NKHANI ZA PADZIKO LONSE
A Mboni za Yehova Anamangidwa Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira—Potengera Dera
Madera amene a Mboni za Yehova anamangidwa, ndipo nthawi zina amazunzidwa kwambiri, chifukwa cha zimene amakhulupirira ngakhale kuti umenewu ndi ufulu wawo.
NKHANI
A Mboni za Yehova a ku Irkutsk Anakhalabe Okhulupirika Ngakhale Apolisi Anawachitira Nkhanza
Pa 4 October 2021, apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba zingapo m’chigawo cha Irkutsk. Anapanikiza anthu ndi mafunso komanso kuwamenya mwankhanza kwambiri. Pamapeto pake a Mboni za Yehova okwana 6, anakawatsekera m’ndende chifukwa chotsatira zomwe amakhulupirira.

