Mika 6:1-16

6  Anthu inu imvani zimene Yehova akunena.+ Nyamukani mukanene mlandu wanu kwa mapiri ndipo zitunda zikamve mawu anu.+  Inu mapiri, imvani mlandu umene Yehova ali nawo pa anthu ake. Inu matanthwe okhazikika, tamverani. Mvetserani inu maziko a dziko lapansi,+ pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake. Iye azenga mlandu Aisiraeli, kuti:+  “Inu anthu anga,+ ndakulakwirani chiyani? Kodi ndakutopetsani mwa njira yanji?+ Perekani umboni wonditsutsa.+  Ine ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo,+ ndipo ndinakuwombolani m’nyumba ya akapolo.+ Ndinakutumizirani Mose, Aroni ndi Miriamu kuti akutsogolereni.+  Inu anthu anga, chonde kumbukirani+ zimene Balaki mfumu ya Mowabu anakonza kuti achite+ ndiponso zimene Balamu mwana wa Beori anamuyankha.+ Kumbukirani zimene zinachitika kuyambira ku Sitimu+ kukafika ku Giligala.+ Zimenezo zinachitika n’cholinga chakuti zochita za Yehova zolungama zidziwike.”+  Kodi nditenge chiyani popita kukakumana+ ndi Yehova? Ndikagwade ndi chiyani kwa Mulungu wakumwamba?+ Kodi ndipite nditatenga nsembe zopsereza zathunthu+ ndi ana a ng’ombe achaka chimodzi?  Kodi Yehova adzakondwera ndi masauzande a nkhosa zamphongo? Kodi adzakondwera ndi mitsinje ya mafuta masauzande makumimakumi?+ Kapena kodi ndipereke mwana wanga wamwamuna woyamba kubadwa chifukwa cha cholakwa changa?+ Kodi ndipereke chipatso cha mimba yanga chifukwa cha tchimo langa?  Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo,+ ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+  Mawu a Yehova akumveka mumzinda.+ Munthu wanzeru zopindulitsa adzaopa dzina lanu.+ Anthu inu, mverani mawu a ndodo ndi a amene anaisankha.+ 10  Kodi m’nyumba ya munthu woipa mukupezekabe chuma chopezedwa mopanda chilungamo,+ ndiponso muyezo woperewera wa efa* umene ndi wosaloleka? 11  Kodi ndingakhale woyera ndili ndi sikelo yachinyengo, ndiponso thumba lachinyengo lamiyala yoyezera zinthu?+ 12  Anthu olemera a mumzindawo amakonda kuchita zachiwawa. Anthu okhalamo akulankhula zonama+ ndipo lilime la m’kamwa mwawo ndi lachinyengo.+ 13  “Ine ndidzakumenyani mpaka kukudwalitsani,+ ndipo mudzawonongedwa chifukwa cha machimo anu.+ 14  Inuyo mudzadya koma simudzakhuta ndipo mudzamvabe njala.+ Mudzanyamula zinthu kuti mukazisunge pabwino koma simudzatha kuziteteza. Zinthu zilizonse zimene mudzazitenge, ine ndidzazipereka kwa adani anu kuti aziwononge.+ 15  Mudzabzala mbewu koma simudzakolola. Mudzaponda maolivi koma simudzadzola mafuta. Mudzaponda mphesa koma simudzamwa vinyo wotsekemera.*+ 16  Anthu inu mukutsatira zochita za Omuri.+ Zochita zonse za anthu a nyumba ya Ahabu, inunso mukuzichita+ ndipo mukuyendera maganizo awo.+ Pa chifukwa chimenechi ndidzakusandutsani chinthu chodabwitsa ndipo anthu a mumzindawo adzakhala oyenera kuwaimbira mluzu.+ Inuyo mudzatonzedwa ndi mitundu ina ya anthu.”+

Mawu a M'munsi

‘Muyezo wa efa’ ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.
Ena amati “wonzuna.”