Pitani ku nkhani yake

Anthu Ambiri Anakaona Ofesi ya Nthambi ya Central America

Anthu Ambiri Anakaona Ofesi ya Nthambi ya Central America

Mu chaka cha 2015, anthu pafupifupi 175,000 anapita kukaona ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya Central America ku Mexico. Zimenezi zikutanthauza kuti kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu, anthu okwana 670 ankapita kukaona ofesi ya nthambiyi tsiku lililonse. Ambiri mwa alendowo ankapita m’magulu akuluakulu ndipo ankayenda kwa masiku angapo pa mabasi a hayala. Ena ankakonzekera ulendo wokaona ofesi ya nthambiyi kwa miyezi ingapo.

“Ulendo wa ku Beteli”

Kwa anthu ena, sizinali zophweka kuti apite kukaona ofesi ya nthambi yomwe imadziwikanso kuti Beteli. Mwachitsanzo, anthu ambiri a mu mpingo wina wa m’dera la Veracruz ku Mexico, analibe ndalama zolipirira ulendo wa pabasi wa makilomita 550 kuti akaone ofesi ya nthambi. Choncho anakhazikitsa dongosolo lomwe ankalitcha kuti “Ulendo wa ku Beteli.” Iwo anapanga magulu a anthu oti aziphika komanso kugulitsa chakudya. Ankapezanso ndalama pogulitsa zinthu zimene ankazipanga pogwiritsa ntchito mabotolo a pulasitiki otha ntchito. Patatha miyezi itatu, anali atapeza ndalama zokwanira zolipirira ulendo wopita ku Beteli.

Kodi khama limene anachita kuti apeze ndalama zolipirira ulendowu linapita pachabe? Ayi ndithu. Mwachitsanzo, mnyamata wina yemwe anapita nawo kukaona malo ku Beteli analemba kuti: “Ulendo wa ku Beteli unandithandiza kuti ndiwonjezere zolinga zanga zauzimu. Komanso tsopano ndimadzipereka kwambiri pochita utumiki wanga ku mpingo.” Nayenso Elizabeth yemwe ali ndi zaka 18, ananena kuti: “Ku Beteli, ndinkatha kuona chikondi chenicheni chomwe ndi chizindikiro cha atumiki a Yehova. Zimenezi zinandipangitsa kuti ndiganize zoyamba kuchita zambiri potumikira Mulungu, choncho ndinayamba utumiki wa nthawi zonse.”

Kumabwera Alendo Ambiri

Nthawi zina, alendo masauzande ambiri amafika tsiku limodzi. Abale ndi alongo amene amaonetsa malo alendo amagwira ntchito mwakhama polandira alendowa ndi manja awiri. Lizzy anati: “Chikhulupiriro changa chimalimba ndikaona anthu odzaona malo akuyamikira ntchito yomwe timagwira komanso ndikamva zomwe anachita kuti akwanitse kudzaona ofesi ya nthambi.”

Chifukwa choti kumabwera alendo ambiri, abale ndi alongo amene amatumikira m’madipatimenti ena amagwira nawonso ntchito yoonetsa malo alendo. Ngakhale kuti kuchita zimenezi kumawawonjezera ntchito, iwo amasangalala kwambiri kulandira alendo. Juan ananena kuti: “Alendo amasangalala kwambiri ndikamaliza kuwaonetsa malo, ndipo ndimadziwa kuti zimene ndachita sizinachite pachabe.”

“Ana Amasangalala Kwambiri”

Ana nawonso amasangalala kwambiri akabwera ku Beteli. Noriko yemwe amagwira ntchito mu Dipatimenti ya Makompyuta anati: “Ndimafunsa ana amene abwera kudzaona ofesi ya nthambi ngati akufuna kudzatumikira pa Beteli. Onse amayankha kuti ‘Inde!’” Malo amodzi omwe amasangalatsa ana ndi pomwe pali zithunzi za Kalebe ndi Sofiya. Pamalowa, anawo amajambulitsa ndi zithunzizi, zomwe kukula kwake n’kofanana ndi misinkhu ya Kalebe ndi Sofiya omwe amapezeka the m’mavidiyo a makatuni a Khalani Bwenzi la Yehova. Noriko ananenanso kuti: “Ana amasangalala kwambiri.”

Ana ambiri amayamikira ntchito imene imachitika pa Beteli. Mwachitsanzo, kamnyamata kena ka ku Mexico dzina lake Henry, kankasunga ndalama m’kachidole kooneka ngati nkhumba n’cholinga choti akapereke ndalamazo akadzapita ku Beteli. Papepala lomwe anaperekera limodzi ndi ndalamazo iye analemba kuti: “Gwiritsani ntchito ndalamazi kuti mupangire mabuku ambiri. Zikomo kwambiri chifukwa cha ntchito yomwe mumagwira potumikira Yehova.”

Inunso Bwerani Mudzaone Malo

A Mboni za Yehova amaonetsa anthu maofesi awo komanso malo osindikizira mabuku kwaulere pa dziko lonse. Ngati nanunso mukufuna kudzaona ofesi ya nthambi, tikukuitanani kuti mudzabwere. Tili ndi chikhulupiriro chonse kuti mudzasangalala. Mukhoza kudziwa zambiri zokhudza kuona maofesi a nthambi pa webusaiti yathu, pambali yakuti ZOKHUDZA IFEYO > MAOFESI NDI KUONA MALO.