Pitani ku nkhani yake

Ena mwa abale ndi alongo opitirira 330 a ku Russia ndi ku Crimea omwe akhala m’ndende kuyambira pomwe Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia linapereka chigamulo chake mu 2017

8 JUNE, 2022
RUSSIA

Khoti la ku Europe Lapereka Chigamulo Choti Boma la Russia Lisiye Kuzunza a Mboni za Yehova

Khoti la ku Europe Lapereka Chigamulo Choti Boma la Russia Lisiye Kuzunza a Mboni za Yehova

Pa 7 June 2022, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapereka chigamulo chofunika kwambiri a choletsa boma la Russia kuti lisiye kuzunza a Mboni za Yehova. Khotili linanenanso kuti zomwe boma la Russia linachita poletsa ntchito za Mboni za Yehova mu 2017 ndi zosayenera. Linawonjezeranso kuti boma la Russia linachita zinthu zosemphana ndi malamulo poletsa mabuku a Mboni za Yehova komanso webusaiti yawo ya jw.org. Khotili linalamulanso boma la Russia kuti lisiye kumanga abale ndi alongo athu komanso kuti litulutse onse omwe ali m’ndende. Khotili linalamula boma la Russia kuti libweze zinthu zonse zomwe linalanda a Mboni za Yehova kapena liwalipire ndalama zokwana madola 63,684,978. Khotili linagamulanso kuti boma la Russia lipereke ndalama zokwana madola 3,682,445 kwa a Mboni onse omwe linawamanga ngati chipukuta misozi.

Ofesi ya nthambi ya ku Russia yomwe boma linalanda komanso maofesi okwana 14 omwe ali pamalo aakulu opitirira masikweya mita 100,000, kunja kwa mzinda kwa St. Petersburg

Chigamulochi chinali chokhudza milandu 20 yomwe inachitika kuyambira mu 2010 mpaka mu 2019 yomwe inkakhudza a Mboni za Yehova oposa 1,400. Komabe chigamulochi chithandiza a Mboni enanso ambiri. Chigamulo chimene khoti lija linapereka chinanena kuti boma la Russia “liyenera kutseka milandu yonse yokhudza a Mboni za Yehova . . . komanso kumasula a Mboni onse omwe bomali linawamanga.” (Mawuwo tawadetsa ndife.) Chigamulo chomwe chinaperekedwachi chithandiza abale ndi alongo onse omwe ali m’dziko la Russia ndiponso ena omwe ali kunja kwa dzikoli. Komanso chigamulochi ndi umboni wakuti a Mboni omwe ali m’dziko la Russia ndi nzika zomwe zimalemekeza malamulo moti akuzunzidwa komanso kumangidwa pazifukwa zosamveka.

Pa nthawi yonse yomwe Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linkapereka chigamulo chake, linatsutsa mwamphamvu zomwe akuluakulu a boma la Russia akhala akunena kuti zomwe timachita, kukhulupirira, mabuku athu komanso webusaiti yathu ndi zoopsa. Mwachitsanzo, izi ndi zina zomwe zili m’chigamulochi:

  • Zochita zathu: Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linanena kuti makhoti a ku Russia “sanapeze chilichonse chomwe chikupereka umboni woti a Mboni za Yehova amachita zachiwawa, amadana ndi anthu ena kapena kuwasala.” (§271)

  • Chikhulupiriro choti a Mboni za Yehova amaphunzitsa choonadi: “Kuuza ena mwamtendere kuti chipembedzo chako ndi cholondola komanso kulimbikitsa anthuwo kuti atuluke ‘m’zipembedzo zabodza’ n’kulowa ‘m’chipembedzo cholondola,’ ndi kogwirizana ndi ufulu wachipembedzo komanso ufulu wolankhula maganizo ako, ndipo malamulo amavomereza zimenezi.” (§156)

  • Kulandira magazi: “Munthu aliyense ali ndi ufulu wokana kulandira magazi ndipo zimenezi ndi zogwirizana ndi malamulo omwe anakhazitsidwa pa Msonkhano Wamayiko komanso ndi malamulo a Dziko la Russia.” (§165)

  • Kukana kulowa usilikali potsatira zomwe umakhulupirira: “Kukana kulowa usilikali chifukwa cha zomwe umakhulupirira sikuphwanya lamulo lililonse la Dziko la Russia.” (§169)

  • Mabuku athu: “Zomwe a Mboni za Yehova amachita komanso zomwe amafalitsa m’mabuku awo, zimakhala zolimbikitsa mtendere ndipo zimagwirizana ndi zomwe amanena zoti sachita zachiwawa.” (§157)

  • Webusaiti ya JW.ORG: Khoti linapeza kuti zomwe zimafalitsidwa pawebusaiti ya jw.org si zoopsa. Ngati akuluakulu a boma sankagwirizana ndi zinthu zina zomwe zinkafalitsidwa pawebusaitiyi, ankangofunika kudziwitsa a Mboni za Yehova kuti achotsepo zinthuzo m’malo moletseratu webusaitiyo. (§231 ndi §232)

Chigamulocho chinadzudzula mwamphamvu akuluakulu a boma la Russia posonyeza tsankho, kukondera komanso “mtima wopanda chilungamo.” (§187) Mwachitsanzo pa nkhani imeneyi, chigamulocho chinatchula zinthu zotsatirazi, zomwe khotili linapeza:

  • “Kuletsedwa kwa mabungwe achipembedzo a Mboni za Yehova m’dziko la Russia sikunachitike motsatira malamulo. Kunachitika chifukwa chakuti akuluakulu a boma la Russia amadana ndi a Mboni za Yehova. Zikuoneka kuti akuluakulu a bomawa ankangofuna kupeza njira yoletsera ntchito ya Mboni za Yehova komanso kutsekereza anthu ena kuti asamalowe m’chipembedzochi.” (§254)

  • Akuluakulu a boma la Russia ankalekerera “zolakwika” zikuluzikulu poweruza milandu yokhudza a Mboni za Yehova n’cholinga chongofuna kukhotetsa nkhani. Mwachitsanzo, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia linagwiritsa ntchito malipoti okondera omwe anasankhidwa ndi apolisi komanso maloya a boma m’malo mounika mopanda tsankho mabuku omwe ankanenedwa kuti ndi oopsawo. (§203)

  • Lamulo lonena za anthu ochita zinthu zoopsa linalembedwa mochenjera komanso m’njira yosamveka bwinobwino n’cholinga chongofuna kupereka mwayi kwa apolisi kuti azichitira nkhanza a Mboni za Yehova. (§272)

Sitikudziwa ngati boma la Russia lingatsatire chigamulo chomwe Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe lapereka. Komabe mfundo yaikulu ndi yoti sitidalira maulamuliro a anthu kuti tipirire mavuto omwe tikukumana nawo. M’malomwake, ‘timayembekezeraYehova’ monga “mthandizi wathu ndi chishango chathu.”—Salimo 33:20.

a Pangani dawunilodi lipoti la masamba 7 la Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. Mukhozanso kupanga dawunilodi chigamulo chonse cha masamba 196.