Maliro 2:1-22
א [ʼAʹleph]
2 Chifukwa chokwiya, Yehova waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni ndi mtambo+ wakuda.Iye waponya pansi chokongoletsera+ Isiraeli kuchokera kumwamba.+Sanakumbukire chopondapo mapazi+ ake pa tsiku la mkwiyo wake.
ב [Behth]
2 Yehova wameza malo okhala a Yakobo. Sanamvere chisoni malo ake alionse.+Mu ukali wake, iye wagwetsa mipanda yolimba kwambiri+ ya mwana wamkazi wa Yuda.Waipitsa ufumu+ ndi akalonga+ ake ndipo wawagwetsera pansi.+
ג [Giʹmel]
3 Mu mkwiyo wake wathyola nyanga* iliyonse ya Isiraeli.+Adani athu atatiukira, iye sanatithandize.+Mkwiyo wake ukuyakirabe Yakobo ngati moto umene wawononga ponseponse.+
ד [Daʹleth]
4 Wakunga uta wake ngati mdani.+ Dzanja lake lamanja+ lakonzeka ngati la mdani,+Ndipo wapitiriza kupha+ anthu onse ofunika kwambiri.Ukali wake waukhuthula ngati moto+ m’hema+ wa mwana wamkazi wa Ziyoni.
ה [Heʼ]
5 Yehova wakhala ngati mdani.+ Wameza Isiraeli.+Iye wameza nsanja zonse za Isiraeli zokhalamo.+ Wawononga malo ake otetezedwa ndiponso mipanda yolimba kwambiri.+Wachititsa kuti kulira ndi maliro+ zimveke mumzinda wa mwana wamkazi wa Yuda.
ו [Waw]
6 Iye wapasula chisimba*+ chake ngati chisimba cha m’munda+ ndipo wathetsa zikondwerero zake.Yehova wachititsa kuti zikondwerero+ ndi sabata ziiwalike mu Ziyoni,Ndipo mu mkwiyo wake waukulu wakana mfumu ndi wansembe.+
ז [Zaʹyin]
7 Yehova wataya guwa lake lansembe.+ Iye wanyoza malo ake opatulika.+Wapereka m’manja mwa adani makoma* a nsanja zake zokhalamo.+Iwo afuula m’nyumba ya Yehova ngati pa tsiku lachikondwerero.+
ח [Chehth]
8 Yehova waganiza zogwetsa mpanda+ wa mwana wamkazi wa Ziyoni.Watambasula chingwe choyezera.+ Sanabweze dzanja lake kuti lisabweretse chiwonongeko.+Walilitsa+ chiunda chomenyerapo nkhondo ndi mpanda. Zonsezi zatha mphamvu.
ט [Tehth]
9 Zipata+ zake zamira munthaka. Wawononga mipiringidzo yake ndipo waithyolathyola.Mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa mitundu ina.+ Malamulo sakutsatiridwa.+Aneneri ake sakuonanso masomphenya ochokera kwa Yehova.+
י [Yohdh]
10 Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi ndipo akhala chete.+Iwo athira fumbi pamitu+ yawo ndipo avala ziguduli.*+Anamwali a Yerusalemu aweramitsa mitu yawo mpaka padothi.+
כ [Kaph]
11 Maso anga atopa ndi kulira.+ M’mimba mwanga mukubwadamuka.+Chiwindi changa chakhuthulidwa+ pansi chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,+Ndiponso chifukwa chakuti ana ndi makanda oyamwa akukomoka+ m’mabwalo a mzinda.
ל [Laʹmedh]
12 Iwo anali kufunsa amayi awo kuti: “Kodi chakudya ndi vinyo zili kuti?”+Anali kufunsa chifukwa anali kukomoka m’mabwalo a mzinda ndi kugona pansi ngati anthu ophedwa,Ndiponso chifukwa moyo wawo unali kukhuthukira pachifuwa cha amayi awo.
מ [Mem]
13 Kodi ndikusonyeze umboni wotani? Kodi ndingakuyerekezere ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?+Kodi ndikufananitse ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwali iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?+Pakuti kuwonongeka+ kwako kwafalikira ngati kukula kwa nyanja. Ndani angakuchiritse?+
נ [Nun]
14 Aneneri ako aona masomphenya achabechabe ndi opanda pake+ onena za iwe.Iwo sanaulule zolakwa zako kuti akuteteze n’cholinga choti usatengedwe kupita ku ukapolo,+Koma anali kuona masomphenya achabechabe ndi osocheretsa+ onena za iwe.
ס [Saʹmekh]
15 Anthu onse odutsa mumsewu akakuona, akuwomba m’manja+ monyodola.Akuimba mluzu+ ndi kupukusa mitu+ yawo poona mwana wamkazi wa Yerusalemu. Iwo akunena kuti:“Kodi uwu ndi mzinda umene anali kunena kuti, ‘Ndi wokongola kwambiri, wotamandika padziko lonse lapansi’?”+
פ [Peʼ]
16 Adani ako onse akukutsegulira pakamwa.+Akuimba mluzu ndi kukukukutira mano.+ Iwo akunena kuti: “Ameneyu timumeza.+Ndithu, lero ndi tsiku limene takhala tikuyembekezera.+ Lafikadi! Taliona!”+
ע [ʽAʹyin]
17 Yehova wachita zimene anali kuganiza.+ Wakwaniritsa zimene ananena,+Zimene analamula kalekale.+ Wapasula zinthu ndipo sanamve chisoni.+Wachititsa adani ako kusangalala+ chifukwa cha zimene zakuchitikira. Wakweza nyanga ya adani+ ako.
צ [Tsa·dhehʹ]
18 Mtima wa anthuwo wafuulira Yehova,+ iwe mpanda wa mwana wamkazi wa Ziyoni.+Gwetsa misozi ngati mtsinje usana ndi usiku.+Usapume. Mwana wa diso lako asaleke kulira.
ק [Qohph]
19 Nyamuka! Lira mofuula usiku, pa nthawi yoyamba ulonda+ wam’mawa.Khuthula+ mtima wako pamaso+ pa Yehova ngati madzi.Pemphera utakweza manja+ ako kwa iye chifukwa cha ana ako,Amene akukomoka ndi njala m’misewu.+
ר [Rehsh]
20 Inu Yehova, yang’anani kuti muone+ yemwe mwamulanga chotere.Kodi amayi azidya zipatso za mimba yawo, ana awo athanzi?+Kapena kodi wansembe ndi mneneri aziphedwa m’malo opatulika a Yehova?+
ש [Shin]
21 Anyamata ndi amuna okalamba+ agona pansi m’misewu.+Anamwali anga ndi anyamata anga aphedwa ndi lupanga.+Mwapha anthu pa tsiku la mkwiyo+ wanu. Onsewo mwawaphadi+ mopanda chisoni.+
ת [Taw]
22 Munaitana+ anthu kuchokera kumalo onse ozungulira, kumene akukhala monga alendo.Pa tsiku la mkwiyo wa Yehova panalibe wothawa kapena wopulumuka.+Ana onse athanzi amene ndinabereka ndi kuwalera, mdani wanga anawapha.+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”
^ Ena amati “zipupa,” kapena “zikupa.”
^ Ena amati “masaka.”

