Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi pa atumwi 12, panali wina amene anali m’bale wake wa Yesu?

Malemba sapereka yankho lachindunji pa funso limeneli. Komabe zochitika zina komanso nkhani zina zimasonyeza kuti ena mwa atumwi 12 a Yesu anali achibale ake.

Anthu amene analemba Uthenga Wabwino amatchula mayina a azimayi amene ankayang’anitsitsa pamene Yesu ankafa pa mtengo wozunzikira. Lemba la Yohane 19:25 limatchula anayi mwa azimayi amenewa: “Mayi ake [Mariya] ndi m’bale wawo wa mayi akewo; Mariya mkazi wa Kulopa, ndi Mariya Mmagadala.” Tikayerekezera lemba limeneli ndi zimene Mateyo ndi Maliko ananena pa nkhani yomweyi, tinganene kuti mchemwali wawo wa amayi ake a Yesu anali Salome. Zikuoneka kuti Salome ameneyu ndi amene anali mayi wa ana a Zebedayo. (Mateyo 27:55, 56; Maliko 15:40) Mavesi ena amasonyeza kuti ana amenewa anali Yakobe ndi Yohane, ndipo anali asuweni ake a Yesu. Anyamata a pachibale amenewa, anali asodzi ndipo Yesu anawasankha kuti akhale ophunzira ake.​—Mateyo 4:21, 22.

Mabuku ena amanena kuti Kulopa kapena kuti Alifeyo, yemwe anali mwamuna wa mmodzi wa azimayi otchulidwa pa Yohane 19:25, anali m’bale wake wa Yosefe, omwe anali bambo ake a Yesu. Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti Yakobe, mwana wa Alifeyo, yemwe anali mmodzi wa atumwi 12, anali msuweni wake wa Yesu.​—Mateyo 10:3.

Kodi panali chibale chotani pakati pa Yesu ndi Yohane M’batizi?

Anthu ena amakhulupirira kuti chibale chimene chinali pakati pa Yesu ndi Yohane M’batizi chinali chakuti mayi ake a Yesu ndi mayi ake a Yohane anali pa chisuweni. Anthuwa amakhulupirira zimenezi chifukwa cha mmene mabaibulo ena anamasulilira lemba la Luka 1:36. Mwachitsanzo, palemba limeneli Baibulo la King James Version limanena kuti Elizabeti, yemwe anali mayi ake a Yohane, anali msuweni wa Mariya, mayi ake a Yesu.

Koma zoona n’zakuti, mawu achigiriki choyambirira amene anawagwiritsa ntchito pavesili, sasonyeza bwinobwino kuti chibale chake chinali chotani. Mawuwo amangosonyeza kuti azimayi awiriwa anali pa chibale, koma sasonyeza kuti anali pa chisuweni. Malinga ndi zimene dikishonale ina yomasulira mawu a m’Baibulo imanena, “mawuwa ali ndi matanthauzo ambiri moti n’zovuta kudziwa bwinobwino kuti chibale chake chinali chotani.” (The Interpreter’s Dictionary of the Bible) Ndiye kodi mfundo yoti chibale chimene chinali pakati pa Yesu ndi Yohane M’batizi chinali chakuti mayi ake a Yesu ndi a Yohane anali pa chisuweni inachokera kuti? Buku lina limayankha kuti: “Zonse zimene timadziwa zokhudza . . . makolo ake a Mariya . . . zinachokera m’mabuku owonjezera pa mabuku enieni a m’Baibulo.”​—The Catholic Encyclopedia.

Choncho, Yesu ndi Yohane anali apachibale chapatali, koma si kuti mayi ake a Yesu ndi a Yohane anali pa chisuweni.