Maliro 4:1-22

א [ʼAʹleph] 4  Golide amene anali kuwala, golide wabwino, sakuwalanso.+Miyala yopatulika*+ aikhuthulira m’misewu yonse.+ ב [Behth]   Ana okondedwa a Ziyoni+ amene anali amtengo wapatali ngati golide woyengeka bwino,Tsopano ayamba kuonedwa ngati mitsuko ikuluikulu yadothi, ntchito ya manja a munthu woumba mbiya.+ ג [Giʹmel]   Ngakhale mimbulu imapereka bere kwa ana ake kuti ayamwe.Koma mwana wamkazi wa anthu anga wakhala wankhanza+ ngati nthiwatiwa m’chipululu.+ ד [Daʹleth]   Lilime la ana oyamwa lamamatira kummero chifukwa cha ludzu.+Ana apempha chakudya+ koma palibe amene akuwapatsa.+ ה [Heʼ]   Anthu amene anali kudya zinthu zabwino adzidzimuka ndipo agwidwa ndi mantha m’misewu.+Anthu amene akula akuvala zovala zamtengo wapatali*+ agona pamilu ya phulusa.+ ו [Waw]   Chilango chimene mwana wamkazi wa anthu anga walandira chifukwa cha zolakwa zake, n’chachikulu kuposa chimene mzinda wa Sodomu unalandira chifukwa cha machimo ake.+Mzinda umenewu unawonongedwa mwadzidzidzi m’kanthawi kochepa, ndipo palibe dzanja limene linauthandiza.+ ז [Zaʹyin]   Anaziri+ ake anali oyera kuposa chipale chofewa.+ Analinso oyera kuposa mkaka.Ndipotu anali ofiira+ kuposa miyala yamtengo wapatali ya korali. Analinso osalala ngati mwala wa safiro.+ ח [Chehth]   Tsopano ayamba kuoneka akuda kuposa makala. Anthu sakuwazindikiranso mumsewu.+Khungu lawo lafota moti lamamatira kumafupa awo.+ Langoti gwaa ngati mtengo. ט [Tehth]   Amene anaphedwa ndi lupanga+ aliko bwino kusiyana ndi amene anafa ndi njala,+Pakuti amene anafa ndi njala anafooka chifukwa chosowa chakudya, ndipo anakhala ngati apyozedwa ndi lupanga. י [Yohdh] 10  Ngakhale amayi, amene amakhala achifundo, afika pophika ana awo ndi manja awo.+Anawo akhala ngati chakudya chotonthoza anthu pa nthawi ya kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+ כ [Kaph] 11  Yehova wasonyeza ukali wake wonse.+ Wakhuthula mkwiyo wake woyaka moto.+Iye wayatsa moto m’Ziyoni, umene wanyeketsa maziko ake.+ ל [Laʹmedh] 12  Mafumu a padziko lapansi ndiponso anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi,+Sanayembekezere kuti mdani angadzalowe pazipata za Yerusalemu.+ מ [Mem] 13  Zimenezi zinachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi zolakwa za ansembe ake,+Amene anakhetsa magazi a anthu olungama a mumzindawo.+ נ [Nun] 14  Ansembe ndi aneneriwo akungoyendayenda mumsewu ngati anthu akhungu.+ Aipitsidwa ndi magazi,+Moti palibe amene akukhudza zovala zawo.+ ס [Saʹmekh] 15  Anthu akuwafuulira kuti: “Chokani! Ndinu odetsedwa!+ Chokani! Chokani! Musatikhudze!”+Ansembe ndi aneneriwo alibe pokhala+ ndipo akungoyendayenda.+ Anthu a mitundu ina akunena kuti: “Amenewa sapitiriza kukhala kuno.+ פ [Peʼ] 16  Yehova wawabalalitsa+ ndipo sadzawayang’ananso.+Anthu sadzaganiziranso ansembe.+ Sadzachitiranso chifundo amuna okalamba.”+ ע [ʽAʹyin] 17  Pamene tili ndi moyo, maso athu akulefuka chifukwa choyembekezera thandizo lomwe silikubwera.+Pofunafuna thandizo, tadalira mtundu wa anthu amene sangabweretse chipulumutso.+ צ [Tsa·dhehʹ] 18  Akutisakasaka kulikonse kumene tikupita,+ moti palibe amene akuyenda m’mabwalo a mizinda yathu.Mapeto athu ayandikira. Masiku athu akwanira, pakuti mapeto athu afika.+ ק [Qohph] 19  Otithamangitsawo ndi aliwiro kuposa ziwombankhanga zouluka m’mwamba.+Iwo atithamangitsa pamapiri.+ Atibisalira m’chipululu.+ ר [Rehsh] 20  Wodzozedwa wa Yehova,+ amene ndi mpweya wotuluka mphuno mwathu,+ wagwidwa m’dzenje lawo lalikulu.+Ponena za ameneyu, ife tinati: “Tidzakhala mumthunzi wake+ pakati pa mitundu ya anthu.”+ ש [Sin] 21  Kondwa ndipo usangalale,+ iwe mwana wamkazi wa Edomu,+ amene ukukhala m’dziko la Uzi.+Iwenso kapuyo ikupeza.+ Udzaledzera ndipo anthu adzakuona uli maliseche.+ ת [Taw] 22  Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chimene anakupatsa chifukwa cha zolakwa zako chatha.+ Sadzakutenganso kupita nawe ku ukapolo.+Tsopano iwe mwana wamkazi wa Edomu, Mulungu watembenukira kwa iwe kuti aone zolakwa zako. Machimo ako wawaika poyera.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “miyala ya pamalo opatulika.”
Mawu ake enieni, “zovala zofiira,” kutanthauza zovala zofiira zamtengo wapatali.