Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dzikoli Litha mu 2012?

Kodi Dzikoli Litha mu 2012?

 Zimene Owerenga Amafunsa . . .

Kodi Dzikoli Litha mu 2012?

▪ “Chinamtindi cha anthu okhulupirira kuti dziko litha pa 21 December 2012, chakhamukira m’tauni inayake ku France . . . Anthuwo akukhulupirira kuti dziko litha pa tsiku limeneli chifukwa m’pamene pakuthera kalendala yakale ya anthu a mtundu wa Maya, ya zaka 5,125.”​—Zinatero nkhani za pa BBC.

Dziko lapansili lipitirizabe kukhalapo kwa nthawi yaitali kwambiri ngakhale kuti anthu osiyanasiyana akuuza anthu kuti dzikoli litha. Ena mwa anthu amene akunena zimenezi ndi atsogoleri a zipembedzo, anthu ena amene amati ndi asayansi, ndiponso anthu ena a m’nthawi yathu ino olosera za m’tsogolo. Ndithudi, dziko lapansili silitha mu 2012. Ndipo kunena mwatchutchutchu, pulaneti lathuli, lomwe timalitchula kuti dziko lapansi, lidzakhalapo mpaka kalekale.

Baibulo limatiuza kuti: “M’badwo umapita ndipo m’badwo wina umabwera, koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.” (Mlaliki 1:4) Komanso taganizirani mawu amene ali pa Yesaya 45:18. Lembali limati: “Yehova, . . . amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga, amene analikhazikitsa mwamphamvu, amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo, wanena kuti: ‘Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.’”

Kodi bambo wachikondi, yemwe wathera nthawi yaitali poumbira mwana wake chidole kuti aziseweretsa, angalande mwanayo chidolecho n’kuchiphwanyaphwanya atangomupatsa kumene? Ayi, chifukwa zimenezo zingakhale nkhanza. Mofanana ndi zimenezi, chifukwa chachikulu chimene Mulungu analengera dziko lapansili n’choti anthu azikhalamo mosangalala. Mulungu anauza Adamu ndi Hava, omwe anali banja loyambirira, kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.” Kenako “Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.” (Genesis 1:27, 28, 31) Mulungu sanasinthe cholinga chimene analengera dziko lapansi, ndipo sadzalola kuti liwonongedwe. Ponena za malonjezo ake onse, Yehova ananena motsindika kuti: “[Mawu anga] sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake, koma adzachitadi zimene ine ndikufuna ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:11.

Komabe Yehova ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) M’Mawu ake, iye analonjeza kuti: “Owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo. Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi ndipo achinyengo adzazulidwamo.”​—Miyambo 2:21, 22.

Kodi zimenezi zidzachitika liti? Palibe munthu amene akudziwa nthawi yake yeniyeni. Yesu anati: “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, koma Atate okha.” (Maliko 13:32) Ndipo a Mboni za Yehova sayesa kulosera nthawi imene Mulungu adzawononge anthu oipa. Ngakhale kuti iwo amaonetsetsa mwachidwi “chizindikiro” cha nthawi yamapeto ndiponso amakhulupirira kuti tikukhala m’nthawi imene Baibulo limaitchula kuti “masiku otsiriza,” iwo sangadziwe nthawi yeniyeni imene “mapeto” adzafike. (Maliko 13:4-8, 33; 2 Timoteyo 3:1) M’malomwake, iwo amasiya nkhani imeneyi m’manja mwa Atate wawo wakumwamba ndi Mwana wake.

Koma padakali pano, anthu a Mboni za Yehova ndi otanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu ndi boma lakumwamba limene lidzalamulire dziko lapansili ndi kulisintha kukhala paradaiso wamtendere, yemwe ‘olungama adzalandire, n’kukhalamo kwamuyaya.’​—Salimo 37:29.

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Image Science and Analysis Laboratory, NASA-Johnson Space Center