Pitani ku nkhani yake

Khoti la ku Europe Loona za Ufulu wa Anthu lomwe lili ku Strasbourg, m’dziko la France

29 SEPTEMBER, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Khoti la ku Europe Loona za Ufulu wa Anthu Lamaliza Kupereka Zigamulo Zokhudza Ufulu Wolambira ku Russia ndi ku Lithuania

Khoti la ku Europe Loona za Ufulu wa Anthu Lamaliza Kupereka Zigamulo Zokhudza Ufulu Wolambira ku Russia ndi ku Lithuania

Pa 7 September 2022, Khoti la ku Europe Loona za Ufulu wa Anthu linamaliza kupereka zigamulo ziwiri zofunika kwambiri zokhudza a Mboni za Yehova. Pa 7 June 2022, khotili linagamula kuti boma la Russia, linaphwanya malamulo poletsa ntchito za Mboni za Yehova mu 2017. Pa tsiku lomweli khotili linapezanso kuti boma la Lithuania linaphwanya mfundo zomwe mayiko a ku Europe anagwirizana pankhani yokhudza ufulu wa anthu chifukwa bomali linamanga M’bale Stanislav Teliatnikov yemwe anakana kulowa usilikali chifukwa chotsatira zomwe amakhulupirira.

Komabe, boma la Russia kapenanso la Lithuania silinapangire apilo chigamulo chimene khotili linapereka pa 7 June. Choncho mayiko awiriwa anauzidwa kuti ayenera kutsatira chigamulo chimene khotili linapereka, zomwe zikusonyeza kuti akuyenera kupereka chipukuta misozi kwa anthu amene anawaphwanyira ufulu.

Pa 11 June 2022, boma la Russia linayesa kuzemba zomwe khotili linagamula pomwe linanena kuti lasiya kukhala membala wa Khoti la ku Europe. Komabe, pali milandu ina yonena kuti boma la Russia linaphwanya mfundo zomwe mayiko a ku Europe anagwirizana pa nkhani yokhudza ufulu wa anthu pasanafike pa 16 September 2022 ndipo Khoti la ku Europe Loona za Ufulu wa Anthu, likhoza kudzaperekabe chigamulo chake pa milandu imeneyi.

Tikupempherera kuti zigamulo zomwe Khoti la ku Europe Loona za Ufulu wa Anthu linapereka zigwire ntchito yake komanso kuti ufulu wolambira uzilemekezedwa ndi cholinga choti Akhristu okonda mtendere ‘akhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti akhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira.’—1 Timoteyo 2:1, 2.