Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo Wakuchipululu Chachikulu Choyera

Ulendo Wakuchipululu Chachikulu Choyera

 Kalata Yochokera ku Norway

Ulendo Wakuchipululu Chachikulu Choyera

M’MAWA kwambiri tsiku lina m’nyengo yachisanu, ine ndi mkazi wanga tinakankha katani n’kusuzumira panja kuti tione mmene kunja kunachera. Tinasangalala kwambiri titaona kuti kwacha bwino zedi moti kumwamba kunali mbee! kopanda mitambo. Apa n’kuti titatsala pang’ono kuyambapo ulendo wopita kudera linalake lalikulu lotchedwa Finnmarksvidda, lomwe lili pamalo athyathyathya pamwamba pa phiri, kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi. Cholinga chathu chinali chakuti tikalalikire kuderali kwa masiku atatu.

Ku Norway, nyengo yachisanu imakhala yozizira zedi, moti kunena zoona, tinkada nkhawa tikaganizira za ulendo wopita kuchipululu cha m’dera lakumpoto limeneli. Koma mwamwayi, pa ulendowu tinali ndi anthu ena atatu a Mboni za Yehova omwe amakhala m’derali. Anthuwa ankadziwa bwino zimene tingakumane nazo ndipo anatipatsa malangizo abwino.

Kuderali kuli misewu yochepa kwambiri. Njira yabwino kwambiri imene tingafikire anthu mosavuta, n’kukwera mthuthuthu woyenda pachipale chofewa. Motero tinatenga mithuthuthu yathu n’kulongedzamo zovala, chakudya komanso petulo wina wapadera. Zina mwa zinthu zimenezi tinazilongedza m’kangolo komwe tinakamangirira kumthuthuthu. Titafika kudera lathyathyathya la pamwamba pa phirilo, tinkati tikaponya maso mbali zonse, tinkangoona chipale chofewa chokhachokha mpaka kutali kwambiri. Chipalecho chinkaoneka chokongola kwambiri chifukwa chinkanyezimira bwino ndi kuwala kwa dzuwa.

Ku Finnmarksvidda kumapezeka nyama zosiyanasiyana monga mphalapala zokhala m’madera achipale chofewa, nyama zinazake zofanana ndi ntchefu, avumbwe, nkhandwe, zimbalangondo zing’onozing’ono, komanso zimbalangondo zikulukulu, zomwe zilipo zochepa. Ngakhale zili choncho, chomwe tinkayembekezera kwambiri n’choti tikumane ndi anthu a m’dera lakutalili. Komabe, tinkafunitsitsa kwambiri kukumana ndi anthu a mtundu wachisami, omwe pamoyo wawo amadalira kuweta mphalapala za kuderalo, kapena kugwira ntchito m’malo osiyanasiyana ogona alendo omwe ali paphiripo.

Pamene tinali paphiripo, tinaona ana a sukulu ambiri akuchita masewera otsetsereka pachipale chofewa, panja pa malo ena ogona alendo. Atationa, iwo anaima kaye kuti alankhule nafe, ndipo anatifunsa chomwe tinabwerera. Apa tinapezerapo mwayi, ndipo tinasangalala kuwafotokozera chifukwa chomwe tinabwerera. Pamene tinkasiyana nawo, mnyamata wina pagululo anatiuza kuti: “Tikukufunirani zabwino zonse pamene mukugwira ntchito yanu yolalikira uthenga wa m’Baibulo.” Tinakweranso mithuthuthu yathu ndipo tinayenda ulendo wautali kudutsa m’dera lalikulu zedi lopanda chilichonse, la madzi oundana ndiponso la chipale chofewa. Ulendowo uli mkati, tinkaganiza kuti, Koma abale, kodi sitingakumaneko ndi gulu la mphalapala?

Titayandikira kanyumba kena kogona alendo, munthu winawake anafika kudzatipatsa moni mwansangala. Munthu ameneyu anali mmodzi mwa anthu ochepa kwambiri omwe ndi nzika zakuno. Munthuyo ataona kuti kangolo kathu kawonongeka, anadzipereka mokoma mtima n’kuyamba kukakonza. Iye ankachita zinthu mwa phee! chifukwa anthu akuno sachita zinthu mwaphuma. Zimenezi zinachititsa kuti nafenso mitima yathu ikhale m’malo. Atamaliza kukonza kangoloko,  tinamuthokoza kwambiri ndipo tinamuuza mfundo zingapo za m’Baibulo, zofotokoza chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu azivutika. Munthuyo anamvetsera mwachidwi kwambiri, ndipo tisanasiyane, tinam’patsa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? komanso magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Atalandira, anangomwetulira n’kunena kuti, “Ndathokoza chifukwa chocheza nane.”

Titacheza ndi anthu ena angapo, kunja kunayamba kuda ndipo tinayamba ulendo wobwerera kukanyumba kamene tinafikira. Mwadzidzidzi, tinaona nkhandwe. Ubweya wake wofiira unkaoneka mokongola kwambiri chifukwa unkanyezimira ndi kuwala kwa chipale chofewa. Nkhandweyo itationa, inangoima kwakanthawi ndithu n’kumangotiyang’anitsitsa koma kenako inapitiriza ulendo wake. Ulendo wathu uli mkati, kunja kunayamba kugwa chipale chofewa ndipo zinali zovuta zedi kuti tione kumene tikupita. Kenako mitima yathu inakhala m’malo titaona kanyumba kathu kaja. Titangofika, tinatenga sitovu yathu n’kukoleza moto, ndipo pang’ono m’pang’ono, m’kanyumbako munayamba kutenthera bwino. Tinali osangalala kwambiri ngakhale kuti tinali titatheratu n’kutopa chifukwa choyenda tsiku lonse pachipale chofewa m’mithuthuthu yathu.

Pasanapite nthawi yaitali, kunja kunachanso. Tinalongedza katundu wathu pamthuthuthu wathu, n’kuyamba ulendo wopita m’dera linalake lotsika, ndipo tinatsetsereka podutsa m’mbali mwa mtsinje. Kenako tinafika kunyumba ina yogona alendo, komwe tinakumana ndi mnyamata wina ndipo tinamulalikira pomuuza mfundo zingapo zolimbikitsa zochokera m’Baibulo. Titamaliza kucheza naye, mnyamatayu anatikomera mtima potisonyeza kanjira kachidule kobwerera mumsewu.

Tsopano tsiku loti tibwerere kwathu linafika. Ulendo wobwerera uli mkati, tinalowa m’malo ena omwe mumakhala nyama zakutchire (Stabbursdalen National Park). Malo amenewa ndi okongola zedi moti tinkati tikayang’ana mbali iyi, n’kutembenukiranso mbali iyo, tinkangoona dera lokongola lokhalokha, ndipo chapatali, tinkaona mapiri okutidwa ndi chipale chofewa omwe ankanyezimira ndi kuwala kwa dzuwa. Kenako tinangoona chigulu cha mphalapala. Nyamazi zinkangodya mwachifatse ndipo zinkafukula ndi mapazi udzu umene unaphimbidwa ndi chipale chofewacho. Chapatali ndithu, tinaona munthu wina wa mtundu wachisami, ali khalee! pamthuthuthu wake. Iye ankayang’anira mphalapala zakezo ali phee! ndipo galu wake ndi yemwe ankathamangathamanga pokusa ziwetozo kuti zikhale malo amodzi. Kenako galuyo anaima kaye n’kumatinunkhiza. Koma posapita nthawi, tinangomuona uyo, wayambiranso kukusa ziweto zija. Tinayamba kucheza ndi mwini ziwetozo ndipo tinamuuza uthenga wathu. Iye anali munthu womasuka ndiponso wochezeka kwabasi, moti ankamvetsera mwachidwi.

Pamene tinkapitiriza ulendo wobwerera kwathu, tinkaganizira za anthu onse amene tinakumana nawo pa ulendo wathu wa makilomita 300. Ngakhale kuti zomwe tinakwanitsa kuchita kuderali n’zochepa, tikuona kuti ndife amwayi kwambiri chifukwa chogwira nawo ntchito yolalikira kwa anthu amene amakhala kuchipululu chachikulu choyerachi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 15]

© Norway Post