Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuwerenga Baibulo?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuwerenga Baibulo?

Nkhani ili m’munsiyi ikusonyeza mmene a Mboni za Yehova amachitira akamakambirana ndi anthu mfundo za m’Baibulo. Tiyerekeze kuti abambo ena a Mboni, dzina lawo a Brian, akucheza ndi a Eric.

BAIBULO LIMAFOTOKOZA MBIRI YAKALE MOLONDOLA

A Brian: Muli bwanji? Dzina langa ndine Brian. Kaya inu ndinu ndani?

A Eric: Ndili bwino. Ine dzina langa ndi Eric.

A Brian: Ndasangalala kukudziwani. Ndikungofuna kukambirana nanu pang’ono mfundo ya m’Baibulo.

A Eric: Komatu ine zachipembedzozi si kwenikweni.

A Brian: Oo. Ndiye kuti simunakulire m’banja lopemphera?

A Eric: Ndinakulira m’banja lopemphera ndithu, koma nditapita kuyunivesite, ndinasiya kupemphera.

A Brian: Kani, ndiye kuyunivesiteko munkaphunzira za chiyani?

A Eric: Ndinkaphunzira zokhudza chikhalidwe cha anthu komanso mbiri yakale. Ndimakonda kwambiri kudziwa zokhudza mbiri yakale, makamaka mmene zikhalidwe ndi zochita za anthu zakhala zikusinthira.

A Brian: Zimasangalatsadi kuphunzira mbiri yakale. Koma kodi munafufuzapo m’Baibulo zokhudza nkhaniyi?

A Eric: Ayi. Ndikudziwa kuti Baibulo ndi buku lothandiza, koma sindinamvepo zoti limafotokoza mbiri yakale.

A Brian: Baibulotu limafotokoza mbiri yakale, ndipo limafotokoza molondola. Ngati mungakonde, ndingakusonyezeni zitsanzo zingapo.

A Eric: Ndingakonde. Komatu ine ndilibe Baibulo.

A Brian: Palibe vuto. Tigwiritsa ntchito langali. Chitsanzo choyamba chikupezeka palemba la 1 Mbiri 29 vesi 26 ndi 27. Lembali likuti: “Kunena za Davide mwana wa Jese, iye analamulira Isiraeli yense. Masiku onse amene iye analamulira Isiraeli anakwana zaka 40. Ku Heburoni analamulira zaka 7, ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.”

A Eric: Ndiye mavesi amenewa akugwirizana bwanji ndi zimene tikukambiranazi?

A Brian: M’mbuyomu, anthu ena amene amatsutsa Baibulo ankanena kuti si zoona kuti kunali Mfumu Davide wotchulidwa m’Baibulo.

A Eric: Oo? N’chifukwa chiyani ankatsutsa?

A Brian: N’chifukwa choti panalibe umboni uliwonse wosonyeza kuti Mfumu Davide analipodi, kupatulapo wa m’Baibulo. Koma mu 1993 anthu ena ofukula zakale anapeza mwala wakale kwambiri pomwe panali mawu akuti, “Nyumba ya Davide.”

A Eric: Nde n’zodabwitsa bwanji?

A Brian: Eetu. Munthu winanso wotchulidwa m’Baibulo amene anthu ena ankatsutsa zoti analipo, ndi Pontiyo Pilato yemwe anali bwanamkubwa m’nthawi ya Yesu. Anatchulidwa pa Luka 3 vesi 1. Vesili likuti: “M’chaka cha 15 cha ulamuliro wa Kaisara Tiberiyo, Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode anali wolamulira chigawo cha Galileya. Filipo m’bale wake anali wolamulira chigawo cha madera a Itureya ndi Tirakoniti. Ndipo Lusaniyo anali wolamulira chigawo cha Abilene.” Pavesili patchulidwa mayina a anthu angapo kuphatikizaponso Pontiyo Pilato.

 A Eric: Eyadi chifukwa pavesili pali mawu akuti, “Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya.”

A Brian: Mwalondola. Kwa zaka zambiri akatswiri ena ankakayikira zoti kunalidi Pontiyo Pilato. Koma pafupifupi zaka 50 zapitazo, ofufuza zakale anapeza mwala winawake ku Middle East pomwe panalembedwa dzina la Pontiyo Pilato.

A Eric: Oo? Ndinali ndisanamvepo zimenezi. Kunena zoona ndimaona kuti Baibulo linalembedwa mwaukatswiri. Komanso zimene takambiranazi zikusonyeza kuti limafotokoza mbiri yakale molondola. Komabe ndikukayikira ngati lingakhale ndi malangizo amene angatithandize masiku ano.

BAIBULO NDI BUKU LAKALE KOMA NDI LOTHANDIZABE

A Brian: Anthu ambiri amaganiza choncho. Koma ineyo ndimaona kuti ndi lothandizabe masiku ano. Chifukwatu ngakhale kuti patenga nthawi yaitali kuchokera pamene Baibulo linalembedwa, zimene anthu amafunika pa moyo sizinasinthe. Mwachitsanzo, kuyambira kale anthu amafunika chakudya, zovala, malo ogona komanso anthu olankhula nawo. Timafunanso kukhala ndi banja losangalala. Si choncho?

A Eric: Ee, zoonadi.

A Brian: Koma kodi mukudziwa kuti mfundo za m’Baibulo zingatithandize pambali zonsezi?

A Eric: Oo? Mungandipatse chitsanzo cha zimenezi?

A Brian: Ee. Mwachitsanzo, m’Baibulo muli malangizo othandiza pa nkhani zokhudza ndalama, moyo wabanja komanso kukhala ndi mabwenzi abwino. Pa nkhani ya banjayi, kodi si zoona kuti amuna ambiri sagwirizana ndi akazi awo komanso amavutika kulera bwino ana awo?

Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa kalekale, mfundo zake ndi zothandizabe masiku ano

A Eric: N’zoonadi. Mwachitsanzo, ine ndi mkazi wanga nthawi zina timasiyana maganizo, ngakhale kuti tatha chaka tili m’banja.

A Brian: Mwaonatu. Koma m’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni. Mwachitsanzo, tiyeni tione zimene lemba la Aefeso 5 vesi 22, 23 ndi 28 limanena. Mungawerenge mavesi amenewa?

A Eric: Ee ndikhoza kuwerenga. Likuti: “Akazi agonjere amuna awo ngati mmene amagonjerera Ambuye, chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo, pokhala mpulumutsi wa thupilo.” Ndipo vesi 28 likuti: “Mwa njira imeneyi amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha.”

A Brian: Zikomo kwambiri. Kodi si zoona kuti ngati mwamuna ndi mkazi atamatsatira malangizo amenewa, banja lawo lingakhale losangalala?

A Eric: Lingakhaledi losangalala. Komatu kuchita zimenezi si kophweka.

A Brian: N’zoonadi, chifukwa tonse timalakwitsa nthawi zina. Ndipotu m’chaputala chomwechi muli vesi limene limatithandiza kuti tisamaiwale mfundo imeneyi. * Choncho anthu okwatirana ayenera kukhala omvetsetsana komanso ololerana. Ine ndi mkazi wanga timaona kuti Baibulo latithandiza kukhala ndi makhalidwe amenewa. Komansotu a Mboni za Yehovafe, tili ndi webusaiti yothandiza kwambiri. Pawebusaitiyi pamapezeka nkhani zosiyanasiyana zothandiza mabanja. Ngati muli ndi nthawi pang’ono ndingathe kukusonyezani nkhani zina zomwe zili pa webusaitiyi.

A Eric: Palibe vuto.

A Brian: Chabwino. Adiresi yolowera pa webusaitiyi ndi www.jw.org/ny. Mwaona? Apa ndiye yatsegula poyambira.

A Eric: Ee! Koma ndiye pali zithunzi zokongola bwanji!

A Brian: Zithunzi zimenezi zikusonyeza ntchito yathu yolalikira imene ikuchitika padziko lonse lapansi. Ndiye tiyeni tifufuze pamene palembedwa kuti, “Mabanja ndi Makolo.” Eya, tapapeza. Pamutuwu pali nkhani zosiyanasiyana zokhudza mabanja komanso kulera ana. Mwaona? Mungakonde kuti tikambirane mutu uti?

A Eric: Ndakonda uwu, wakuti: “Zimene Mwamuna ndi Mkazi Angachite Kuti Asamasiye Kulankhulana Akasemphana Maganizo.” Ndikuona kuti mutu umenewu ungathandize banja lathu.

 A Brian: Mwasankha mutu wabwino kwambiri. Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zitatu zimene zingathandize mwamuna ndi mkazi wake kuti asamasiye kulankhulana. Tawerengani ndime iyi.

A Eric: Chabwino. Akuti: “Kusiya kulankhulana mukasemphana maganizo sikugwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Baibulo limati: “Aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.” Ee! Sindimadziwa zoti Baibulo limaletsanso zimenezi.

A Brian: M’Baibulotu muli zambiri. Mawu a m’Baibulowa achokera palemba la Aefeso 5:33. Tingathe kungotabwanya pali lembali kuti tiliwerenge. Mwaona? Latsegula.

A Eric: Ee ndalionadi.

A Brian: Kodi mwaona kuti vesili likusonyeza kuti mwamuna ayenera kukonda mkazi wake ndipo mkazi ayenera kulemekeza kwambiri mwamuna wake?

A Eric: Akuterodi. Koma zimenezi zingathandize bwanji kuti tisamasiye kulankhulana tikasemphana maganizo?

A Brian: Mwamuna akamakonda mkazi wake ndipo mkazi akamalemekeza mwamuna wake, amagwirizana kwambiri. Kugwirizana kumeneku kumachititsa kuti asamasiye kulankhulana zivute zitani.

A Eric: Komaditu.

A Brian: Ndipotu mwamuna akamakonda kwambiri mkazi wake, mkaziyo amayambanso kumulemekeza kwambiri.

A Eric: Lembali ndi lothandizadi kwambiri.

A Brian: Mwaonatu. Lembali, ngakhale kuti linalembedwa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, lili ndi malangizo amene angathandize mwamuna ndi mkazi wake kukhala ndi banja losangalala. Komatu ichi ndi chitsanzo chimodzi chabe chosonyeza kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza pa nkhani zosiyanasiyana.

A Eric: Sindinkadziwa kuti Baibulo ndi lothandiza ngakhale masiku ano.

A Brian: Ndasangalala kuti tsopano mwadziwa zimenezi. Tikadzakumananso tidzapitiriza kukambirana nkhaniyi pawebusaiti yathuyi. Paja ndinati nkhaniyi ikufotokoza zinthu zitatu zimene zingathandize kuti mwamuna ndi mkazi wake asamasiye kulankhulana. *

A Eric: Tidzaipitirizedi nkhani imeneyi. Mkazi wanganso adzakhalapo.

Kodi pali nkhani ina ya m’Baibulo imene simumaimvetsa? Kapena mumafuna mutadziwa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira? Ngati ndi choncho, funsani a Mboni za Yehova kuti mukambirane nkhani zimenezi.

^ ndime 56 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 14 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.