Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ena Ali pa Umphawi Wadzaoneni

Anthu Ena Ali pa Umphawi Wadzaoneni

Anthu Ena Ali pa Umphawi Wadzaoneni

UMPHAWI ndi woopsa kwambiri chifukwa munthu akhoza kufa nawo. Anthu amene ali pa umphawi wadzaoneni, sakhala ndi chakudya chokwanira ndipo amasowa madzi abwino. Amavutika kupeza nkhuni, amasowa malo abwino okhala, amasowa chithandizo chakuchipatala komanso amasowa ndalama zolipirira sukulu. Padziko lonse pali anthu 1 biliyoni amene ali pa umphawi wadzaoneni ndipo chiwerengero chimenechi n’chofanana ndi cha anthu a m’mayiko onse mu Africa muno. Komabe anthu ambiri a m’madera monga kumadzulo kwa Ulaya ndi ku North America chibadwireni sanaonepo munthu amene ali pa umphawi wadzaoneni. Choncho tiyeni tikambirane zitsanzo za anthu ena omwe ali pa umphawi wadzaoneni.

Mbarushimana ndi mkazi wake komanso ana awo asanu amakhala ku Rwanda. Mwana wawo wa nambala 6 anamwalira ndi malungo. Mbarushimana ananena kuti: “Bambo athu anagawa munda wawo kwa ana tonse 6. Malo amene anandipatsa anali ochepa kwambiri moti ndinaganiza zosamukira m’tauni ina ndi banja langa. Kuti tipeze ndalama, ine ndi mkazi wanga timagwira ganyu yonyamula matumba a mchenga ndi miyala. Nyumba yomwe timakhala ilibe mawindo. Timamwa madzi omwe timakatunga pachitsime china ku polisi. Nthawi zambiri timangodya kamodzi patsiku, koma tikalephera kupeza ganyu timakhala tsiku lonse osadya. Zoterezi zikachitika ndimangochoka panyumba chifukwa ndimamva chisoni kumaona ana akungolira ndi njala.”

Victor ndi mkazi wake Carmen ali ndi ana asanu ndipo amakhala ku Bolivia, m’tawuni ina yomwe ili kwa yokhayokha. Iwo amagwira ntchito yosoka nsapato ndipo amachita lendi chipinda cha nyumba ina yazidina, yopanda magetsi, yogumukagumuka komanso yodontha. Pasukulu ya m’derali pali ana ambiri koma palibe madesiki okwanira moti Victor anachita kupanga desiki kuti mwana wake azikakhalira kusukuluko. Victor ndi Carmen amayenda ulendo wautali wokwana makilomita 10 kukatola nkhuni zoti aziphikira chakudya komanso kuwiritsira madzi akumwa. Carmen ananena kuti: “Tilibe chimbudzi, choncho timangopita kum’tsinje kumenenso timasamba komanso kutaya zinyalala. Zimenezi zimachititsa kuti ana athu azidwaladwala.”

Francisco ndi mkazi wake Ilídia amakhala m’dera linalake lakumidzi m’dziko la Mozambique. Iwo anali ndi ana asanu koma mmodzi anamwalira ndi malungo chifukwa madokotala sanamugoneke m’chipatala kuti alandire chithandizo chokwanira. Banjali limalima mpunga ndi mbatata pamunda wawo waung’ono, koma zimene amakolola zimangokwana kudya miyezi itatu basi. Fransisco anafotokoza kuti: “Nthawi zina mvula siimagwa bwino kapena akuba amatibera zinthu m’munda. Kuti ndipeze ndalama ndimakadula ndikugulitsa nsungwi zomangira nyumba komabe ndalama imene ndimapeza ndi yochepa kwambiri. Komanso ine ndi mkazi wanga timapita kokatola nkhuni kutali, ulendo wa maola awiri. Aliyense amabweretsa mtolo wake, ndiyeno winawo timaphikira ndipo umakwana kuphikira mlungu umodzi, pomwe winawo timagulitsa.”

Anthu ambiri akuona kuti padzikoli zinthu sizikuyenda bwino ngakhale pang’ono ndipo pakuchitika zinthu zopanda chilungamo. Zili choncho chifukwa munthu mmodzi pa anthu 7 aliwonse ali pa umphawi wadzaoneni ngati mmene zilili ndi Mbarushimana, Victor ndiponso Francisco. Koma ngakhale kuti anthu ena ali pa umphawi woterewu, anthu ambiri zinthu zikuwayendera bwino kwambiri moti umphawi saudziwa n’komwe. Anthu ena ayeserapo kuti athetse umphawi ndipo nkhani yotsatira ikunena zimene achita.

[Chithunzi pamasamba 2, 3]

Carmen ndi ana ake awiri akutunga madzi mumtsinje