Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Ophunzira a pa Yunivesite Ina Anakaona Ofesi ya Nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico

Ophunzira a pa Yunivesite Ina Anakaona Ofesi ya Nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico

Ophunzira a pa yunivesite ina amene anakaona ofesi komanso malo osindikizira mabuku a Mboni za Yehova ku Mexico anaona kuti ulendowu unawathandiza “kusiya tsankho,” inatero magazini yotchedwa Gaceta, ya yunivesiteyo.

Ophunzirawo ananena zotsatirazi:

  • “Tinachita chidwi ndi makhalidwe abwino amene anthu ogwira ntchito kumalowa ankasonyeza . . . anali aulemu, oganizira ena, opanda tsankho komanso aukhondo.”

  • “Aliyense ankagwira ntchito mofunitsitsa ndi anthu ena ndipo zinatipatsa chitsanzo chabwino.”

  • “Aliyense ankaika maganizo pa ntchito imene ankagwira ndipo ankagwira mosangalala.”

  • “Tinachita chidwi chifukwa cha mmene zinthu zimachitikira mwadongosolo m’nyumba yosindikizira mabuku.”

Ophunzirawa anali ochokera kuyunivesite yotchedwa National School of Library and Archival Sciences yomwe ili mu mzinda wa Mexico.

A Mboni za Yehova ali ndi nyumba zomwe ndi maofesi komanso malo osindikizira mabuku m’mayiko pafupifupi 100. Iwo amaloleza anthu kudzaona malo amenewa kwa ulele. Aliyense amene angafune kukaona malo kumaofesi athu akhoza kudziwa zina n’zina zokhudza malowo komanso nthawi yoonera. Pitani pamutu wakuti ZOKHUDZA IFEYO > MAOFESI NDI KUONA MALO. Munthu aliyense komanso mabanja ndi olandiridwa kudzaona malo athu.