Maliro 1:1-22

א [ʼAʹleph] 1  Amene anali ndi anthu ambiri+ tsopano wakhala wopanda anthu.+Amene anali ndi anthu ambiri pakati pa mitundu ina+ wakhala ngati mkazi wamasiye.+Amene anali wolemekezeka pakati pa zigawo zina wayamba kugwira ntchito yaukapolo.+ ב [Behth]   Iye akulira kwambiri usiku,+ ndipo misozi ikutsika pamasaya ake.+Pakati pa onse amene anali kumukonda, palibe amene akumutonthoza.+Anthu onse amene anali anzake amuchitira zachinyengo+ ndipo akhala adani ake.+ ג [Giʹmel]   Yuda wakhala kapolo chifukwa cha nsautso+ ndiponso chifukwa cha kukula kwa ntchito yaukapolo imene akugwira.+Iye wakhala pakati pa mitundu ina ya anthu,+ ndipo sanapeze malo ampumulo.Onse amene anali kumuzunza amupeza pa nthawi ya mavuto ake.+ ד [Daʹleth]   Njira zopita ku Ziyoni zikulira, chifukwa palibe amene akupita kuchikondwerero.+Zipata zake zonse zasiyidwa.+ Ansembe+ ake akuusa moyo.*Anamwali ake agwidwa ndi chisoni,+ ndipo iyeyo akumva kuwawa mumtima. ה [Heʼ]   Adani ake akumulamulira.+ Anthu odana naye sakuda nkhawa.+Yehova wamuchititsa kukhala wachisoni chifukwa cha kuchuluka kwa machimo+ ake,Ndipo ana ake ayenda patsogolo pa adani awo atagwidwa ukapolo.+ ו [Waw]   Ulemerero+ wonse wamuchokera mwana wamkazi wa Ziyoni.Akalonga ake akhala ngati mbawala zamphongo zimene zikusowa msipu.+Iwo akuyenda mofooka+ pamaso pa wowazunza.* ז [Zaʹyin]   Yerusalemu anakumbukira zinthu zake zonse zabwino+ zimene anali nazo kuyambira kalekale.Anazikumbukira m’masiku a masautso ake ndi a anthu ake osowa pokhala.Anthu ake atagwidwa ndi adani, pamene iye analibe munthu womuthandiza,+Adani akewo anamuona, ndipo anamuseka+ chifukwa chakuti wagwa. ח [Chehth]   Yerusalemu wachita tchimo+ lalikulu. N’chifukwa chake wakhala chinthu chonyansa.+Onse amene anali kumulemekeza ayamba kumuona ngati chinthu chachabechabe,+ chifukwa aona maliseche+ ake.Iyenso akuusa moyo+ ndipo watembenukira kwina chifukwa cha manyazi. ט [Tehth]   Zovala+ zake ndi zodetsedwa. Iye sanaganizire za tsogolo+ lake.Wagwa modabwitsa ndipo alibe womutonthoza.+Inu Yehova, onani kusautsika+ kwanga, pakuti mdani wanga akudzitukumula.+ י [Yohdh] 10  Mdani watambasula dzanja lake n’kutenga zinthu+ zake zonse zabwino.Yerusalemu waona mitundu ina itabwera ndi kulowa m’malo ake opatulika,+Mitundu imene munalamula kuti isalowe mumpingo wanu. כ [Kaph] 11  Anthu ake onse akuusa moyo. Iwo akufunafuna chakudya.+Asinthanitsa zinthu zawo zabwino ndi chakudya kuti adzitsitsimutse.+Inu Yehova ndiyang’aneni. Onani kuti ndakhala ngati mkazi wachabechabe.+ ל [Laʹmedh] 12  Inu nonse amene mukudutsa m’njira, kodi mukuona ngati imeneyi ndi nkhani yaing’ono? Ndiyang’aneni kuti muone.+Kodi palinso ululu wina woposa ululu umene ineyo ndalangidwa nawo,+Ululu umene Yehova wandibweretsera nawo chisoni m’tsiku la mkwiyo+ wake woyaka moto? מ [Mem] 13  Iye watumiza moto m’mafupa+ mwanga kuchokera kumwamba, ndipo wafooketsa fupa lililonse.Watchera ukonde+ kuti ukole mapazi anga. Wandibweza kumbuyo.Wandisandutsa mkazi wosiyidwa popanda thandizo. Ndikudwala tsiku lonse.+ נ [Nun] 14  Iye wakhala tcheru kuti aone machimo+ anga. Machimowo alukanalukana m’dzanja lake.Amangidwa m’khosi+ mwanga, moti mphamvu zanga zatha.Yehova wandipereka m’manja mwa anthu amene sindingathe kulimbana nawo.+ ס [Saʹmekh] 15  Yehova wandichotsera anthu anga onse amphamvu+ ndi kuwakankhira pambali.Wandiitanitsira msonkhano kuti athyolethyole anyamata anga.+Yehova wapondaponda moponderamo mphesa+ mwa namwali, mwana wamkazi wa Yuda.+ ע [ʽAʹyin] 16  Ndikulirira zinthu zimenezi ngati mkazi.+ Maso anga ine! Maso anga akutuluka misozi.+Pakuti wonditonthoza, munthu woti anditsitsimule, ali kutali ndi ine.Ana anga asiyidwa+ popanda thandizo, pakuti mdani wanga wadzitukumula.+ פ [Peʼ] 17  Ziyoni watambasula manja ake.+ Iye alibe womutonthoza.+Yehova walamula onse ozungulira Yakobo kuti akhale adani ake.+Yerusalemu wakhala chinthu chonyansa pakati pawo.+ צ [Tsa·dhehʹ] 18  Yehova ndi wolungama,+ koma ine ndapandukira+ mawu a pakamwa pake.Anthu nonsenu, tamverani mawu anga, ndipo muone ululu umene ndikumva.Anamwali anga ndi anyamata anga atengedwa kupita ku ukapolo.+ ק [Qohph] 19  Ndaitana anthu ondikonda kwambiri,+ koma anthuwo andichitira zachinyengo.Ansembe anga ndiponso akuluakulu atha+ mumzinda.Atha pamene anali kufunafuna chakudya choti adye kuti adzitsitsimutse.+ ר [Rehsh] 20  Taonani, inu Yehova. Inetu zandivuta. M’mimba mwanga mukubwadamuka.+Mtima wanga wasweka,+ pakuti ndapanduka kwambiri.+Panja, lupanga lapha+ ana. M’nyumba, anthu akufanso.+ ש [Shin] 21  Anthu amva mmene ndikuusira moyo ngati mkazi,+ koma palibe wonditonthoza.+Adani anga onse amva za tsoka+ langa. Iwo akondwera,+ chifukwa ndinu mwachititsa zimenezi.Inu mubweretsadi tsiku limene mwanena,+ kuti iwo akhale ngati ine.+ ת [Taw] 22  Kuipa kwawo konse kuonekere pamaso panu, ndipo muwalange+ koopsa.Muwalange koopsa monga mmene mwandilangira ine chifukwa cha machimo+ anga onse.Pakuti ndikuusa+ moyo kwambiri ndipo mtima wanga ukudwala.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “wowathamangitsa.”