M’zaka za pakati pa 1999 ndi 2015, a Mboni za Yehova anamanga Nyumba za Ufumu zoposa 5,000 ku Central America * ndi ku Mexico. Panopa pakufunika nyumba zinanso zoposa 700 zoti a Mboni okwana 1 miliyoni komanso anthu ena a m’maderawa azisonkhanamo.

Poyamba, zinali zovuta kuti mipingo kumaderawa izimanga malo olambirira. A Mboni za Yehova ambiri ku Mexico ankasonkhana m’nyumba za anthu. Izi zinkachitika chifukwa boma linkaletsa zipembedzo kugula malo kapena kumanga nyumba. Koma m’zaka za m’ma 1990 lamuloli linasintha ndipo a Mboni za Yehova anayamba kumanga Nyumba za Ufumu zambiri. Komabe pankatenga miyezi yambiri kuti amalize kumanga nyumba imodzi.

Ntchitoyi Yakhala Ikuyenda Bwino Kwambiri

Mu 1999, ntchito yomanga inayamba kuyenda mofulumira kungochokera pamene panakhazikitsidwa Magulu Omanga Nyumba za Ufumu komanso pulogalamu yomanga Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka kuphatikizapo dziko la Mexico ndiponso mayiko ena 7 a ku Central America. Kuchokera mu 2010, ofesi ya nthambi ku Mexico yakhala ikuyang’anira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’chigawo chonsechi.

Magulu Omanga Nyumba za Ufumu amakumana ndi mavuto ena akamamanga nyumbazi m’madera akutali kwambiri. Mwachitsanzo, ku Panama gulu lina linkafunika kuyenda kwa maola atatu pa boti kuti akafike kumene kunkachitika ntchito yomanga. Gulu linanso lomwe linkamanga Nyumba ya Ufumu ku Chiapas ku Mexico, linkafunika kunyamula zipangizo zomangira pogwiritsa ntchito ndege yaing’ono.

Nyumba za Ufumuzi Zathandiza Kwambiri

Ngakhale anthu ena omwe si a Mboni amafunitsitsa Nyumba ya Ufumu itamangidwa m’dera lawo. Mwachitsanzo, munthu wina wa ku Honduras ananena kuti anthu a m’dera lawo ankafuna kumanga malo achisangalalo pamalo enaake. Koma iye sankagwirazana nazo. Ndiyeno a Mboni atamuuza kuti akufuna kumanga Nyumba ya Ufumu pamalowo iye anati: “Mulungu atamandike.”

M’madera ambiri anthu amachita chidwi ndi khama la ogwira ntchito. Munthu wina wa ku Guatemala anati: “Pachikhalidwe chathu ntchito ya azimayi ndi kuphika basi. Koma n’zochititsa chidwi kuti akazi amene akugwira nawo ntchitoyi akugwira ntchito zimene zimayenera kugwiridwa ndi amuna. Ndikusowa chonena ndikaona akaziwa akunyamula zitsulo komanso kupanga pulasitala. Zimenezi ndi zosowa kwambiri.” Anthu ena okhala pafupi anafika mpaka pogulira omangawo zakudya ndi zakumwa.

Anthu ambiri amayamikiranso mmene timamangira Nyumba za Ufumu. Mwachitsanzo ku Nicaragua, katswiri wina woona za zomangamanga anauza Meya wa mzinda wina kuti nyumba yathu inali yokongola kwambiri ndipo inamangidwa ndi zipangizo zapamwamba. Ananenanso kuti inali yabwino kuposa nyumba zina zonse za mumzindawo.

Nawonso a Mboni za Yehova amasangalala kukhala ndi malo abwino olambirira. Iwo amaona kuti anthu amene amaphunzira nawo Baibulo amayamba kusonkhana Nyumba ya Ufumu ikangomangidwa m’dera lawo. A Mboni a mpingo wina ku Mexico omwe anathandiza kumanga Nyumba ina ya Ufumu anati: “Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa mwayi womanga nawo Nyumba ya Ufumu yomwe imatamanda komanso kulemekeza dzina lake.”

^ ndime 2 Buku la Merriam-Webster’s Collegiate Dictionary, 11th Edition, limanena kuti Central America anapangidwa ndi mayiko monga Guatemala, El Salvador, Honduras, Nicaragua, Costa Rica, Panama, komanso Belize.