Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ali ndi Gulu Lake Limene Akulitsogolera?

Kodi Mulungu Ali ndi Gulu Lake Limene Akulitsogolera?

 Kodi Mulungu Ali ndi Gulu Lake Limene Akulitsogolera?

CHILICHONSE chimene Mulungu analenga chimagwira ntchito yake mwadongosolo kwambiri. Koma mfundo yoti zinthu zonse zimene Mulungu anapanga zimagwira ntchito mwadongosolo imaonekanso mu zinthu zimene sitingathe kuziona. Mwachitsanzo, Baibulo limasonyeza kuti angelo nawonso amatumikira Mulungu mwadongosolo ndiponso mogwirizana ndi zimene Mlengi amafuna. Mneneri Danieli anaona m’masomphenya gulu lalikulu la angelo ali m’bwalo la milandu la Mulungu. Iye anati: “Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira nthawi zonse, ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake nthawi zonse.” (Danieli 7:9, 10) N’zosakayikitsa kuti payenera kukhala dongosolo labwino kuti angelo ochuluka kwambiri amenewa, oposa 100 miliyoni, azitha kuchita zimene Mulungu akufuna zokhudza anthu ake padziko lapansili.​—Salimo 91:11.

Ngakhale kuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu ndi Mulungu wa dongosolo kwambiri, iye sachita zinthu mopanda chifundo ndipo sapondereza zolengedwa zake. M’malomwake iye ndi wachikondi, ndi Mulungu wachimwemwe komanso amafunira zabwino zolengedwa zake zonse. (1 Timoteyo 1:11; 1 Petulo 5:7) Umboni wa zimenezi ndi mmene ankachitira zinthu ndi mtundu wakale wa Isiraeli komanso Akhristu a m’nthawi ya atumwi.

Yehova Ankatsogolera Mtundu wa Isiraeli Mwadongosolo

Yehova Mulungu anagwiritsa ntchito Mose kutsogolera Aisiraeli mwadongosolo pa kulambira koona. Taganizirani zimene zinachitika pamene iwo anamanga misasa m’chipululu cha Sinai. Zinthu sizikanalongosoka zikanakhala kuti banja lililonse linkangomanga hema wawo paliponse pamene likufuna. Koma Yehova anapatsa anthuwa malangizo omveka bwino onena za malo amene fuko lililonse liyenera kukhala. (Numeri 2:1-34) Chilamulo cha Mose chinalinso ndi mfundo zomveka bwino zokhudza ukhondo ndi umoyo wa anthu. Mwachitsanzo, panali malamulo onena zimene munthu ayenera kuchita akafuna kudzithandiza.​—Deuteronomo 23:12, 13.

Pamene Aisiraeli analowa m’Dziko Lolonjezedwa, ankachita zinthu mwadongosolo kwambiri. Mwachitsanzo, mtunduwu unagawidwa m’mafuko 12 ndipo fuko lililonse linapatsidwa malo akeake. Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisiraeli kudzera mwa Mose chinali ndi mfundo zokhudza mbali zonse za moyo wa munthu monga kulambira, ukwati, banja, maphunziro, bizinezi, zakudya, ulimi, kuweta ziweto ndi zinanso zambiri. * Ngakhale kuti malamulo ena amene Mulungu anapatsa Aisiraeli anali osapita m’mbali komanso ofotokoza zinthu mwatsatanetsatane, onse anali umboni woti Mulungu ankawakonda ndipo ankafuna kuti mtunduwo uzisangalala. Aisiraeli ankakondedwa mwapadera ndi Yehova chifukwa chotsatira dongosolo limeneli, limene Yehova anawapatsa chifukwa chowakonda.​—Salimo 147:19, 20.

N’zoona kuti mwachibadwa Mose anali mtsogoleri waluso, komabe kuti zinthu ziyende bwino sizinkadalira luso lakelo. Koma zinkadalira kuti iyeyo azitsatira dongosolo la Mulungu mokhulupirika. Mwachitsanzo, kodi Mose anadziwa bwanji njira yoyenera kudutsa pa nthawi imene iye ndi  Aisiraeli anzake anali m’chipululu? Yehova ndi amene ankawatsogolera usana pogwiritsa ntchito mtambo woima njo ngati chipilala komanso usiku pogwiritsa ntchito moto woima njo ngati chipilala. (Ekisodo 13:21, 22) Ngakhale kuti Yehova Mulungu ankagwiritsira ntchito anthu, kwenikweni iye ndi amene ankatsogolera anthu ake mwadongosolo. Anachitanso chimodzimodzi m’nthawi ya atumwi.

Yehova Ankatsogolera Akhristu Oyambirira Mwadongosolo

M’nthawi ya atumwi, mipingo yachikhristu inakhazikitsidwa m’madera ambiri ku Asia ndi ku Ulaya chifukwa chakuti atumwi komanso ophunzira a Yesu ankalalikira mwakhama. Ngakhale kuti mipingo imeneyi inali motalikirana, palibe mpingo umene unkachita zinthu zosiyana ndi mipingo ina. Panali dongosolo labwino limene mipingoyi inkayendera ndipo atumwi ndi amene ankaitsogolera mwachikondi. Mwachitsanzo, Tito anatumidwa ndi mtumwi Paulo kuti ‘akakonze zinthu’ ku Kerete. (Tito 1:5) Komanso Paulo ananena m’kalata imene analembera mpingo wa ku Korinto kuti abale ena anali ndi “luso loyendetsa zinthu.” (1 Akorinto 12:28) Koma kodi ndani anachititsa kuti zinthu zonsezi ziziyenda bwino? Paulo ananena kuti “Mulungu analumikiza” kapena kuti kukhazikitsa dongosolo mumpingo.​—1 Akorinto 12:24.

Anthu amene anali ndi udindo mu mpingo wachikhristu ntchito yawo sinali kulamulira Akhristu anzawo. M’malomwake anali ‘antchito anzawo’ amene ankatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu komanso anafunika kukhala “zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (2 Akorinto 1:24; 1 Petulo 5:2, 3) Yesu Khristu, ndiye “mutu wampingo” osati munthu aliyense kapena gulu la anthu opanda ungwiro.​—Aefeso 5:23.

Pa nthawi ina mpingo wa ku Korinto unayamba kuchita zinthu zosiyana kwambiri ndi zimene mipingo ina inkachita. Choncho Paulo anawalembera kuti: “Kodi mawu a Mulungu anachokera kwa inu, kapena anafika kwa inu nokha?” (1 Akorinto 14:36) Paulo anagwiritsa ntchito funso limeneli losafunika yankho, pofuna kuwathandiza kumvetsa kuti sankayenera kumachita zinthu zosiyana ndi mipingo ina yachikhristu. Chifukwa chotsatira malangizo a atumwi, mipingo inakula ndiponso inkayenda bwino.​—Machitidwe 16:4, 5.

Umboni Wosonyeza Kuti Mulungu Amakonda Atumiki Ake

Nanga bwanji masiku ano? Anthu ena angamaganize kuti sakufunikira kukhala m’chipembedzo chilichonse. Koma Baibulo limasonyeza kuti Mulungu wakhala akugwiritsa ntchito gulu lake kuti akwaniritse zofuna zake. Iye ankatsogolera mwadongosolo Aisiraeli akale komanso Akhristu oyambirira.

Ndiye kodi si zoona kuti masiku anonso Yehova Mulungu akutsogolera anthu ake ngati mmene ankachitira kale? N’zoonekeratu kuti Mulungu akutsogolera atumiki ake mwadongosolo komanso akuonetsetsa kuti ndi ogwirizana ndipo umenewu ndi umboni wakuti amawakonda. Masiku ano Yehova akugwiritsa ntchito gulu lake kukwaniritsa chifuno chake chokhudza anthu. Ndiyeno kodi gulu la Yehova tingalidziwe bwanji? Tiyeni tione mfundo zimene zingatithandize kulidziwa.

Akhristu oona akugwira mwadongosolo ntchito yolalikira. (Mateyu 24:14; 1 Timoteyo 2:3, 4) Yesu analamula otsatira ake kuti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu ku mitundu yonse. Ntchito imeneyi siingatheke patakhala kuti palibe gulu la padziko lonse lochita zinthu mwadongosolo. Mwachitsanzo, inuyo mungathe kudyetsa munthu mmodzi koma mutakhala kuti mukufunika kudyetsa anthu mamiliyoni ambiri, mungafunike kugwira ntchito mogwirizana ndi gulu la anthu lotsogoleredwa bwino komanso logwira ntchito mwadongosolo. N’chimodzimodzinso Akhristu oona. Kuti akwaniritse ntchito yawo yolalikira padziko lonse, afunika ‘kutumikira Mulungu mogwirizana’ (Zefaniya 3:9) Ntchito imeneyi, ikuchitika m’mayiko osiyanasiyana, kwa anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana komanso ochokera m’mitundu yosiyanasiyana. Ndiye kodi ntchito imeneyi ingatheke popanda gulu logwirizana? N’zachidziwikire kuti izi sizingatheke.

Akhristu oona amathandizana komanso kulimbikitsana. Katswiri wokwera mapiri, akamakwera phiri yekha angakhale ndi ufulu wosankha kupita kulikonse kumene akufuna ndipo sangavutike ndi kusamalira anthu ena amene sanazolowere kukwera mapiri. Komabe munthu ameneyu  atachita ngozi kapena atakumana ndi vuto lililonse, angavutike kwambiri chifukwa angasowe womuthandiza. N’kupanda nzeru kudzipatula n’kumachita zinthu pawekha. (Miyambo 18:1) Kuti Akhristu akwanitse kugwira ntchito imene Yesu anawapatsa, ayenera kumathandizana. (Mateyu 28:19, 20) Mpingo wachikhristu umapereka malangizo a m’Baibulo, kuphunzitsa komanso kulimbikitsa anthu ndipo izi n’zofunika kwambiri kuti Akhristu apitirizebe kutumikira Yehova. Kodi pakanakhala kuti palibe mpingo wachikhristu, anthu akanamapita kuti kukaphunzitsidwa njira za Yehova?​—Aheberi 10:24, 25.

Akhristu oona amatumikira Mulungu mogwirizana. Nkhosa za Yesu zimamva mawu ake ndipo zimakhala “gulu limodzi” komanso zimatsogoleredwa ndi iyeyo. (Yohane 10:16) Nkhosa zimenezi sizimapezeka m’matchalitchi kapena m’magulu ogawanika azipembedzo komanso sizogawikana pa nkhani ya ziphunzitso. Koma nkhosa zonsezi ‘zimalankhula mogwirizana.’ (1 Akorinto 1:10) Kuti anthu azikhala mogwirizana pamafunika dongosolo ndipo kuti pakhale dongosolo pamafunika mgwirizano. Mulungu amadalitsa anthu okhawo amene amakondana komanso kugwirizana.​—Salimo 133:1, 3.

Kukonda Mulungu ndiponso choonadi cha m’Baibulo kwachititsa anthu mamiliyoni ambiri kukhala m’gulu limene limatsatira mfundo zimenezi komanso zina zopezeka m’Baibulo. A Mboni za Yehova padziko lonse ndi gulu logwirizana ndipo akuyesetsa kuchita chifuno cha Mulungu. Iwo amakhulupirira kuti lonjezo ili ndi loona: “Ndidzakhala pakati pawo ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.” (2 Akorinto 6:16) Inunso mungapeze madalitso amenewa ngati mutalowa m’gulu la Yehova Mulungu n’kuyamba kumulambira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani buku la, Insight on the Scriptures, Volume 2, tsamba 214 mpaka 220, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 13]

Aisiraeli anamanga mahema awo mwadongosolo kwambiri

[Zithunzi pamasamba 14, 15]

Kuti ntchito yolalikira ichitike padziko lonse pafunika kuchita zinthu mwadongosolo

Kulalikira khomo ndi khomo

Kuthandiza pakagwa tsoka

Misonkhano

Kumanga malo olambirira