Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YANU?

Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu?

Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu?

Baibulo limati: “Aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlaliki 3:13) Lembali likusonyeza kuti Mulungu amafuna kuti tizisangalala ndi ntchito yathu. Iye amatiuzanso zimene tingachite kuti zimenezi zitheke. (Yesaya 48:17) Amatiuza zimenezi kudzera m’Mawu ake, Baibulo. Tiyeni tione mfundo zingapo za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuti muzisangalala ndi ntchito yanu.

DZIWANI KUTI KUGWIRA NTCHITO N’KOFUNIKA

Kaya ntchito yanu imapangitsa kuti muziganiza kwambiri kapena imafuna mphamvu, dziwani kuti “kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa.” (Miyambo 14:23) Kodi kumapindulitsa bwanji? Choyamba, kugwira ntchito kumathandiza kuti tizipeza zofunika pa moyo. N’zoona kuti Mulungu amalonjeza kuti sangalephere kusamalira anthu amene amamulambira mokhulupirika. (Mateyu 6:31, 32) Komabe amafuna kuti ifenso tichite mbali yathu pogwira ntchito mwakhama kuti tizipeza zofunika pa moyo.2 Atesalonika 3:10.

Choncho tiyenera kuona kuti ntchito yathu ndi yofunika chifukwa imatithandiza kupeza zofunika pa moyo komanso kuti tizitha kusamalira anthu a m’banja lathu. Joshua, yemwe ali ndi zaka 25, anati: “Munthu umagwira ntchito n’cholinga choti uzipeza zofunika pa moyo. Choncho ngati ntchito yako ikukuthandiza kupeza zofunika pa moyo, ndiye kuti zili bwino.”

Chachiwiri, kugwira ntchito mwakhama kumachititsa kuti uzilemekezeka. Ndipo mawu akuti “kugwira ntchito” akutanthauza kuti munthu akuchita zinazake, osati kungokhala. Tikamayesetsa kugwirabe ntchito yathu, ngakhale itakhala yosasangalatsa kapena yovuta, timasangalala chifukwa chodziwa kuti ndife akhama. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti ndife osiyana ndi anthu amene amathawa ntchito ikakhala yovuta. (Miyambo 26:14) Aaron, amene tamutchula m’nkhani yoyamba ija, anati: “Ndikamaweruka kuntchito, ndimakhala  nditatopa chifukwa chogwira ntchito mwakhama tsiku lonse. Ndimadziwanso kuti ambiri sazindikira n’komwe kuti ndagwira ntchito yambiri. Komabe ndimakhala wosangalala chifukwa chodziwa kuti ndagwira ntchito inayake.”

MUZIYESETSA KUIDZIWA BWINO NTCHITO YANU KUTI MUZIIGWIRA MWALUSO

Baibulo limanena za mkazi amene “manja ake amagwira ntchito iliyonse mosangalala.” Limanenanso za munthu “waluso pa ntchito yake.” (Miyambo 22:29; 31:13) Komatu pamafunika khama kuti munthu aidziwe bwino ntchito yake n’kumaigwira mwaluso. Zimenezi n’zofunika chifukwa ngati munthu sakuidziwa bwino ntchito yake sasangalala nayo.

Ntchito iliyonse ikhoza kukhala yosangalatsa. Chongofunika ndi kuidziwa bwino kuti uziigwira mwaluso. William yemwe ali ndi zaka 24 anati: “Ukachita khama kuphunzira ntchito kenako n’kuona kuti wayamba kuigwira bwino, umasangalala kwambiri. Chinanso chimene chimathandiza kuti uzisangalala ndi ntchito yako, ndi kuigwira moikirapo mtima osati mwam’gwazo.”

MUZIGANIZIRA MMENE NTCHITO YANU IMATHANDIZIRA ENA

Mukamagwira ntchito, musamangoganizira za ndalama zimene mumalandira. M’malomwake mungadzifunse mafunso awa: ‘Kodi ntchito yanga ndi yofunika bwanji? Kodi chingachitike n’chiyani ngati nditapanda kuigwira kapena nditakhala kuti sindinaigwire bwino? Nanga ntchito yangayi imathandiza bwanji anthu ena?’

Funso lomalizali ndi lofunikadi kuliganizira chifukwa munthu amasangalala kwambiri ndi ntchito yake, makamaka akaona kuti ikuthandizanso anthu ena. Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Musaiwale kuti kuwonjezera pa makasitomala komanso mabwana anu, palinso anthu ena amene amapindula ndi ntchito yanu. Anthu amenewa ndi monga a m’banja lanu ndiponso ovutika.

Anthu a m’banja lanu. Bambo akamagwira ntchito mwakhama zimathandiza banja lake m’njira ziwiri. Choyamba, zimathandiza kuti azipeza zofunika pa banja lake monga chakudya, zovala komanso malo ogona. Akamachita zimenezi amakhala akukwaniritsa udindo umene Mulungu anamupatsa wosamalira “anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira.” (1 Timoteyo 5:8) Chachiwiri, bambo amene amagwira ntchito mwakhama, amapereka chitsanzo chabwino kwa ana ake. Shane, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, anati: “Bambo anga ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yolimbikira ntchito. Iwo akhala akugwira ntchito ya ukalipentala kwa zaka zambiri. Zinthu zimene amapanga zimathandiza kwambiri anthu. Chitsanzo chawo chandiphunzitsa kuona kufunika kogwira ntchito ndi manja athu.”

Anthu ovutika. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti azigwira “ntchito molimbikira . . . kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.” (Aefeso 4:28) Ngati timagwira ntchito n’kumapeza ndalama zothandizira banja lathu, zingakhale zosavuta kuti tikhalenso ndi ndalama zothandizira anthu ovutika. (Miyambo 3:27) Choncho, tikamagwira ntchito mwakhama timathanso kuthandiza ena. Kuchita zimenezi kumachititsa kuti tizikhala osangalala.

 MUZICHITA ZOPOSA ZOMWE MWAUZIDWA

Pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu anati: “Winawake waudindo akakulamula kuti umunyamulire katundu mtunda wa kilomita imodzi, umunyamulire mtunda wa makilomita awiri.” (Mateyu 5:41) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo imeneyi pa nkhani ya ntchito? Mukapatsidwa ntchito yoti mugwire, muzikhala wokonzeka kuchita zoposa zimene mwauzidwa. Muzidziikira nthawi yoti muimalize komanso muziyesetsa kuigwira bwino ndiponso mofulumira. Muziyesetsanso kuigwira motsatira malangizo ake onse.

Mukamachita zoposa zimene mwauzidwa, mumasangalala kwambiri ndi ntchito yanu. Zili choncho chifukwa chakuti mumachita zinthu chifukwa choti mwafuna nokha osati chifukwa choti wina wakukakamizani. (Filimoni 14) Mfundo imeneyi ikutikumbutsa zimene lemba la Miyambo 12:24 limanena. Limati: “Dzanja la anthu akhama n’limene lidzalamulire, koma dzanja laulesi lidzagwira ntchito yaukapolo.” N’zoona kuti siinu kapolo. Komabe nthawi zonse mukamadikira kuti abwana anu achite kukuuzani kuti muchite zambiri, mumayamba kudziona ngati kapolo womangouzidwa zochita. Koma mukamachita zambiri mwakufuna kwanu, simumadziona ngati kapolo chifukwa palibe amene wakulamulani kuchita zimenezo.

MUZIPEZANSO NTHAWI YOCHITA ZINTHU ZINA

Baibulo limatilimbikitsa kukhala akhama ndipo monga taonera, munthu amene amagwira ntchito mwakhama zinthu zimamuyendera bwino. (Miyambo 13:4) Komabe kumbukirani kuti pali zinthu zinanso zofunika zimene mungachite. Baibulo silinena kuti munthu azingokhalira kugwira ntchito. Lemba la Mlaliki 4:6 limati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Munthu amene amangokhalira kugwira ntchito moti sakhalanso ndi nthawi kapena mphamvu yochita zinthu zina, amakhala wosasangalala. Munthu wotereyu cholinga cha ntchito yake sichioneka ndipo amangokhala ngati ‘akuthamangitsa mphepo.’

Baibulo limasonyeza kuti sitiyenera kuona ntchito ngati yofunika kwambiri kuposa chilichonse. Ngakhale kuti limanena kuti tizikonda ntchito yathu, limatiuzanso kuti ‘tizitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.’ (Afilipi 1:10) Kodi zinthu zina zofunika kwambiri zimene tingachite ndi ziti? Ndi monga kupeza nthawi yochita zinthu ndi anthu a m’banja lathu komanso kucheza ndi anzathu. Chinanso chofunika kwambiri ndi kuchita zinthu zauzimu monga kuwerenga Baibulo ndi kuganizira mmene ungagwiritse ntchito zimene wawerengazo.

Anthu amene amagwira ntchito mwakhama koma n’kumapezanso nthawi yochita zinthu zina zofunika, amasangalala kwambiri ndi ntchito yawo. William yemwe tamutchula kale uja anati: “Ndimachita chidwi kwambiri ndi zimene abwana anga amachita. Ndi munthu wolimbikira ntchito ndipo makasitomala awo amawakonda chifukwa amagwira ntchito yotamandika. Komabe amapezanso nthawi yochita zina zofunika monga kucheza ndi banja lawo komanso kuchita zinthu zina zokhudza chipembedzo chawo. Amaoneka kuti ndi munthu wosangalala kwambiri ndipo zinthu zimawayendera.”