Maliro 3:1-66

א [ʼAʹleph] 3  Ine ndine mwamuna wamphamvu amene ndaona masautso+ chifukwa cha ndodo ya ukali wa Mulungu.   Iye wanditsogolera ndi kundiyendetsa m’malo amdima, osati m’malo owala.+   Ndithudi, iye amandimenya ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.+ ב [Behth]   Wafooketsa thupi langa ndipo wachititsa khungu langa kunyala.+ Iye waphwanyanso mafupa anga.+   Wandimangira mpanda+ kuti chomera chakupha+ ndi mavuto zindizungulire.   Wandichititsa kukhala m’malo amdima,+ ngati munthu woti anafa kalekale.+ ג [Giʹmel]   Wanditsekereza ngati mmene mpanda wamiyala umatsekerezera, kuti ndisatuluke.+ Wandimanga ndi maunyolo olemera amkuwa.+   Komanso ndikalira ndi kupempha thandizo mofuula, iye amatsekereza pemphero+ langa.   Watsekereza njira zanga ndi miyala yosema.+ Wachititsa njira zanga kukhala zovuta kuyendamo.+ ד [Daʹleth] 10  Kwa ine, iye ali ngati chimbalangondo chimene chandibisalira,+ ndiponso ngati mkango umene wakhala pamalo obisika.+ 11  Wasokoneza njira zanga ndipo wandichititsa kukhala wopanda chochita. Wandichititsanso kukhala wosiyidwa.+ 12  Wakunga uta wake+ ndipo wandisandutsa chinthu cholasapo mivi+ yake. ה [Heʼ] 13  Walasa impso zanga ndi mivi yotuluka m’kachikwama kake.+ 14  Ndakhala chinthu choseketsa+ kwa anthu onse odana nane, ndipo amandiimba m’nyimbo yawo tsiku lonse.+ 15  Wandipatsa zinthu zowawa zokwanira.+ Wandikhutitsa chitsamba chowawa.+ ו [Waw] 16  Wachititsa kuti mano anga aguluke ndi miyala.+ Wandipondaponda m’phulusa.+ 17  Inu mwanditayira kutali, moti sindilinso pa mtendere. Sindikukumbukiranso zinthu zabwino.+ 18  Nthawi zonse ndikunena kuti: “Ulemerero wanga ndi chiyembekezo changa mwa Yehova zatha.”+ ז [Zaʹyin] 19  Kumbukirani kuti ndine wosautsika ndi wosowa pokhala.+ Kumbukiraninso kuti ndimadya chitsamba chowawa ndi chomera chakupha.+ 20  Ndithu mudzandikumbukira ndi kundiweramira kuti mundithandize.+ 21  Ndidzakumbukira zimenezi mumtima mwanga.+ Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima wodikira.+ ח [Chehth] 22  Chifukwa cha kukoma mtima kosatha+ kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe,+ ndipo chifundo chake sichidzatha.+ 23  Chifundocho chimakhala chatsopano m’mawa uliwonse,+ pakuti inu ndinu wokhulupirika kwambiri.+ 24  Ine ndanena kuti: “Yehova ndiye cholowa changa.+ Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima womudikira.”+ ט [Tehth] 25  Yehova ndi wabwino kwa munthu amene akumuyembekezera,+ kwa munthu amene akumufunafuna.+ 26  Ndi bwino kuti munthu ayembekezere+ chipulumutso cha Yehova+ moleza mtima.+ 27  Ndi bwino kuti mwamuna wamphamvu anyamule goli ali mnyamata.+ י [Yohdh] 28  Iye akhale payekha ndipo akhale chete,+ chifukwa Mulungu walola kuti zimenezi zimuchitikire.+ 29  Iye awerame mpaka pakamwa pake pafike padothi.+ Mwina angakhale ndi chiyembekezo.+ 30  Aperekere tsaya lake kwa munthu amene akumumenya.+ Alandire chitonzo chokwanira.+ כ [Kaph] 31  Pakuti Yehova sadzatitaya mpaka kalekale.*+ 32  Ngakhale kuti watichititsa kumva chisoni,+ ndithu adzatichitira chifundo chifukwa kukoma mtima kwake kosatha n’kwakukulu.+ 33  Pakuti iye sasangalala ndi kusautsa anthu kapena kuwamvetsa chisoni.+ ל [Laʹmedh] 34  Pajatu kupondaponda+ akaidi onse a padziko lapansi,+ 35  Kukankhira pambali chilungamo cha mwamuna wamphamvu pamaso pa Wam’mwambamwamba,+ 36  Ndi kupotoza chiweruzo cha munthu pa mlandu wake, Yehova savomereza zimenezi.+ מ [Mem] 37  Tsopano ndani ananenapo kuti chinthu chichitike, chinthucho n’kuchitikadi Yehova asanalamule?+ 38  Zinthu zoipa ndi zabwino sizitulukira limodzi pakamwa pa Wam’mwambamwamba.+ 39  Kodi munthu angadandaulirenji+ chifukwa cha zotsatirapo za tchimo lake?+ נ [Nun] 40  Tiyeni tifufuze njira zathu kuti tizidziwe,+ ndipo tibwerere kwa Yehova.+ 41  Tiyeni tichonderere Mulungu kumwamba ndi mtima wonse, ndipo tikweze manja athu m’mwamba+ ndi kunena kuti: 42  “Ife taphwanya malamulo. Tachita zinthu zopanduka+ ndipo inu simunatikhululukire.+ ס [Saʹmekh] 43  Mwadzitchinga ndi mkwiyo wanu kuti tisakufikireni+ ndipo mukupitiriza kutithamangitsa.+ Mwapha anthu mopanda chisoni.+ 44  Mwadzitchinga ndi mtambo waukulu+ kuti pemphero lisadutse ndi kufika kwa inu.+ 45  Mwatisandutsa nyansi ndi zinyalala pakati pa anthu a mitundu ina.”+ פ [Peʼ] 46  Pakamwa pa adani athu onse pakutinenera zoipa.+ 47  Ife tagwidwa ndi mantha ndipo tikusowa chochita.+ Tasiyidwa ndipo tawonongedwa.+ 48  Maso anga akungotuluka misozi ngati mtsinje chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+ ע [ʽAʹyin] 49  Maso anga akungotuluka misozi mosalekeza,+ 50  Kufikira Yehova atayang’ana pansi ndi kutiona ali kumwamba.+ 51  Mtima wanga ukusautsika ndi zimene maso anga aona,+ zimene zachitikira ana onse aakazi a mzinda wanga.*+ צ [Tsa·dhehʹ] 52  Adani anga akundisaka ngati mbalame+ popanda chifukwa.+ 53  Anali kufuna kuchotsa moyo wanga kuti andiponye m’dzenje+ ndipo anali kundiponya miyala. 54  Madzi asefukira ndi kumiza mutu wanga,+ moti ndanena kuti: “Ndifa basi!”+ ק [Qohph] 55  Inu Yehova, ndaitana dzina lanu mofuula ndili m’dzenje lakuya kwambiri.+ 56  Mumve mawu anga.+ Musatseke khutu lanu pamene ndikupempha mpumulo ndiponso pamene ndikulirira thandizo.+ 57  Pa tsiku limene ndinakuitanani,+ munandiyandikira ndi kundiuza kuti: “Usaope.”+ ר [Rehsh] 58  Inu Yehova, mwandiweruzira milandu yanga.+ Mwawombola moyo wanga.+ 59  Inu Yehova, mwaona zoipa zimene andichitira.+ Chonde, ndiweruzireni mlandu wanga.+ 60  Mwaona mtima wawo wokonda kubwezera ndiponso ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.+ ש [Sin] kapena [Shin] 61  Inu Yehova, mwamva mawu awo otonza ndipo mwaona ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.+ 62  Mwamva mawu ochokera pakamwa pa anthu amene akundiukira.+ Mwamvanso zoipa zimene akundinenera monong’ona tsiku lonse.+ 63  Onani zochita zawo zonse.+ Iwo akundiimba m’nyimbo yawo.+ ת [Taw] 64  Inu Yehova, mudzawabwezera mogwirizana ndi ntchito za manja awo.+ 65  Mudzaumitsa mtima wawo,+ ndipo kuchita zimenezi n’kuwatemberera.+ 66  Inu Yehova, mudzawakwiyira ndi kuwathamangitsa ndipo mudzawafafaniza+ padziko lanu lapansi.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “midzi yozungulira.”