “Choncho Mulungu adzapereka ana a Isiraeli kwa adani awo+ mpaka pamene mkazi amene adzabereke atabereka.+ Ndipo abale ake onse a munthuyo adzabwerera kwa ana a Isiraeli.  “Iye adzaimirira n’kuyamba kuweta nkhosa mu mphamvu ya Yehova+ ndiponso m’dzina lalikulu la Yehova Mulungu wake.+ Anthuwo azidzakhala kumeneko motetezeka,+ pakuti iye adzakhala wamkulu mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+  Ameneyu adzabweretsa mtendere.+ Msuri akadzalowa m’dziko lathu, akadzaponda nsanja zathu zokhalamo,+ ife tidzamutumizira abusa 7, inde atsogoleri 8 a anthu kuti akathane naye.  Atsogoleriwo adzalanga dziko la Asuri ndi lupanga.+ Adzalanganso dziko la Nimurodi+ m’njira zake zonse zolowera m’dzikolo. Wolamulirayo adzatipulumutsa kwa Msuri.+ Adzatipulumutsa Msuriyo akadzangofika m’dziko lathu ndi kuponda nthaka yathu.  “Otsala a Yakobo,+ pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzakhala ngati mame ochokera kwa Yehova.+ Iwo adzakhala ngati mvula yamvumbi imene ikuwaza pazomera,+ yomwe sidalira munthu kapena kuyembekezera ana a anthu ochokera kufumbi.+  Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu. Iwo adzakhala ngati mkango pakati pa nyama zakutchire. Adzakhala ngati mkango wamphamvu pakati pa magulu ankhosa, umene umati ukadutsa pakati pa nkhosazo, ndithu umazimbwandira ndi kuzikhadzula+ ndipo sipakhala wozipulumutsa.  Dzanja lanu lidzakhala pamwamba pa adani anu,+ ndipo adani anu onse adzaphedwa.”+ 10  Yehova wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzapha mahatchi anu ndipo magaleta anu ndidzawawononga.+ 11  Ine ndidzagwetsa mizinda ya m’dziko lanu. Ndidzagumula malo anu onse amene ali ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 12  Amatsenga onse m’dziko lanu ndidzawapha, ndipo pakati panu sipadzapezekanso anthu ochita zamatsenga.+ 13  Ndidzagwetsa zifaniziro zanu zogoba ndi zipilala zopatulika zimene zili pakati panu, ndipo simudzagwadiranso ntchito za manja anu.+ 14  Ndidzazula mizati yanu yopatulika+ imene ili pakati panu ndi kuwononga mizinda yanu. 15  Ndidzabwezera mokwiya ndiponso mwaukali mitundu ya anthu imene sinandimvere.”+

Mawu a M'munsi