Pitani ku nkhani yake

Khoti la ku Europe Loona za Ufulu wa Anthu lomwe lili ku Strasbourg, m’dziko la France

29 JUNE, 2022
RUSSIA

Dziko la Russia Lasiya Kukhala Membala wa Khoti la ku Europe

Dziko la Russia Lasiya Kukhala Membala wa Khoti la ku Europe

Pa 11 June 2022, Pulezidenti Vladimir Putin anasainira lamulo lonena kuti kuyambira pa 15 March 2022, dziko la Russia lasiya kukhala membala wa Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. Choncho kuyambira pa 15 March 2022 kupita m’tsogolo, zigamulo zonse zopangidwa ndi khotili sizidzagwira ntchito ku Russia. Zimenezi zikuphatikizapo chigamulo chomwe khotili linapereka pa 7 June choletsa boma la Russia kuzunza kapena kumanga a Mboni za Yehova. Zikuphatikikaponso zimene khotili linagamula kuti boma la Russia litulutse Amboni omwe linawamanga komanso kuti libweze katundu yemwe linawalanda kapena liwalipire ndalama zokwana madola 63 miliyoni a ku United States.

Komiti ya Bungwe la Mayiko a ku Europe ndi yomwe imatsimikizira kuti zomwe khotili lagamula zikugwiritsidwa ntchito m’mayiko onse omwe ndi mamembala a bungweli. Dziko la Russia linakhala membala wa Bungwe la Mayiko a ku Europe mu 1996.

Pa 15 March 2022, boma la Russia linadziwitsa komitiyi kuti dziko lawo likufuna kutuluka m’bungweli. Mawa lake, komitiyi inatulutsadi dziko la Russia m’bungweli. Komabe, akuluakulu a boma la Russia anauzidwa kuti mogwirizana ndi zikalata za mgwirizano zomwe anasainira pomwe ankalowa mu Bungwe la Mayiko a ku Europe, akuyenera kupitirizabe kutsatira zigamulo za Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe mpaka pa 16 September 2022.

Pa 7 June 2022, pomwe boma la Russia linkakhazikitsa lamuloli, linkaganiza kuti likadzasiya kukhala membala wa Khoti la ku Europe silidzafunikanso kutsatira mfundo zilizonse zakhotili. Ndi pa tsikunso lomweli pomwe Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapereka chigamulo chake pa mlandu wa abale athu ku Russia.

Chigamulo chomwe Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapanga, chitha kudzagwiritsidwa ntchito pothandiza a Mboni za Yehova m’makhoti a m’mayiko 46 omwe ndi mamembala a Bungwe la Mayiko a ku Europe. Koma chosangalatsa kwambiri ndi chigamulochi n’chakuti chithandiza anthu kudziwa kuti a Mboni za Yehova ndi osalakwa pa zinthu zonse zomwe boma la Russia likuwanamizira. Chigamulochi chithandizanso kuti anthu padziko lonse adziwe za Yehova komanso chithandiza kuti dzina lake lilemekezedwe. Zoonadi, Yehova yekha ndi amene ayenera kulemekezedwa pa zomwe zachitikazi.—Salimo 83:18.