Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

 Kodi Mukudziwa?

Kodi “ulusi wofiira kwambiri” umene watchulidwa kambirimbiri m’buku la Ekisodo n’chiyani?

Nkhani ina ya m’Baibulo imanena kuti nsalu zimene anakutira chihema, chomwe chinali malo olambirira mu Isiraeli kalelo, ndiponso zimene ankatchingira m’zipata zake, anaziwomba ndi “ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.” (Ekisodo 26:1; 38:18) Nazonso “zovala zopatulika” za ansembe zinkafunika kuti zikhale za nsalu yopangidwa ndi “ulusi wofiira kwambiri.”​—Ekisodo 28:1-6.

Utoto wofiira kwambiri unkachokera kutizilombo tinatake tatikazi topanda mapiko. Tizilombo timeneti timapezeka m’mitengo inayake ikuluikulu ya ku Middle East komanso m’mphepete mwa nyanja ya Mediterranean. Utoto wofiira kwambiriwo umapezeka m’mazira amene amakhala m’mimba mwa tizilomboti. Kachilomboka kakakhala ndi mazira kamakhala kofiira ngati mabulosi, kukula kwake kamakhala ngati nsawawa ndipo kamamatirira kutsamba kapena nthambi ya mtengo. Anthu akagwira tizilombo timeneti n’kutiphwanyaphwanya, tinkatulutsa utoto wofiira kwambiri umene umasungunuka m’madzi ndipo ankatha kunyikamo nsalu kuti zikhale zofiira. Wolemba mbiri wachiroma, Pliny Wamkulu, ananena kuti nsalu zonyikidwa mu utoto wofiira kwambiri zinali zina mwa nsalu zimene anthu ankazikonda kwambiri pa nthawiyo.

Pa anthu amene analemba nawo Malemba Achigiriki, ndi ati amene analipo pa Pentekosite mu 33 C.E.?

N’kutheka kuti omwe analipo ndi anthu 6, pa anthu 8 amene analemba nawo gawo limeneli la Malemba.

Malinga ndi nkhani yomwe ili m’buku la Machitidwe, Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Musatuluke mu Yerusalemu, koma muyembekezere chimene Atate analonjeza.” (Machitidwe 1:4) Nkhani yomweyi ikusonyezanso kuti Mateyu, Yohane ndi Petulo, omwe analemba nawo Baibulo, anamvera malangizo amenewa ndipo anasonkhana ndi ophunzira ena “pamalo amodzi.” Azibale ake a Yesu analinso pomwepo. (Machitidwe 1:12-14; 2:1-4) Ndipo awiri mwa azibale a Yesu amenewa, Yakobo ndi Yuda (Yudasi), analemba mabuku awiri a m’Baibulo amene amatchedwa ndi mayina awo.​—Mateyu 13:55; Yakobo 1:1; Yuda 1.

M’buku lake la Uthenga Wabwino, Maliko anafotokoza za mnyamata wina amene anathawa usiku, Yesu atagwidwa. Apa zikuoneka kuti Maliko ankadzinena yekha, chifukwa ophunzira ena onse anali atathawa kale n’kumusiya Yesu. (Maliko 14:50-52) Choncho, zikuoneka kuti Maliko anakhala wophunzira wa Yesu kale kwambiri, ndipo n’kutheka kuti analipo pa Pentekosite.

Anthu awiri otsalawo amene analemba nawo Malemba Achigiriki anali Paulo ndi Luka. Pa Pentekosite mu 33 C.E., Paulo anali asanakhale wotsatira wa Khristu. (Agalatiya 1:17, 18) Zikuoneka kuti nayenso Luka panalibe pa nthawiyi, chifukwa ananena yekha kuti iye sanali m’gulu la “anthu amene anakhala mboni zoona ndi maso” utumiki wa Yesu.​—Luka 1:1-3.

[Chithunzi patsamba 22]

Tizilombo Timene Tinkatulutsa Utoto Wofiira Kwambiri

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy of SDC Colour Experience (www.sdc.org.uk)

[Chithunzi patsamba 22]

Petulo Akulankhula pa Pentekosite mu 33 C.E.