Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Phunzitsani Ana Anu

Ankatchedwa “Ana a Bingu”

Ankatchedwa “Ana a Bingu”

NTHAWI ya mvula mwina unamvapo kulira kwa bingu lamphamvu. Kodi unachita mantha utamva bingu limenelo?​ * Nthawi inayake Yesu anatchula otsatira ake awiri kuti ndi “Ana a Bingu.” Tiye tione chifukwa chake anawatchula dzina limeneli.

Otsatira a Yesu awiriwo anali Yakobo ndi Yohane, omwe anali apachibale ndipo anali ana a Zebedayo ndi mkazi wake Salome. Zikuoneka kuti Salome anali mchemwali wake wa Mariya, amayi ake a Yesu. Choncho Yesu, Yakobo ndi Yohane ayenera kuti anali apachibale ndipo ayenera kuti ankasewerera limodzi ali ana.

Popeza kuti Zebedayo anali msodzi, Yakobo ndi Yohane nawonso anali asodzi. Anthu awiriwa anali m’gulu la anthu oyambirira amene Yesu anawasankha kuti akhale otsatira ake. Yesu atawaitana kuti akhale otsatira ake, nthawi yomweyo iwo anasiya ntchito yawo yausodzi n’kumutsatira. Patapita nthawi, Yesu anasankha anthu 12 mwa otsatira ake kuti akhale atumwi, ndipo Yakobo ndi Yohane anali m’gulu limeneli.

Kutatsala miyezi yochepa kuti Yesu aphedwe, iye limodzi ndi atumwi ake ankadutsa m’dera lamapiri la Samariya. Pa nthawiyi kunja kunali kutayamba kuda ndipo onse anali atatopa kwambiri. Koma Asamariya ananena kuti sakufuna kuti Yesu ndi atumwi akewo agone mumzinda wawo. Kodi ukudziwa chifukwa chake?​— Tiye tione.

Yesu ndi atumwi akewo anali Ayuda, ndipo Ayuda ambiri ankadana ndi Asamariya. Koma Yesu sankadana nawo. Iye ankawachitira chifundo, ndipo Yakobo ndi Yohane ankafunikanso kuchita zimenezi. Komabe, Asamariyawo atakana kuti Yesu ndi atumwiwo alowe mumzinda wawo, Yakobo ndi Yohane  anakwiya kwambiri ndipo anafunsa Yesu kuti: ‘Kodi mukufuna tiwaitanire moto kuchokera kumwamba kuti uwaphe?’ Kodi ukuganiza kuti Yesu anati chiyani?​— Iye anawauza kuti analakwa ponena zinthu zoipa ngati zimenezo. Zikuoneka kuti Yakobo ndi Yohane ankafunika kuphunzira kuti akhale anthu achifundo.

Vuto lina lalikulu limene Yakobo ndi Yohane anali nalo linali lakuti ankafuna kumakhala oyamba nthawi zonse, kapena kuti azioneka ngati ofunika kwambiri. Mwachitsanzo, Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, iwo anatuma mayi awo kwa Yesu kuti akamuuze kuti: “Lonjezani kuti ana angawa adzakhala, mmodzi kudzanja lanu lamanja, wina kumanzere kwanu, mu ufumu wanu.” Koma atumwi 10 ena aja atamva zimene Yakobo ndi Yohane anachita, anakwiya kwambiri. Kodi iwenso ukanakwiya?​

Mwina ukanakwiya. Palibe amene amasangalala ndi munthu wofuna kukhala woyamba nthawi zonse komanso wofuna kuti azionedwa ngati wofunika kwambiri. Patapita nthawi, Yakobo ndi Yohane anazindikira kuti analakwa posasonyeza chifundo ndipo kenako anasintha. Iwo anakhala atumwi achikondi kwambiri komanso achifundo. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa?​

Tikuphunzira kuchokera kwa Yesu kuti ifenso tiyenera kusonyeza chifundo kwa ena. Yesu ankachita zabwino kwa anthu onse, kaya akhale amuna, akazi kapena ana. Kodi nthawi zonse uziyesetsa kukumbukira chitsanzo chake n’kumamutsanzira?​

^ ndime 3 Ngati mukuwerengera mwana nkhaniyi, mukapeza mzera muime kaye ndi kumulimbikitsa kuti anenepo maganizo ake.