Maliro 5:1-22

5  Inu Yehova, kumbukirani zimene zatichitikira.+ Tiyang’aneni kuti muone chitonzo chathu.+   Cholowa chathu chaperekedwa kwa anthu achilendo. Nyumba zathu zaperekedwa kwa alendo.+   Ife takhala anthu amasiye opanda bambo.+ Amayi athu akhala ngati akazi amasiye.+   Madzi akumwa ndi nkhuni, tikuchita kugula.+   Akutithamangitsa ndipo atsala pang’ono kutigwira.+ Tatopa ndipo tikusowa mpumulo.+   Kuti tipeze chakudya chokwanira, tikudalira Iguputo+ ndi Asuri.+   Makolo athu ndi amene anachimwa.+ Iwo anafa, koma ifeyo ndi amene tikuvutika ndi zolakwa zawozo.+   Antchito wamba ndi amene akutilamulira.+ Palibe amene akutilanditsa m’manja mwawo.+   Kuti tipeze chakudya, timaika moyo wathu pachiswe+ chifukwa cha anthu amene ali ndi malupanga m’chipululu. 10  Khungu lathu latentha kwambiri ngati ng’anjo, chifukwa cha njala yaikulu.+ 11  Achitira zachipongwe+ akazi athu amene ali m’Ziyoni ndi anamwali amene ali m’mizinda ya Yuda. 12  Akalonga athu awapachika dzanja limodzi lokha.+ Anthuwo sanalemekezenso ngakhale amuna okalamba.+ 13  Anyamata awanyamulitsa mphero,+ ndipo tianyamata tadzandira polemedwa ndi mitolo ya nkhuni.+ 14  Pazipata sipakupezekanso amuna achikulire+ ndipo anyamata sakuimbanso nyimbo ndi zipangizo zawo zoimbira.+ 15  Chisangalalo cha mumtima mwathu chatha. Kuvina kwathu kwasanduka kulira maliro.+ 16  Chisoti chathu chachifumu chagwa.+ Tsoka kwa ife chifukwa tachimwa!+ 17  Pa chifukwa chimenechi, mtima wathu wadwala.+ Chifukwa cha zinthu zimenezi, maso athu achita mdima.+ 18  Nkhandwe zayamba kuyendayenda paphiri la Ziyoni chifukwa lasanduka bwinja.+ 19  Koma inu Yehova mudzakhala pampando wanu wachifumu mpaka kalekale.+ Mpando wanu wachifumuwo udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+ 20  N’chifukwa chiyani mwatiiwala kwamuyaya+ ndi kutisiya kwa masiku ambiri?+ 21  Inu Yehova, tibwezeni+ kwa inu ndipo ife tibwerera mwamsanga. Mubwezeretse zinthu zonse kuti zikhale ngati mmene zinalili kale.+ 22  Koma inu mwatikanitsitsa.+ Mwatikwiyira kwambiri.+

Mawu a M'munsi