Mika 1:1-16

1  M’masiku a Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda,+ Yehova analankhula ndi Mika+ wa ku Moreseti kudzera m’masomphenya. M’masomphenyawo anamuuza zokhudza Samariya+ ndi Yerusalemu+ kuti:  “Tamverani anthu nonsenu. Mvetsera mwatcheru iwe dziko lapansi ndi anthu onse okhala mwa iwe.+ Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa akhale mboni yokutsutsani pa zimene mukuchita.+ Yehova akutsutseni ali m’kachisi wake woyera.+  Tamverani! Yehova akuchoka pamalo ake,+ ndipo atsika ndi kupondaponda m’malo okwezeka a padziko lapansi.+  Mapiri asungunuka kumapazi ake+ ndipo zigwa zigawanika. Zonsezi zisungunuka ngati phula losungunuka ndi moto+ ndipo ziyenda ngati madzi othiridwa pamalo otsetsereka.  “Izi zichitika chifukwa cha kupanduka kwa Yakobo ndiponso chifukwa cha machimo a nyumba ya Isiraeli.+ Kodi wachititsa kupanduka kwa Yakobo ndani? Kodi si anthu a ku Samariya?+ Wachititsa ndani kuti Yuda akhale ndi malo okwezeka?+ Si anthu a ku Yerusalemu kodi?  Samariya ndidzamusandutsa bwinja+ ndi malo oyenera kubzalapo mpesa. Miyala yake ndidzaiponya m’chigwa ndipo maziko ake ndidzawafukula n’kuwasiya pamtunda.+  Zifaniziro zake zonse zogoba zidzaphwanyidwa n’kukhala zidutswazidutswa+ ndipo mphatso zonse zimene ankalandira monga malipiro zidzatenthedwa pamoto.+ Mafano ake onse ndidzawawononga. Samariya anapeza zinthu zonsezi ndi ndalama zimene anapeza pochita uhule. Ndipo tsopano zitengedwa kuti zikakhale malipiro a mahule kwinakwake.”+  Chifukwa cha zimenezi ndidzalira ndi kufuula.+ Ndidzayenda wopanda nsapato komanso wosavala.+ Ndidzalira ngati mimbulu ndi kumva chisoni ngati nthiwatiwa zazikazi.  Zilonda zake n’zosachiritsika+ ndipo zafalikira mpaka kukafika ku Yuda.+ Mliri umenewu wakafika pachipata cha anthu amtundu wanga ku Yerusalemu.+ 10  “Anthu inu musanene zimenezi ku Gati ndipo asakuoneni mukulira.+ “Gubudukani pafumbi+ m’nyumba ya Afira. 11  Iwe mkazi wokhala ku Safiri tuluka m’dziko lako uli maliseche mochititsa manyazi.+ Mkazi wokhala ku Zaanana sanachoke m’dziko lake. Beti-ezeli anali malo anu othawirako, koma tsopano kuzingomveka kulira kokhakokha. 12  Mkazi wokhala ku Maroti anali kuyembekezera zinthu zabwino,+ koma zoipa zochokera kwa Yehova zafika pachipata cha Yerusalemu.+ 13  Iwe mkazi wokhala ku Lakisi,+ mangirira galeta ku gulu la mahatchi.* Mzinda umenewu ndiwo unayambitsa tchimo la mwana wamkazi wa Ziyoni,+ pakuti kupanduka kwa Isiraeli kwapezeka mwa iwe.+ 14  Choncho iwe udzapereka mphatso zotsanzikirana kwa Moreseti-gati.+ Nyumba za Akizibu+ zinali chinthu chokhumudwitsa kwa mafumu a Isiraeli. 15  Iwe mkazi wokhala ku Maresha+ ndidzakubweretsera wolanda zinthu za ena.+ Ulemerero wa Isiraeli udzafika ku Adulamu.+ 16  Meta mpala ndi kuchotsa tsitsi lonse chifukwa cha ana ako aamuna amene unali kuwakonda.+ Meta mpala mpaka ufanane ndi wa chiwombankhanga, chifukwa chakuti ana akowo akusiya ndipo apita kudziko lina.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”