NSANJA YA OLONDA February 2015 | Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu?

Pali anthu ambiri amene amasangalala ndi ntchito yawo. Kodi n’chiyani chawathandiza kuti asamadane ndi ntchito yawo ngakhale itakhala yovuta?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Kugwira Ntchito Mwakhama Ndi Kwachikale?

Anthu ambiri safuna kugwira ntchito zina chifukwa amaziona kuti ndi zonyozeka. Koma anthu ena amagwira ntchito mwakhama ndipo zimenezi zimachititsa kuti azisangalala. Kodi n’chiyani chimawathandiza kuti azisangalala ndi ntchito yawo?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe malangizo a m’Baibulo omwe angakuthandizeni kuti muzisangalala ndi ntchito yanu.

KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuwerenga Baibulo?

Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa kalekale, malangizo ake ndi othandizabe. Kodi mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni bwanji?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinapeza Mayankho Ogwira Mtima a Mafunso Anga

Ernest Loedi anapeza mayankho ogwira mtima a mafunso ake. Mayankho a m’Baibulo anamuthandiza kukhala ndi chiyembekezo.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

“Kodi Mulungu Sindiye Amamasulira Maloto?”

Kodi n’chiyani chinathandiza Yosefe kuti amasulire molimba mtima maloto a mkulu wa ophika mikate, a woperekera chikho komanso a mfumu ya ku Iguputo? Kodi zinatheka bwanji kuti Yosefe yemwe anali mkaidi apezeke kuti ndi wachiwiri kwa mfumu tsiku limodzi lokha?

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi mukuganiza kuti zinthu zingakhale bwanji patakhala boma limodzi lolamulira dziko lonse lapansi? Mulungu walonjeza kuti adzakhazikitsa boma lolamulira dziko lonse lapansi. Kodi ndani ali woyenera kukhala wolamulira wa boma limenelo?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Nkhani Zimene Zili M’Baibulo Ndi Nzeru za Anthu?

Taonani mfundo yochititsa chidwi iyi imene ili m’Baibulo.